LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 January tsa. 7
  • Khalani Otsimikiza za Cikondi Cosasintha ca Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalani Otsimikiza za Cikondi Cosasintha ca Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Thandizo pa Matsoka a mu 2021—Abale na Alongo Athu Sananyalanyazidwe
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Kupeleka Thandizo kwa Anthu Okhudzidwa na Matsoka
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Tengelani Cikondi Cosasintha ca Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 January tsa. 7
Abale na alongo aimilila panja pa Nyumba ya Ufumu atalandila thandizo la cakudya.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Khalani Otsimikiza za Cikondi Cosasintha ca Yehova

Yehova amakuonani kuti ndinu amtengo wapatali. (Yes. 43:4) Yehova anakukokelani kwa iye komanso ku gulu lake. Ndipo pamene munadzipatulila na kubatizika, munakhala ake a Yehova. Iye adzakusamalilani monga cuma cake capadela ngakhale panthawi zovuta. Adzakuonetsani cikondi cake cosasintha kupitila m’gulu lake.—Sal. 25:10.

Kuona mmene gulu la Yehova lathandizila anthu ake pa matsoka a zacilengedwe m’zaka zaposacedwapa, kungatilimbikitse kuyamikila kwambili cikondi cake cosasintha.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI YA 2019 YA KOMITI YA OGWILIZANITSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Lipoti ya 2019 ya Komiti ya Ogwilizanitsa.” Abale a m’Komiti Yothandizila Pakagwa Tsoka akukamba na abale na alongo okhudzidwa na tsoka la zacilengedwe.

    Kodi Komiti ya Ogwilizanitsa inakonzekeletsa bwanji maofesi a nthambi padziko lonse kuti azicitapo kanthu mwamsanga pakacitika matsoka?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Lipoti ya 2019 ya Komiti ya Ogwilizanitsa.” Abale akumanganso nyumba imene inawonongeka na tsoka la zacilengedwe ku Indonesia.

    Kodi gulu la Yehova linapeleka bwanji thandizo pa nthawi ya tsoka ku Indonesia na ku Nigeria?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Lipoti ya 2019 ya Komiti ya Ogwilizanitsa.” Nesi mu Africa akupima wodwala poseŵenzetsa cipangizo copimila kugunda kwa mtima na kupuma.

    N’ciani cakufikani pamtima mukaganizila mmene gulu lacitila zinthu pa nthawi ya mlili wa COVID-19?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani