LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsa. 3
  • Makolo, Phunzitsani Ana Anu Zimene Afunika Kudziŵa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Makolo, Phunzitsani Ana Anu Zimene Afunika Kudziŵa
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Phunzitsani Ana Anu Kutumikila Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 January tsa. 3
Ana aimika manja kwinaku akukamba kuti, ‘Iyayi!’ poyeseza zimene makolo awo akuwaphunzitsa zokhudza mmene angadzitetezele.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Makolo, Phunzitsani Ana Anu Zimene Afunika Kudziŵa

Tikhala m’dziko limene limafuna kuti tiziona monga cabwino ni coipa ndipo coipa ni cabwino. (Yes. 5:20) N’zacisoni kuti anthu ena m’dzikoli, amacita zinthu zimene Yehova amadana nazo kuphatikizapo kucita zinthu zosayenela pakati pa amuna okha-okha kapena akazi okha-okha. Ana athu ni amtengo wapatali. Koma anzawo kusukulu ndi anthu ena angayese kuwanyengelela kuti azitsatila zocita zawo. Kodi mungawakonzekeletse bwanji ana anu ku mayeselo amenewa na ena otelo?

Konzekeletsani ana anu mwa kuwaphunzitsa mfundo za Yehova. (Lev. 18:3) Malinga na msinkhu wawo, pang’ono-m’pang’ono aphunzitseni zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kugonana. (Deut. 6:7) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ana anga n’nawaphunzitsa za kuonetsana cikondi m’njila yoyenela, kufunika kovala mwaulemu, komanso kufunika kwakuti ena azipewa kuwagwila kumalo obisika kapena kuwaonela? Kodi ana anga adziŵa zoyenela kucita ngati wina afuna kuwaonetsa zithunzi zamalisece, kapena ngati wawapempha kuti acite zinthu zimene Yehova amati n’zoipa?’ Kudziŵilatu zocita kungawathandize kupewa kugwela m’mavuto. (Miy. 27:12; Mlal. 7:12) Ngati muphunzitsa ana anu, mumaonetsa kuti mumakonda coloŵa canu camtengo wapatali cocokela kwa Yehova.—Sal. 127:3.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI MANGANI NYUMBA IMENE IDZAKHALITSA—TETEZANI ANA ANU KU “ZINTHU ZOIPA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Mangani Nyumba Imene Idzakhalitsa—Tetezani Ana Anu Ku ‘Zinthu Zoipa.’ Mayi na mwana wake akuonelela vidiyo yakuti ‘Tetezani Ana Anu.’

    N’cifukwa ciani makolo ena amaopa kuunikila ana awo pankhani zakugonana?

  • Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Mangani Nyumba Imene Idzakhalitsa—Tetezani Ana Anu Ku ‘Zinthu Zoipa.’ Makolo akukambilana ndi ana awo aŵili buku lakuti, ‘Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso’ na zofalitsa zina.

    N’cifukwa ciani makolo ayenela kulela ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake”?—Aef. 6:4

  • Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Mangani Nyumba Imene Idzakhalitsa—Tetezani Ana Anu Ku ‘Zinthu Zoipa.’ Makolo mu Africa akuŵelenga na kukambilana malemba ndi ana awo.

    Kudziŵa zinthu kumateteza

    Kodi gulu la Yehova lapeleka zida zotani zothandiza makolo kuunikila ana awo pankhani zakugonana?—w19.05 12, bokosi

  • N’cifukwa ciani mufunika kumakambilana kaŵili-kaŵili na ana anu pasanabuke mavuto aakulu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani