LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 3 masa. 12-14
  • N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MALANGIZO OCOKELA KWA WINAWAKE WANZELU KWAMBILI
  • Baibo Ni Gwelo la Malangizo Odalilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
    Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
  • “Anthu Ofatsa Adzalandila Dziko Lapansi”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • 12 Zolinga
    Galamuka!—2018
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 3 masa. 12-14
Munthu akuŵelenga Baibo.

N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?

Monga taonela m’nkhani zapita, anthu amayesa kudzikonzela tsogolo labwino mwa kukhulupilila zinthu monga mphamvu inayake imene amati ndiyo imayendetsa zocitika pa umoyo wawo, maphunzilo, cuma, komanso kukhala munthu wabwino. Koma kucita zinthu zimenezi kuli ngati kuseŵenzetsa mapu yolakwika imene ingasoceletse munthu paulendo. Kodi izi zitanthauza kuti palibe malangizo odalilika amene angatithandize kukhala na tsogolo labwino? Iyai!

MALANGIZO OCOKELA KWA WINAWAKE WANZELU KWAMBILI

Popanga zisankho, nthawi zambili timafunsila malangizo kwa munthu wamkulu komanso wanzelu kuposa ife. Mofananamo, tingapeze malangizo odalilika otithandiza kukhala na tsogolo labwino kucokela kwa Winawake wamkulu komanso wanzelu kwambili kuposa ife. Malangizo ake tingawapeze m’buku limene linayamba kulembedwa zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Buku limenelo limachedwa Baibo.

N’cifukwa ciani muyenela kuikhulupilila Baibo? Cifukwa Mlembi wake ni wamkulu ndiponso wanzelu kwambili m’cilengedwe conse. Iye amachedwa “Wamasiku Ambili,” amene wakhalapo “kuyambila kalekale mpaka kalekale.” (Danieli 7:9; Salimo 90:2) Ni “Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga.” (Yesaya 45:18) Iye amatiuza kuti dzina lake ni Yehova.—Salimo 83:18.

Cifukwa cakuti Baibo ni yocokela kwa Mlengi wa anthu onse, sionetsa kuti anthu a mtundu wina kapena a cikhalidwe cina ni apamwamba kuposa ena. Malangizo ake amathandiza nthawi zonse, ndipo apindulitsa anthu kulikonse padzikoli. Baibo imapezeka m’zinenelo zambili, ndipo yafalitsidwa kwambili kuposa buku lina lililonse.a Conco anthu kulikonse angathe kuiŵelenga na kupeza malangizo amene angawathandize pa umoyo wawo. Izi zigwilizana na zimene Baibo imakamba zakuti:

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.

Mofanana na kholo limene limapeleka malangizo kwa ana ake, Yehova Mulungu ni Tate wacikondi amene amatithandiza kupitila m’Mawu ake Baibo. (2 Timoteyo 3:16) Tingadalile Mawu ake cifukwa iye ndiye anatilenga, ndipo amadziŵa zimene zingatithandize kukhala na umoyo wabwino.

MALANGIZO A M’BAIBO NI ODALILIKA

Zithunzi: 1. Munthu ali m’sitima ndipo akuŵelenga Baibo pa foni yake. 2. Pa foni yake paoneka mawu a m’Baibo.

Baibo ili na malangizo odalilika otithandiza kukhala na tsogolo labwino. Tingakhulupilile zimenezi cifukwa zaka 2,000 zapitazo inakambilatu zocitika za padziko komanso khalidwe la anthu limene timaona masiku ano.

ZOCITIKA ZA PADZIKO

“Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzacitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala milili ndi njala m’malo osiyanasiyana.”—LUKA 21:10, 11.

KHALIDWE LA ANTHU

“Koma dziwa kuti, masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale awo, osafuna kugwilizana ndi anzawo, onenela anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” —2 TIMOTEYO 3:1-4.

Kodi muganiza zinatheka bwanji kuti Baibo ikambiletu molondola zinthu zimene zikucitika masiku ano? Mosakayikila, mungavomeleze zimene Leung wa ku Hong Kong anakamba, zakuti: “Maulosi a m’Baibo analembedwa kale-kale. Palibe munthu aliyense amene akanakwanitsa kukambilatu zinthu zimenezi molondola. N’zoonekelatu kuti Baibo inauzilidwa na wina wake wanzelu kwambili kuposa anthufe.”

M’Baibo muli maulosi amene anakwanilitsidwa.b Izi zimatsimikizila kuti Baibo ni Mawudi a Mulungu. Yehova anati: “Ine ndine Mulungu ndipo palibenso Mulungu wina, kapena aliyense wofanana ndi ine. Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi.” (Yesaya 46:9, 10) Conco pali zifukwa zomveka zokhulupilila zimene Baibo imakamba ponena za kutsogolo.

M’BAIBO MULI MALANGIZO AMENE ANGAKUTHANDIZENI PALIPANO KOMANSO KWAMUYAYA

Makolo agwilana manja na ana awo, ndipo akuyenda mwacimwemwe m’munda.

Mukamatsatila malangizo a m’Buku Lopatulika, mudzapindula. Onani zitsanzo izi.

KUONA NDALAMA NA NCHITO MOYENELA

“Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—MLALIKI 4:6.

UMOYO WA BANJA

“Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”—AEFESO 5:33.

MOKHALILA NA ANTHU ENA

“Usapse mtima ndipo pewa kukwiya. Usapse mtima kuti ungacite coipa.”—SALIMO 37:8.

Kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kungakupindulitseni palipano komanso kungakupatseni mwayi wokhala na tsogolo labwino. M’Baibo muli malonjezo a Mulungu abwino kwambili. Ena mwa malonjezowo ni awa:

MTENDELE NA CITETEZO

“Adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—SALIMO 37:11.

ALIYENSE ADZAKHALA NA MALO OKHALA KOMANSO CAKUDYA

“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”—YESAYA 65:21.

SIKUDZAKHALANSO MATENDA KAPENA IMFA

“Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—CHIVUMBULUTSO 21:4.

Kodi mungacite ciani kuti mukhale na tsogolo labwino conco? Ŵelengani nkhani yotsatila.

a Kuti mudziŵe zambili zokhudza nchito yomasulila Baibo na kufalitsidwa kwake, pitani pa www.jw.org na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MBILI KOMANSO BAIBULO.

b Kuti mudziŵe zambili, onani mutu 9 m’buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa na Mboni za Yehova. Bukuli lipezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org. Pitani ku Chichewa pa LAIBULALE > MABUKU NDI ZINTHU ZINA.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani