UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mmene Tingayambitsile Makambilano Pogwilitsila Nchito Mathirakiti
Kucokela mu January 2018, pa cikuto ca kabuku ka misonkhano ya Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu pamakhala makambilano acitsanzo. Ndipo takhala tikulimbikitsidwa kusumika maganizo athu pa kukambilana na anthu m’malo mongowagaŵila cabe zofalitsa zathu. Pofuna kuthandiza ofalitsa kusintha moyambitsila makambilano, mavidiyo a makambilano acitsanzo amaonetsa mmene tingayambitsile makambilano mwa kuseŵenzetsa Baibo cabe. Koma kodi izi zitanthauza kuti tinaleka kuseŵenzetsa zofalitsa polalikila ku nyumba na nyumba? Kutalitali! Mwacitsanzo, kuseŵenzetsa mathirakiti ingakhale njila yabwino yoyambitsila makambilano. Tingaseŵenzetse njila yotsatilayi pogaŵila kathirakiti kalikonse:
Funsani mwininyumba funso la pa cikuto lokhala na mayankho ocita kusankhapo.
Muonetseni yankho la m’Baibo limene lili pa lemba kapena malemba amene ali pamwamba pa peji yaciŵili. Ngati nthawi ilola, ŵelengani na kukambilana mfundo za mkati mwa kathirakiti.
Mugaŵileni kathirakiti mwininyumba, na kumulimbikitsa kuti akaŵelenge konse pa nthawi imene angakonde.
Musanacoke, muonetseni funso la pa mbali yakuti “Ganizilani Funso Ili” na kukonza zakuti mukakambilane yankho ya m’Baibo ulendo wotsatila.
Pa ulendo wobwelelako, kambilanani yankho ya funsolo, na kusiya funso lina kuti mukakambilane ulendo wotsatila. Mungasankhe funso pa webusaiti yathu kapena m’cofalitsa cimene cikuonetsedwa pa peji yothela. Pa nthawi yoyenelela, mugaŵileni bulosha yakuti Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu! kapena cofalitsa cina cophunzitsila ca mu Thuboksi Yathu.