January 20-26
GENESIS 6-8
Nyimbo 89 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anacitadi Momwemo”: (10 min.)
Gen. 6:9, 13—Munthu wolungama Nowa anali kukhala pakati pa anthu oipa (w18.02 4 ¶4)
Gen. 6:14-16—Nowa anapatsidwa nchito yovuta (w13 4/1 14 ¶1)
Gen. 6:22—Nowa anali na cikhulupililo mwa Yehova (w11 9/15 18 ¶13)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 7:2—Kodi cosiyanitsila pakati pa nyama zodetsedwa na zosadetsedwa maka-maka cinali ciani? (w04 1/1 29 ¶7)
Gen. 7:11—Kodi madzi amene anacititsa Cigumula pa dziko lonse ayenela kuti anacokela kuti? (w04 1/1 30 ¶1)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni cuma ca kuuzimu citi cimene mwapeza ponena za Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mfundo ina?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 6:1-16 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Woyamba: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela mafunso otsatilawa: Kodi wofalitsa wathandiza bwanji mwininyumba kumvetsetsa mfundo ya pa 1 Yohane 4:8? Kodi ofalitsa athandizana bwanji polalikila?
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 12)
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani cofalitsa ca mu Thuboksi Yathu. (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kulambila Kwa Pabanja: Nowa—Anayenda na Mulungu: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi (pitani ku mavidiyo pa BANJA). Ndiyeno kambilanani mafunso aya: Kodi makolo m’vidiyoyi anaseŵenzetsa bwanji nkhani ya Nowa pophunzitsa ana awo mfundo zofunika? Ni zinthu ziti zothandiza zimene muona kuti mungaziseŵenzetse pocita kulambila kwanu kwa pabanja?
Zofunikila za Mpingo: (5 min.)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 100
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 37 na Pemphelo