LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w21 October masa. 14-17
  • Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI PAMAKHALA ZOPINGA ZOTANI?
  • DZIIKILENI ZOLINGA ZIMEME MUNGAKWANITSE POKONZA UBWENZI WANU
  • MUSATAYE MTIMA!
  • ‘Itanani Akulu’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Yehova Amakukondani Kwambili!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Inu Akulu—Pitilizani Kutsanzila Mtumwi Paulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Yehova Ali Namwe, Simuli Mwekha
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
w21 October masa. 14-17
M’bale walefuka poona cinchito cimene adzakhala naco kuti amangenso nyumba yake.

Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova

CAKA ciliconse, nkhosa zambili zamtengo wapatali zimabwezeletsedwa mu mpingo wacikhristu. Tangoganizilani cisangalalo cacikulu cimene cimakhalako kumwamba munthu mmodzi akabwelela! (Luka 15:7, 10) Ngati munabwezeletsedwa mu mpingo, dziŵani kuti Yesu, angelo, komanso Yehova iye mwini, ni okondwela ngako kukuonani kuti mwanyamukanso na kuima kumbali ya coonadi. Komabe, pamene mukonza ubwenzi wanu na Yehova, mungakumane na zopinga. Kodi zina mwa zopingazo n’ziti? Nanga n’ciani cingakuthandizeni kuzigonjetsa?

KODI PAMAKHALA ZOPINGA ZOTANI?

Ambili amakhala na maganizo olefula pambuyo pobwelela mu mpingo. Mwina mungamvetse mmene Mfumu Davide anamvelela. Ngakhale pambuyo pokhululukidwa macimo ake, iye anati: “Zolakwa zanga zandikulila.” (Sal. 40:12; 65:3) Munthu akabwelela kwa Yehova, angakhalebe na maganizo odziimba mlandu, kapena kukhala wamanyazi kwa zaka ndithu. Isabelle, amene anali wocotsedwa kwa zaka zoposa 20,a anati: “Cinali covuta kwambili kwa ine kukhulupilila kuti Yehova anganikhululukile.” Mukalefuka, mungafooke mwauzimu. (Miy. 24:10) Conco, musalole zimenezi kukucitikilani.

Ena amaopa kuti sadzakwanitsa kucita zonse zofunikila kuti abwezeletsecifukwa ca kaamba ka cifukwa ndaŵa ubale wawo na Yehova. Antoine atabwezeletsedwa, anati: “N’nali kuona kuti n’naiŵala zinthu zambili zimene n’nali kucita nili Mboni.” Pa cifukwa cimeneci, ena amazengeleza kutengako mbali mokwanila pa zauzimu.

Mwacitsanzo, munthu amene nyumba yake yawonongeka kwambili na cimphepo camkuntho, angagwe mphwayi akaganizila nthawi na mphamvu zimene ayenela kutailapo kuti amangenso nyumbayo. Mofananamo, ngati ubwenzi wanu na Yehova unawonongeka cifukwa cocita chimo lalikulu, mungamaone kuti muli na cinchito cacikulu kuti mukonzenso ubwenziwo. Koma musade nkhawa, thandizo lilipo.

Yehova akutipempha kuti: “Bwelani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambilane.” (Yes. 1:18) Pofika pano, mwayesetsa kukonza zinthu. Yehova ni wokondwa ngako cifukwa ca khama lanu. Ganizilani izi: Cifukwa cakuti munabwelela kwa Yehova, mwakhala citsanzo coonetsa kuti Mdyelekezi ni wabodza.—Miy. 27:11.

Kubwelela kwanu mu mpingo, kwaonetsa kale kuti mwamuyandikila Yehova, ndipo nayenso analonjeza kuti adzakuyandikilani. (Yak. 4:8) Abale na alongo ni okondwela kuti munabwelela mu mpingo. Komabe, palinso zina zimene muyenela kucita. Muyenela kupitiliza kulimbitsa cikondi pa Atate wanu, komanso Bwenzi lanu Yehova. Mungacite bwanji zimenezi?

DZIIKILENI ZOLINGA ZIMEME MUNGAKWANITSE POKONZA UBWENZI WANU

Yesani kudziikila zolinga zimene mungakwanitse. Mwina mukali kukumbukila zimene munaphunzila zokhudza Yehova, komanso lonjezo lake la Paradaiso. Koma lomba muyenela kukhalanso na pulogilamu ya zauzimu, monga kulalikila nthawi zonse, kusonkhana, komanso kuceza na abale na alongo. Ganizilani zolinga izi.

Muzipemphela kwa Yehova nthawi zonse. Atate wanu adziŵa kuti mukamapitiliza kudziimba mlandu, cingakuvuteni kupemphela kwa iye. (Aroma 8:26) Ngakhale conco, “limbikilani kupemphela,” muuzeni Yehova kuti mufunitsitsa kukhala naye paubwenzi wolimba. (Aroma 12:12) Andrej anati: “N’nali kudziimba mlandu kwambili, komanso n’nali kucita manyazi. Koma pambuyo pa pemphelo lililonse n’nali kumvelako bwino. N’nali kukhala na mtendele wamaganizo.” Ngati simudziŵa zimene mungachule m’pemphelo, phunzilani pa mapemphelo amene Mfumu Davide yolapa inapeleka, olembedwa pa Salimo 51 na 65.

Muziŵelenga Baibo nthawi zonse. Izi zidzakuthandizani kukhala na cikhulupililo colimba, komanso kukulitsa cikondi canu pa Yehova. (Sal. 19:7-11) Felipe anati: “Cifukwa cosakhala na pulogilamu yoŵelenga Baibo nthawi zonse, n’nafooka ndipo n’namgwilitsa mwala Yehova. Sin’nafune kubwelezanso colakwaco. Conco, n’naonetsetsa kuti nikucita phunzilo laumwini nthawi zonse.” Na imwe mungacite cimodzi-modzi. Ngati mufuna thandizo pa nkhani zimene mungaŵelenge pa phunzilo lanu laumwini, bwanji osapempha mnzanu wofikapo mwauzimu kuti akuthandizeni.

Konzaninso ubwenzi wanu na abale na alongo. Ena amene anabwelela mu mpingo, anali na nkhawa yakuti abale na alongo adzayamba kuwaona mosayenela. Larissa anati: “N’nali kucita manyazi kwambili. N’nali kuona kuti n’nakhumudwitsa mpingo. Maganizo amenewa n’nakhala nawo kwa nthawi yaitali.” Dziŵani kuti akulu komanso Akhristu ena okhwima, ni ofunitsitsa kukuthandizani kukonzanso ubwenzi wanu na Yehova. (Onani bokosi lakuti, “Zimene Akulu Angacite”) Iwo ni okondwela kuti munabwelela, ndipo afuna kuti zizikuyendelani bwino.—Miy. 17:17.

N’ciani cingakuthandizeni kuyandikila mpingo? Muzicita mokwanila zimene abale na alongo amacita, monga kupezeka ku misonkhano, komanso kulalikila nthawi zonse. Kodi izi zingakuthandizeni bwanji? Felix anati: “Mpingo unali kuniyembekezela mwacidwi kuti nibwelele. N’naona kuti ndine wofunika. Onse ananithandiza kuti nikhalenso m’banja lauzimu, kuona kuti Yehova ananikhululukila, komanso kupitiliza kum’tumikila.”—Onani bokosi lakuti, “Zimene Mungacite.”

Zimene Mungacite

Konzaninso umoyo wanu wauzimu

Mkulu akupemphela pamodzi na m’bale amene wabwela kwa Yehova.

MUZIPEMPHELA KWA YEHOVA NTHAWI ZONSE

Muuzeni Yehova kuti mufunitsitsa kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Akulu adzapemphela namwe pamodzi

Mkulu akutsogoza phunzilo m’baleyo m’buku lakuti, “Yandikilani kwa Yehova.”

MUZIŴELENGA BAIBO NTHAWI ZONSE

Muzidya cakudya cauzimu, ndipo izi zidzakuthandizani kukulitsa cikondi canu pa Yehova

M’baleyo akukambilana na ena pa maceza olimbikitsa.

KONZANINSO UBWENZI WANU NA ABALE KOMANSO ALONGO

Muzigwilizana kwambili na mpingo, kupezeka ku misonkhano, na kulalikila

MUSATAYE MTIMA!

Satana adzapitiliza kukuponyelani “zimphepo zamkuntho” za mayeso kuti akufooketseni pamene mukonzanso ubwenzi wanu na Yehova. (Luka 4:13) Konzekelani kulimbana na mavutowo mwa kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova pali pano.

Ponena za nkhosa zake, Yehova analonjeza kuti: “Nkhosa zosocela ndidzazifunafuna, zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa.” (Ezek. 34:16) Yehova wathandiza anthu osaŵelengeka kukonzanso ubale wawo na iye. Dziŵani kuti amafuna kukuthandiza kupitiliza kulimbitsa ubale wanu na iye.

Zimene Akulu Angacite

Mkulu akuthandiza m’bale kumanganso nyumba yake yowonongeka.

Akulu amacita mbali yofunika kuthandiza ofalitsa obwezeletsedwa mu mpingo kukonzanso ubale wawo na Yehova. Nazi zimene angacite.

Muziŵalimbikitsa. Mtumwi Paulo anadziŵa kuti munthu wocimwa amene walapa, angakhale na ‘cisoni copitilila malile.’ (2 Akor. 2:7) Ndiponso angakhale wamanyazi komanso wodziona kukhala wosanunkha kanthu. Paulo anauza mpingo kuti: “Mukhululukileni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza.” Anthu obwezeletsedwa afunika kuwatsimikizila kuti Yehova komanso okhulupilila anzawo amawakonda kwambili. Ngati nthawi zonse akulu amawalimbikitsa na kuwathandiza, iwo sadzalefuka.

Muzipemphela nawo. “Pembedzelo la munthu wolungama limagwila nchito mwamphamvu kwambili.” (Yak. 5:16) Larissa, amene tam’chula poyamba, anati: “N’nauza akulu nkhawa zanga. Iwo anapemphela nane. Ndipo n’naona kuti akulu sananikwiyile. Anali kufuna kunithandiza kukonzanso ubale wanga na Yehova. Mapemphelo awo ananithandiza kuona kuti Yehova amanikondadi, ndipo amaona zabwino mwa ine osati zoipa.”

Khalani mabwenzi awo. Anthu obwezeletsedwa afunikila mabwenzi mu mpingo. Mkulu wina dzina lake Justin anati: “Tiziwapempha kuti tiseŵenze nawo mu ulaliki, ndipo cofunika kwambili, tiziwacezela ku nyumba kwawo. Kukhala nawo pa ubwenzi n’kofunika ngako!” Mkulu winanso dzina lake Henry anati: “Ngati ena mu mpingo aona akulu akupanga ubwenzi na munthu amene wabwezeletsedwa, naonso amacita cimodzi-cimodzi.”

Alimbikitseni kucita phunzilo laumwini. Bwenzi lokhwima mwauzimu lingathandize wobwezeletsedwa kukhala na pulogilamu yabwino yocita zauzimu. Mkulu wina dzina lake Darko anati: “Nimakonda kuuzako ena cuma cauzimu cimene napeza pa phunzilo laumwini, komanso mmene napindulila. Cina, nimaphunzila nawo pamodzi nkhani zolimbikitsa zimene napeza.” Mkulu winanso dzina lake Clayton ananena kuti: “Nimawalimbikitsa kupeza nkhani za m’Baibo zimene zigwilizana kwambili na zimene iwo anapitamo.”

Citani ubusa kwa iwo. Anthu obwezeletsedwa anaona akulu akucita mbali ya oweluza. Koma lomba, ayenela kuona akuluwo akucita mbali yawo monga abusa. (Yer. 23:4) Conco, muziwamvetsela na kuwayamikila. Muzikambilana nawo kaŵili-kaŵili. Onani zimene Marcus, amene ni mkulu, amacita pa maulendo ake aubusa: “Timakambilana nawo mfundo ya m’Malemba, kuwayamikila, na kuwatsimikizila kuti ife komanso Yehova, timawanyadila cifukwa ca kuyesetsa mwakhama kubwelela mu mpingo. Pambuyo pa ulendo wa ubusa uliwonse, timapangana nawo tsiku limene tikabwelanso.”

a Maina m’nkhani ino asinthidwa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani