LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 1 masa. 14-15
  • Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Pemphelo—Kodi Lingakuthandizeni Bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 1 masa. 14-15

Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?

Pamela atayamba kudwala matenda aakulu, anapita kucipatala. Komanso anapemphela kwa Mulungu kuti amuthandize kupilila. Kodi kupemphela kunamuthandiza?

Pamela anati: “Pamene n’nali kulandila thandizo pa matenda anga a khansa, nthawi zambili n’nali kukhala na mantha kwambili. Koma nikapemphela kwa Yehova Mulungu, mtima unali kukhala m’malo. Sin’nali kukhalanso na mantha kwambili. Nimamvelabe kuŵaŵa nthawi zonse. Koma pemphelo limanithandiza kucepetsa nkhawa. Anthu akanifunsa kuti, ‘Mumvelako bwanji?’ Nimawayankha kuti, ‘Sinimvela bwino, koma ndine wacimwemwe!’”

Koma sikuti timafunika kucita kuyembekezela kukumana na mavuto aakulu kuti tipemphele. Tonsefe timakumana na mavuto, aakulu komanso aang’ono, ndipo nthawi zambili timadziŵa kuti tifunika thandizo kuti tipilile mavutowo. Kodi pemphelo lingatithandize?

Baibo imati: “Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakucilikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” (Salimo 55:22) Kodi si zolimbikitsa zimenezi? Inde, n’zolimbikitsadi! Ndiye kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji? Ngati mwapemphela kwa Mulungu m’njila yoyenela, iye adzakupatsani zimene mufunikila kuti mukwanitse kupilila mavuto anu.—Onani bokosi yakuti ““Zimene Mudzalandila Ngati Mupemphela.”

Zimene Mudzalandila Ngati Mupemphela

Mtendele wa Maganizo

Munthu wamalonda amene nchito inamuthela poyamba, akumwetulila komanso akuyenda mwacidalilo.

“Zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Ngati mukhuthulila Mulungu nkhawa zanu, adzakuthandizani kuti musakhale na nkhawa komanso kuti mucite zinthu mwanzelu pa nthawi zovuta.

Nzelu Zocokela kwa Mulungu

Mayi amene poyamba anali kupemphela mocita kuŵelenga mapemphelo m’buku la mapemphelo, akuŵelenga Baibo yake ku nyumba.

“Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.” (Yakobo 1:5) Tikapanikizika na mavuto, nthawi zina sitipanga zosankha mwanzelu. Ngati tipempha nzelu kwa Mulungu, iye angatikumbutse mfundo zambili zothandiza za m’Mawu ake, Baibo.

Mphamvu na Citonthozo

Mwamuna na mkazi wake amene anali m’cipatala akuyenda capamodzi m’paki. Mwamunayo mwacikondi akuthandiza mkazi wake kuyenda na ndodo.

“Pa zinthu zonse ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Yehova ni Mulungu wamphamvuzonse. Conco angakupatseni mphamvu zofunikila kuti muthane na mavuto anu, kapena kuti mupilile mayeselo. (Yesaya 40:29) Baibo imakambanso kuti Yehova ni “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.” Angatitonthoze “m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

KODI MUFUNA KUTI MAPEMPHELO AZIKUTHANDIZANI?

Yehova sakukakamizani kuti muzipemphela kwa iye. Koma amakupemphani mwacikondi kuti muzipemphela. (Yeremiya 29:11, 12) Koma bwanji ngati m’mbuyomu munali kuona kuti Mulungu sayankha mapemphelo anu? Musataye mtima kapena kuleka kupemphela. Mwacitsanzo, nthawi zina makolo acikondi sathandiza ana awo ndendende mmene anawo akufunila kapena panthawi imene akufuna. Angacite izi mwina cifukwa ali na njila yabwino yothetsela vuto la anawo. Koma mulimonse mmene zingakhalile, makolo acikondi salephela kuthandiza ana awo.

Nayenso Yehova Mulungu, amene ni kholo labwino koposa, amafuna kukuthandizani. Ngati muŵelenga mosamala malangizo amene takamba m’magazini ino na kuyesetsa kuwaseŵenzetsa, Mulungu adzayankha mapemphelo anu m’njila yabwino koposa! —Salimo 34:15; Mateyu 7:7-11.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani