LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 3 masa. 6-8
  • Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CISANKHO CA ANTHU AMBILI
  • KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?
  • Aliyense Amafuna Kukhala na Tsogolo Labwino
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Mmene Mungakhalile na Tsogolo Labwino
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila
    Galamuka!—2021
  • Kodi Kukhala Munthu Wabwino Kungakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 3 masa. 6-8
Atsikana aŵili a ku yunivesite akukaloŵa m’kalasi.

Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Ambili amaganiza kuti anthu ophunzila kwambili komanso olemela ali na tsogolo labwino. Iwo amakhulupilila kuti maphunzilo a ku yunivesite angathandize munthu kukhala wanchito wabwino, wothandiza kwambili m’banja, ndiponso nzika yabwino. Iwo angaganizenso kuti maphunzilo apamwamba amathandiza munthu kupeza nchito ya malipilo abwino, komanso kuti anthu amene ali na ndalama zambili amakhala acimwemwe.

CISANKHO CA ANTHU AMBILI

Ganizilani zimene Zhang Chen wa ku China anakamba. Iye anati: “N’nali kukhulupilila kuti niyenela kutenga digili ku yunivesite kuti umphawi wanga uthe. N’nali kukhulupililanso kuti nchito ya malipilo abwino idzanithandiza kukhala na umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa.”

Pofuna kudzikonzela tsogolo labwino, ambili amacita zonse zotheka kuti akaphunzile ku mayunivesite ochuka, ngakhale a ku maiko ena. Zimenezi zinali kucitika kwambili mpaka pamene mlili wa COVID-19 unapangitsa kuti zikhale zovuta anthu kupita ku maiko ena. Lipoti la 2012 la bungwe lina loona pa zacuma na umoyo wa anthu linati: “52% pelesenti ya anthu amene anali kucita maphunzilo ku maiko ena anali ocokela ku Asia.”

Nthawi zambili makolo amagwila nchito molimbika kuti ana awo akacite maphunzilo a ku yunivesite ku maiko ena. Qixiang, wa ku Taiwan anati: “Makolo athu sanali olemela. Koma ana tonse anayi anatipeleka ku koleji ya ku America.” Kuti apeze ndalama zolipilila maphunzilo amenewo, banja lake linacita kutenga nkhongole yaikulu. Izi n’zimenenso mabanja ena ambili amacita.

KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?

Mmodzi wa atsikana aja ali pampando usiku patsogolo pa kompyuta, ndipo aoneka wolema komanso wopsinjika maganizo.

Ambili amene amayesetsa kuzama nawo maphunzilo ndiponso kufunafuna cuma amagwilitsidwa mwala

N’zoona kuti maphunzilo angathandize munthu kukhalako na umoyo wabwino. Koma si nthawi zonse pamene amathandiza ophunzila kupeza zimene anali kuyembekezela. Mwacitsanzo, ambili amagwila nchito molimbika kwa zaka zambili na kukongola ndalama zoculuka kuti alipilile maphunzilo apamwamba. Koma akatsiliza maphunzilowo sapeza nchito imene anali kufuna. Mu lipoti yake ya m’nyuzipepala ya ku Singapore yochedwa Business Times, Rachel Mui anati: “Vuto la kusoŵa nchito kwa anthu amene anacita maphunzilo a ku yunivesite likukulilakulila.” Munthu wina wophunzila kwambili wa ku Taiwan dzina lake Jianjie, anati, “Ambili amasoŵa cocita moti amangolola kugwila nchito yosagwilizana na maphunzilo a ku yunivesite amene anacita.”

Ngakhale anthu amene amapeza nchito yogwilizana na maphunzilo amene anacita, angaonebe kuti umoyo wawo sunakhale mmene anali kuyembekezela. Niran, wa ku Thailand anapita ku United Kingdom kukacita maphunzilo a ku yunivesite. Atabwelela kwawo, anapeza nchito yogwilizana na maphunzilo amene anacita. Iye anati: “Monga mmene n’nali kuyembekezela, digili imene n’natenga inanithandiza kupeza nchito ya ndalama zambili. Koma kuti nilandile malipilo amenewo, n’nafunika kugwila nchito molimbika komanso kwa maola ambili. M’kupita kwa nthawi, kampani imene n’nali kugwilako nchito inacotsa anchito ambili kuphatikizapo ine. N’nazindikila kuti kulibe nchito imene ingathandize munthu kukhala na tsogolo labwino.”

Ngakhale anthu olemela amene amaoneka kuti ali na umoyo wabwino, amakumanabe na mavuto a m’banja, amadwala, komanso amakhalabe na nkhawa pa nkhani ya zacuma. Katsutoshi wa ku Japan anakamba kuti, “N’nali na ndalama zambili, koma n’nalibe cimwemwe cifukwa anthu anali kunicitila nsanje, ndipo sanali kucita nane zinthu mwacikondi.” Mayi wina wa ku Vietnam dzina lake Lam anati: “Nimaona anthu ambili akufunafuna nchito ya malipilo apamwamba kuti apeze ndalama zambili. Koma zotulukapo zake n’zakuti amakhala na nkhawa kwambili, komanso amapsinjika maganizo ngakhale kudwala kumene.”

CIFUKWA CAKE MAPHUNZILO NA NDALAMA SIZOKWANILA

N’zoona kuti anthu amafunika maphunzilo na ndalama kuti azikwanitsa kudzisamalila na kusamalilanso mabanja awo. Koma zinthu zimenezi sizokwanila kuti munthu akhale na tsogolo labwino. Cifukwa ciani? Onani zimene Buku Lopatulika limakamba.

MAPHUNZILO APAMWAMBA NTHAWI ZINA SATHANDIZA.

“Othamanga kwambili sapambana pampikisano, . . . omvetsa zinthu nawonso sapeza cuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, cifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.”—MLALIKI 9:11.

Ngakhale anthu ophunzila kwambili, nthawi zina zinthu sizingawayendele bwino pa umoyo cifukwa pali zambili zimene sangathe kuzilamulila. Mwacitsanzo, kusakhazikika kwa zacuma, mavuto a zandale, ndiponso tsankho, zingalepheletse ngakhale munthu wophunzila kwambili kucita zimene akufuna.

CUMA SICIKHALITSA.

“Usamadzitopetse ndi nchito kuti upeze cuma. Leka kudzidalila kuti ndiwe womvetsa zinthu. Kodi maso ako amayang’anitsitsa cuma, pomwe ico sicicedwa kucoka? Cifukwa ndithu cimadzipangila mapiko ngati a ciwombankhanga n’kuulukila kumwamba.”—MIYAMBO 23:4, 5.

Citetezo cimene munthu angakhale naco cifukwa ca ndalama cimakhala cakanthawi. Kusokonezeka kwa zacuma m’dziko kungapangitse munthu kutaya ndalama zake zonse m’kanthawi kocepa. Matsoka a zacilengedwe monga zivomezi, moto wolilima, na mphepo zamkuntho zingasiye munthu alibiletu ndalama komanso malo okhala.

NTHAWI ZAMBILI NDALAMA ZIMABWELETSA MAVUTO

“Zambili zimene munthu wolemela amakhala nazo zimamulepheletsa kugona.”—MLALIKI 5:12.

Izi n’zimene zinacitikila Franklin amene amakhala ku Hong Kong. Iye ni wophunzila kwambili ndipo anali pa nchito ya malipilo apamwamba. M’kupita kwa nthawi, Franklin anakwezedwa n’kukhala bwana. Iye anati: “ N’nali kupanikizika kwambili pa nchito, ndipo zimenezi zinayamba kukhudza thanzi langa. N’nali kukhala na nkhawa kwambili moti n’nali kulephela kugona.” Zinthu zinafika poipa kwambili cakuti anangoleka nchitoyo. Franklin anati: “N’nali kudzifunsa cifukwa cake izi zinali kunicitikila, ndipo zinanipangitsa kuganizila mozama za colinga ca moyo.”

“Usamadzitopetse ndi nchito kuti upeze cuma.”—MIYAMBO 23:4

Mofanana na Franklin, anthu ambili azindikila kuti pali zinthu zambili zofunika ngako pa umoyo kuposa kucita maphunzilo apamwamba kapena kukhala na cuma. M’malo moika maganizo onse pa kufuna-funa cuma, ena mwa anthu amenewa amayesa kudzikonzela tsogolo labwino mwa kuyesetsa kukhala anthu abwino na kucitila ena zabwino. Koma kodi kucita zimenezi kungathandize munthu kukhala na tsogolo labwino? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani