LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 3 masa. 9-11
  • Kodi Kukhala Munthu Wabwino Kungakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Kukhala Munthu Wabwino Kungakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE AMBILI AMASANKHA KUCITA
  • KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?
  • Aliyense Amafuna Kukhala na Tsogolo Labwino
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Mmene Mungakhalile na Tsogolo Labwino
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • “Anthu Ofatsa Adzalandila Dziko Lapansi”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 3 masa. 9-11
Mayi wacitsikana akupatsa mayi wacikulile mpando wake kuti akhalepo m’basi.

Kodi Kukhala Munthu Wabwino Kungakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Kwa zaka mazana ambili, anthu akhala akukhulupilila kuti kukhala munthu wabwino n’kumene kungawathandize kukhala na tsogolo labwino. Mwacitsanzo, anthu ambili ku Asia amakhulupilila zimene anakamba mphunzitsi wochuka dzina lake Confucius (amene anakhalako pakati pa 551 na 479 B.C.E.) Iye anati: “Zimene simufuna kuti ena akucitileni, inunso musawacitile zimenezo.”a

ZIMENE AMBILI AMASANKHA KUCITA

Ambili amakhulupilila kuti kukhala na khalidwe labwino n’kumene kungawathandize kukhala na tsogolo labwino. Iwo amayesetsa kukhala aulemu, okoma mtima, kuzindikila udindo wawo, komanso kukhala na cikumbumtima cabwino. Mayi wina wa ku Vietnam, dzina lake Linh anati: “Nthawi zonse n’nali kukhulupilila kuti ngati nicita zinthu moona mtima, ndiye kuti nidzadalitsidwa.”

Mayi mmodzimodziyo akugaŵila cakudya anthu osauka komanso osoŵa kokhala.

Anthu ena amayesetsa kucita zabwino cifukwa ca zimene amaphunzila ku cipembedzo cawo. Munthu wina dzina lake Hsu-Yun, amene amakhala ku Taiwan, anati: “N’naphunzitsidwa kuti ngati munthu acita zabwino, ndiye kuti adzakhala na umoyo wacimwemwe akadzamwalila. Koma ngati acita zoipa adzavutika.”

KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?

Kumapeto kwa tsiku, mayi uja aoneka wosasangalala komanso wolema atafukata mwana wake wamwamuna.

N’zoona kuti tikamacitila ena zabwino, timapindula m’njila zambili. Komabe, anthu ambili amene amayesetsa kucitila ena zabwino, amaona kuti nthawi zina anthu ena sawacitila zabwino. Mayi wina wa ku Hong Kong, dzina lake Shiu Ping anati: “N’nadzionela nekha kuti anthu amene amacitila ena zabwino, nthawi zina sacitilidwa zabwino. N’nali kuyesetsa kusamalila banja langa na kucita zabwino. Koma ukwati wathu unavuta, ndipo mwamuna wanga anatithaŵa, ine na mwana wanga.”

Ambili amaona kuti anthu ena opembedza sakhala abwino. Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Etsuko anati: “N’naloŵa cipembedzo cinacake, ndipo n’nakhala mtsogoleli wa kagulu ka acinyamata. N’nadabwa kuona kuti ena m’cipembedzo cathu anali na khalidwe la ciwelewele, anali kulimbilana maudindo, komanso anali osakhulupilika poseŵenzetsa ndalama za chalichi.”

“N’nali kuyesetsa kusamalila banja langa na kucita zabwino. Koma ukwati wathu unavuta, ndipo mwamuna wanga anatithaŵa, ine na mwana wanga.”—SHIU PING, HONG KONG

Anthu ena odzipeleka kwambili pa zacipembedzo komanso amene amayesetsa kucita zabwino, amakhumudwa akaona zinthu zoipa zimene zimawacitikila. Umu ni mmene mayi wina wa ku Vietnam dzina lake Van anamvelela. Iye anati: “Tsiku lililonse n’nali kugula zipatso, maluwa, na zakudya n’kukazipeleka pa guwa la nsembe la makolo anga akale amene anamwalila. N’nali kucita izi poganiza kuti kutsogolo nidzalandila madalitso. Ngakhale kuti kwa zaka zambili n’nali kucita zabwino na kutsatila miyambo ya cipembedzo cathu, mwamuna wanga anadwala matenda oopsa. Kenako mwana wanga anamwalila ali mtsikana, pamene anali kucita maphunzilo ku dziko lina.”

CIFUKWA CAKE KUKHALA CABE MUNTHU WABWINO SI KOKWANILA

Kukhala munthu wabwino n’kofunika, koma si kokwanila kuti munthu akhale na tsogolo labwino. Cifukwa ciani? Onani zimene Buku Lopatulika limakamba.

SI ALIYENSE AMENE AMASANKHA KUCITA ZABWINO

“Wocimwa mmodzi yekha akhoza kuwononga zabwino zoculuka.”—MLALIKI 9:18.

Ngakhale mutayesetsa bwanji kukhala munthu wabwino umoyo wanu ungakhale pa ciopsezo cifukwa ca zocita za anthu ena odzikonda. Mwacitsanzo, pa nthawi ya mlili mungamatsatile malangizo amene aboma amapeleka na kupewa kukhala moyandikana na ena. Koma bwanji ngati ena amakana kutsatila malangizowo? Zocita zawo zingapangitse kuti ngakhale anthu amene amayesetsa kutsatila malangizo adwale.

ANTHU ANGAONE KUTI ZINAZAKE N’ZABWINO PAMENE N’ZOIPA

“Pali njila yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.”—MIYAMBO 14:12.

Kuyambila kale-kale, anthu ambili acitapo zinthu zimene anali kuona kuti n’zabwino, koma pambuyo pake anazindikila kuti zinali zoipa. Ngakhale kuti pocita zimenezo anali na zolinga zabwino, anakumanabe na mavuto cifukwa ca zisankho zawo zolakwika.

UMOYO NI WOSAPANGANIKA

“Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—YAKOBO 4:14.

Ngakhale munthu atakhala wabwino kwambili, akhoza kufa mosayembekezeleka. Mwacitsanzo, pa nthawi ya mlili wa COVID-19, anthu ambili odzipeleka kuti athandize ena anamwalila. Kapena ganizilani za mayi wina wa ku China dzina lake Liting, amene atate ake anamwalila pa ngozi ya motoka. Iye anati: “Sin’namvetse cifukwa cake munthu wokoma mtima conco anafa. Atate anali munthu wolimbikila nchito, wodzicepetsa, komanso woona mtima. Koma ndiwo okha amene anafa pa ngozi ya motokayo.”

Ngati kukhala munthu wabwino pakokha sikungathandize munthu kukhala na tsogolo labwino, ndiye cingathandize n’ciani? Kuti funso limeneli liyankhidwe na ena amene tingakhale nawo, tifunikila gwelo la malangizo odalilika amene angatithandize kudziŵa zimene tingacite kuti tikhale na tsogolo labwino. Kodi malangizo amenewo tingawapeze kuti?

a Kuti mudziŵe zambili za ciphunzitso ca Confucius, onani mutu 7, ndime 31-35, m’buku lakuti Mankind’s Search for God, lofalitsidwa na Mboni za Yehova, ndipo lilipo pa webusaiti yathu ya www.jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani