CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 6-8
“Anacitadi Momwemo”
6:9, 13-16, 22
Ganizilani kukula kwa nchito imene Nowa na banja lake anafunika kugwila pomanga cingalawa. Iwo analibe zipangizo zamakono kapena njila zatsopano zomangila.
Cingalawa cinali cacikulu—m’litali cinali mamita pafupi-fupi 133, m’lifupi mamita 22, msinkhu mamita 13
Anafunika kugwetsa mitengo, kuidula m’masaizi oyenela, ndiponso kuinyamula na kukaiika pa malo ake
Anafunika kumata phula cingalawa conse mkati na kunja komwe
Nowa na banja lake anafunika kusonkhanitsa cakudya cimene adzadya kwa caka, cawo komanso ca nyama
Nchitoyo iyenela kuti inatenga zaka 40 mpaka 50 kuti ithe
Kodi nkhaniyi ingatithandize bwanji ngati tiona kuti n’zovuta kucita zimene Yehova watipempha?