LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w22 June masa. 14-19
  • Cikondi ca Yehova Cimatithandiza Kugonjetsa Mantha

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cikondi ca Yehova Cimatithandiza Kugonjetsa Mantha
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NKHAWA YAKUTI SITIDZAKWANITSA KUPEZA ZOSOŴA ZA BANJA LATHU
  • KUOPA ANTHU
  • KUOPA IMFA
  • KUGONJETSA MANTHA ATHU
  • Mmene Mungakhalile Bwenzi La Mulungu
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
w22 June masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 26

Cikondi ca Yehova Cimatithandiza Kugonjetsa Mantha

“Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.”—SAL. 118:6.

NYIMBO 105 “Mulungu Ndiye Cikondi”

ZIMENE TIKAMBILANEa

1. Ni zinthu zina ziti zimene zimatipangitsa kukhala na nkhawa?

GANIZILANI zocitika zenizeni izi za pa umoyo. M’bale Nestor na mkazi wake María, anali kufuna kukatumikila ku malo osoŵa.b Kuti akwanitse kucita zimenezo, iwo anafunika kusinthako zinthu zina pa umoyo wawo. Koma anali na nkhawa yakuti mwina sadzakhala acimwemwe ngati ali na ndalama zocepa. Pamene Biniam anakhala wa Mboni za Yehova m’dziko limene nchito yathu imatsutsidwa, iye anazindikila kuti pokhala mmodzi wa anthu a Mulungu adzazunzidwa. Zimenezo zinamucititsa mantha. Anacitanso mantha kwambili ataganizila zimene a m’banja lake adzacita akamva kuti waloŵa cipembedzo cina. Mlongo Valérie anam’peza na matenda a mtundu wina wake wa khansa umene umafalikila mofulumila m’thupi. Mlongoyu anavutika kupeza dokotala amene akanalemekeza zimene amakhulupilila ponena za magazi. Iye anali na nkhawa yakuti mwina angamwalile.

2. N’cifukwa ciyani tiyenela kuyesetsa kugonjetsa mantha athu?

2 Kodi zaconco zinakucitikilam’poni? Ambili a ife zinaticitikilapo. Ngati tilephela kugonjetsa mantha, tingapange zisankho zolakwika zimene zingawononge ubale wathu na Yehova. N’zimene Satana amafuna. Iye amagwilitsanso nchito mantha athu kuti atipangitse kuphwanya malamulo a Yehova, kuphatikizapo lamulo la kulalikila uthenga wabwino. (Chiv. 12:17) Satana ni woipa, wankhanza, komanso wamphamvu. Koma n’zotheka kudziteteza kuti iye asatikole. Motani?

3. N’ciyani cingatithandize kugonjetsa mantha?

3 Tikakhulupilila kuti Yehova amatikonda komanso kuti ali kumbali yathu, tingagonjetse mayeso a Satana. (Sal. 118:6) Mwacitsanzo, wolemba Salimo 118 anakumana na zinthu zina zothetsa nzelu. Iye anali na adani ambili, ndipo ena anali anthu audindo (vesi 9, 10). Nthawi zina anali kukhala wopanikizika kwambili (vesi 13). Cina, Yehova anam’patsa cilango camphamvu (vesi 18). Ngakhale zinali conco, wamasalimoyo anaimba kuti: “Sindidzaopa.” N’ciyani cinamupangitsa kumva kuti ni wotetezeka? Iye anadziŵa kuti Yehova, Atate wake wakumwamba, anali kum’konda olo kuti anam’patsa cilango. Wamasalimoyo anali na cidalilo cakuti kaya akumane na mavuto otani, Mulungu wake wacikondi adzapitiliza kumuthandiza.—Sal. 118:29.

4. Ni mantha ati amene tingagonjetse tikamakhulupilila kuti Mulungu amatikonda?

4 Tiyenela kukhulupilila kuti Yehova amatikonda. Kukhulupilila zimenezi kudzatithandiza kugonjetsa mantha amene timakhala nawo, monga, (1) nkhawa yakuti sitidzakwanitsa kupeza zofunikila za banja lathu; (2) kuopa anthu, ndiponso (3) kuopa imfa. Anthu amene tawachula m’ndime yoyamba anagonjetsa mantha awo cifukwa cokhulupilila kuti Mulungu amawakonda.

NKHAWA YAKUTI SITIDZAKWANITSA KUPEZA ZOSOŴA ZA BANJA LATHU

M’bale na mwana wake akupha nsomba na ukonde.

M’bale na mwana wake, akupha nsomba kuti apeze zosoŵa zakuthupi za banja (Onani ndime 5)

5. Ni zocitika ziti zimene zingapangitse mitu ya mabanja kukhala na nkhawa? (Onani cithunzi pacikuto.)

5 Mkhristu amene ni mutu wa banja sautenga mopepuka udindo wosamalila banja lake kuthupi. (1 Tim. 5:8) Ngati ndinu mutu wa banja, n’kutheka kuti pa nthawi ya mlili wa COVID-19, munada nkhawa kuti mwina nchito yanu ingathe. Cifukwa ca zimenezo, mwina munali na nkhawa yakuti simudzakwanitsa kupeza cakudya ca banja lanu na malo okhala. N’kutheka kuti munalinso na nkhawa yakuti ngati nchito yanu ingathe, simudzapezanso ina. Mofanana na m’bale Nestor komanso mkazi wake María amene tawachula kuciyambi, mwina inunso munali kudodoma kusinthako zinthu zina kuti mukhale na umoyo wosalila zambili. Satana wapambana pa nchito yake yolepheletsa anthu ambili kutumikila Yehova cifukwa iwo amakhala na mantha otelowo.

6. Kodi Satana amafuna tizikhulupilila ciyani?

6 Satana amafuna tizikhulupilila kuti Yehova sasamala za munthu aliyense payekha, komanso kuti sangatithandize kupeza zosoŵa za banja lathu. Mwa ici, tingayambe kuyesetsa kucita zonse zotheka kuti tisunge nchito yathu, ngakhale kuti kucita zimenezo kungafune kuti tinyalanyaze mfundo za m’Malemba.

7. Kodi Yesu amatitsimikizila ciyani?

7 Yesu, amawadziŵa bwino Atate wathu wakumwamba kuposa wina aliyense. Iye amatitsimikizila kuti Mulungu wathu, ‘amadziŵa zimene tikufuna tisanapemphe n’komwe.’ (Mat. 6:8) Ndipo Yesu amadziŵa kuti Yehova ni wokonzeka kutipatsa zosoŵa pa umoyo. Ife Akhristu tili m’banja la Mulungu. Tingakhale otsimikiza kuti Yehova pokhala Mutu wa banja, adzalemekeza mfundo imene anailemba pa 1 Timoteyo 5:8.

Mlongo na mwana wake wamng’ono akucapa zovala pa manja. M’bale na mkazi wake awabweletsela cakudya.

Yehova adzaonetsetsa kuti tili na zofunikila pa umoyo. Iye angaseŵenzetse abale athu potithandiza (Onani ndime 8)d

8. (a) N’ciyani cingatithandize kuthetsa nkhawa yakuti sitidzakwanitsa kusamalila banja lathu? (Mateyu 6:31-33) (b) Malinga na cithunzi ico, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca banja limene likugaŵana cakudya na mlongo wina?

8 Tikamakhulupilila kuti Yehova amatikonda pamodzi na banja lathu, tingakhale na cidalilo cakuti tidzapeza zofunikila pa umoyo. (Ŵelengani Mateyu 6:31-33.) Yehova amatipatsa zosoŵa pa umoyo, ndipo iye ni wacikondi komanso Mpatsi wowolowa manja. Polenga dziko lapansi, sanangotipatsa cabe zinthu zofunikila pa umoyo. Mwa cikondi cake, Mulungu anadzaza dziko lapansi na zinthu zambili zabwino kuti tizisangalala na umoyo. (Gen. 2:9) Ngakhale kuti nthawi zina sitingakhale na zonse zimene tingafune pa umoyo, tizikumbukila kuti zofunikila kwenikweni zimene tili nazo ni Yehova amene watipatsa. (Mat. 6:11) Tizikumbukilanso kuti zinthu zakuthupi zimene tingadzimane pali pano, sizingalingane na zimene Mulungu wathu wacikondi angatipatse pa nthawi ino komanso m’tsogolo. M’bale Nestor na mkazi wake María anaona kuti mfundo imeneyi ni yoona.—Yes. 65:21, 22.

9. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca m’bale Nestor na mkazi wake María?

9 M’bale Nestor na mkazi wake María anali na umoyo wofeŵa ku Colombia. Iwo anati: “Tinaganiza zokhala na umoyo wosalila zambili kuti tiwonjezele utumiki wathu, koma tinali na nkhawa yakuti sitidzakhala acimwemwe tikacita zimenezo.” Kodi n’ciyani cinawathandiza kuthetsa nkhawa yawo? Iwo anaganizila mmene Yehova anawaonetsela cikondi m’njila zambili. Izi zinawapatsa cidalilo cakuti Yehova adzawasamalila nthawi zonse. Conco, anasiya nchito zawo za malipilo apamwamba, anagulitsa nyumba yawo, ndipo anapita kukatumikila ku dela lina kumene alengezi a Ufumu anali ocepa. Kodi iwo amamva bwanji akaganizila za cisankho cawo? M’bale Nestor anati: “Taona kuti mawu a pa Mateyu 6:33 ni oona. Sitinasoŵepo zilizonse zakuthupi. Ndipo tili na cimwemwe coculuka tsopano.”

KUOPA ANTHU

10. N’cifukwa ciyani m’pomveka kuti anthu amaopana?

10 Kungocokela pamene Adamu na Hava anapandukila Yehova, anthu akhala akupweteka anthu anzawo. (Mlal. 8:9) Mwacitsanzo, anthu amagwilitsa nchito ulamulilo molakwika, ophwanya malamulo amacita zaciwawa, ana a sukulu ena amanyoza anzawo a m’kalasi na kuwaopseza, ndipo anthu ena amacitila nkhanza ngakhale anthu a m’banja mwawo. Conco, n’zosadabwitsa kuti anthufe timaopana. Tikamaopa anthu, Satana amatengelapo mwayi wakuti atikole. Motani?

11-12. Kodi Satana amauseŵenzetsa bwanji msampha woopa anthu pofuna kutikola?

11 Satana amagwilitsa nchito msampha woopa anthu pofuna kutilepheletsa kucita zimene Mulungu amafuna, komanso kugwila nchito yolalikila. Mosonkhezeledwa na Satana, maboma aletsa nchito yathu yolalikila, komanso amatizunza. (Luka 21:12; Chiv. 2:10) M’dzikoli lolamulidwa na Satana, anthu ambili amafalitsa nkhani zosoceletsa, komanso mabodza amkunkhuniza okhudza Mboni za Yehova. Anthu amene amakhulupilila mabodza amenewa angayambe kutiseka, ngakhale kuticitila zacipongwe. (Mat. 10:36) Kodi macenjela a Satana ni acilendo kwa ife? Kutalitali! Iye anali kugwilitsa nchito macenjela amenewo ngakhale m’nthawi ya atumwi.—Mac. 5:27, 28, 40.

M’bale wacinyamata wavala bwino popita ku msonkhano, ndipo alibe nkhawa. Koma makolo ake akumunyoza ataimilila pakhomo la nyumba yawo.

Ngakhale a m’banja mwathu atitsutse, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova amatikonda (Onani ndime 12-14)e

12 Kuopa kutsutsidwa na boma si ndiko cida cokha cimene Satana amaseŵenzetsa. Anthu ena amaopa kuphunzila coonadi akaganizila mmene a m’banja mwawo zingawakhudzile. Amaopa zimenezi kuposa mmene amaopela kumenyedwa. Iwo amakonda acibale awo, ndipo amafuna kuti nawonso am’dziŵe Yehova na kuyamba kum’konda. Amamva kuipa pamene acibale awo akamba zonyoza Mulungu woona kapena alambili ake. Komabe, zacitikapo kuti acibale amene poyamba anali otsutsa anaphunzila coonadi. Koma kodi tingacite ciyani ngati a m’banja mwathu alekelatu kuyanjana nafe cifukwa ca cikhulupililo cathu?

13. Kodi kukhulupilila kuti Yehova amatikonda kungatithandize bwanji ngati a m’banja mwathu atikana? (Salimo 27:10)

13 Mawu olimbikitsa a pa Salimo 27:10 (ŵelengani) angatitonthoze. Tikamakumbukila kuti Yehova amatikonda, timamva kukhala otetezeka anthu ena akamatitsutsa. Ndipo timakhala na cidalilo cakuti iye adzatifupa cifukwa ca kupilila kwathu. Kuposa wina aliyense, Yehova adzatipatsa zosoŵa zakuthupi, zauzimu, na kutithandiza kukhala acimwemwe. Izi n’zimene zinacitika kwa m’bale Biniam amene tam’chula kuciyambi.

14. Kodi tingaphunzilepo ciyani pa citsanzo ca Biniam?

14 Biniam anakhala wa Mboni za Yehova ngakhale kuti anadziŵa kuti adzazunzidwa. Onani mmene kudziŵa kuti Yehova amamukonda kunam’thandizila kugonjetsa mantha oopa anthu. Iye anati: “Kunena zoona, cizunzoco cinali coopsa. Koma cimene n’nali kuopa kwambili kuposa cizunzo cocokela ku boma, ni kutsutsidwa na a m’banja mwanga. N’nali kuopa kuti nikakhala wa Mboni za Yehova, atate amene anali osakhulupilila adzakhumudwa, komanso a m’banja mwanga adzaleka kunilemekeza.” Ngakhale n’conco, Biniam anali kukhulupilila kuti Yehova nthawi zonse amasamalila anthu amene iye amawakonda. Iye anakambanso kuti: “N’naganizila mmene Yehova anathandizila anthu ena kupilila mavuto a zacuma, tsankho, komanso anthu ocita zaciwawa. N’nali kudziŵa kuti nikam’mamatila Yehova, adzanidalitsa. N’tamangidwa kangapo konse na kucitidwa nkhanza nthawi zina, n’naonadi kuti Yehova amatithandiza pa nthawi zovuta tikakhalabe okhulupilika kwa iye.” Yehova anakhala Tate weniweni kwa Biniam, ndipo abale na alongo anakhala ngati a m’banja lake lenileni.

KUOPA IMFA

15. N’cifukwa ciyani n’cibadwa kuopa imfa?

15 Baibo imakamba kuti imfa ni mdani. (1 Akor. 15:25, 26) Kungoiganizila cabe imfa kungatipatse nkhawa, maka-maka ngati ife kapena munthu amene timakonda wadwala mwakaya-kaya. N’cifukwa ciyani timaiopa imfa? Cifukwa Yehova anatilenga na mtima wofuna kusangalala na moyo kwamuyaya. (Mlal. 3:11) Ngakhale n’telo, kuopa imfa pa mlingo woyenela kungatithandize kuteteza moyo wathu. Mwacitsanzo, kungatithandize kupanga zisankho zoyenela pa nkhani ya cakudya, kucita maseŵela olimbitsa thupi, kufuna cithandizo ca dokotala kapena kupeza mankhwala tikadwala, komanso kupewa kucita zinthu zoika moyo pa ciopsezo.

16. Kodi Satana amatengelapo mwayi motani pa mantha athu acibadwa oopa imfa?

16 Satana amadziŵa kuti moyo wathu timaukonda. Iye amakamba kuti tingalolele kutaya ciliconse—ngakhale ubwenzi wathu na Yehova, cabe kuti tiuteteze. (Yobu 2:4, 5) Limeneli ni bodza lamkunkhuniza! Komabe, popeza kuti Satana “ali ndi njila yobweletsela imfa,” amagwilitsa nchito mantha athu acibadwa oopa imfa pofuna kutipangitsa kumusiya Yehova. (Aheb. 2:14, 15) Nthawi zina, anthu amene ali ku mbali ya Satana amaopseza anthu a Yehova kuti adzawapha ngati saleka kutumikila Mulungu. Nthawi zinanso, tikadwala matenda aakulu, iye angatengelepo mwayi wotipangitsa kuphwanya malamulo a Mulungu. Madokotala kapena acibale amene si Mboni angatikakamize kuti tilole kuikidwa magazi, kumene kungakhale kuphwanya lamulo la Mulungu. Kapena, wina angatinyengelele kuti tilandile cithandizo ca mankhwala cosemphana na mfundo za m’Malemba.

17. Malinga na Aroma 8:37-39, n’cifukwa ciyani imfa sitiyenela kuiopa kwenikweni?

17 Olo kuti sitifuna kufa, tidziŵa kuti Yehova sadzaleka kutikonda ngakhale timwalile. (Ŵelengani Aroma 8:37-39.) Mabwenzi a Yehova akamwalila, iye amawakumbukilabe, ngati kuti akali moyo. (Luka 20:37, 38) Amacita kulakalaka kuwaukitsa. (Yobu 14:15) Yehova anapeleka malipilo apamwamba kwambili kuti ife ‘tikakhale na moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Tidziŵa kuti Yehova amatikonda kwambili komanso amatisamalila. Conco tikadwala, kapena akatiopseza kuti adzatipha, tisamusiye Yehova. M’malo mwake, tiyenela kutembenukila kwa iye kuti atitonthoze, atipatse nzelu, ndiponso mphamvu. Izi n’zimene mlongo Valérie na mwamuna wake anacita.—Sal. 41:3.

18. Kodi tingaphunzilepo ciyani pa citsanzo ca mlongo Valérie?

18 Pamene mlongo Valérie anali na zaka 35, anam’peza na mtundu wina wake wa khansa imene imafalikila mofulumila m’thupi. Onani mmene cikondi cinamuthandizila kuleka kuopa imfa. Iye anati: “Matendawo anasinthilatu umoyo wathu. Anafunika kunicita opaleshoni yaikulu kuti nikhale na moyo. N’nafikila madokotala ambili, koma onse anakana kunicita opaleshoni popanda kuniika magazi. N’nacita mantha, koma cifukwa ca lamulo la Mulungu, sinikanalola kuikidwa magazi. Pa umoyo wanga wonse, Yehova wakhala akunionetsa kuti amanikonda kwambili. Tsopano uwu unali mwayi wanga woonetsa kuti inenso nimam’konda Mulungu. Nthawi iliyonse akaniuza kuti matenda anga akukulila-kulila, m’pamenenso n’nali kukhala wofunitsitsa kwambili kukondweletsa Yehova kotelo kuti Satana asapambane. Potsilizila pake, ananicita opaleshoni popanda kuniika magazi, ndipo inayenda bwino. Ngakhale kuti nikali kudwala, Yehova wakhala akutipatsa zofunikila pa umoyo. Mwacitsanzo, kutangotsala masiku oŵelengeka asananipeze na matenda a khansa, pa msonkhano wa kumapeto kwa mlungu tinaphunzila nkhani yakuti, ‘Limbani Mtima Pokumana na Mavuto.’c Nkhaniyi inatitonthoza kwambili. Tinaiŵelenga mobweleza-bweleza. Kuŵelenga nkhani ngati imeneyi, komanso kukhala na pulogilamu yokhazikika yocita zauzimu, kwathandiza ine na mwamuna wanga kukhala na mtendele wa maganizo, osatekeseka, komanso kupanga zisankho zoyenela.”

KUGONJETSA MANTHA ATHU

19. N’ciyani cidzacitike posacedwa?

19 Mothandizidwa na Yehova, Akhristu padziko lonse lapansi agonjetsa zopinga zosiyana-siyana, ndipo apambana potsutsa Mdyelekezi. (1 Pet. 5:8, 9) Inunso mungakwanitse. Posacedwapa, Yehova adzalamula Yesu na olamulila anzake ‘kuti adzawononge nchito za Mdyelekezi.’ (1 Yoh. 3:8) Pambuyo pake, atumiki a Mulungu amene adzakhale padziko lapansi ‘sadzaopa aliyense. Ciliconse coopsa adzatalikilana naco.’ (Yes. 54:14; Mika 4:4) Koma pamene tikuyembekezela nthawiyo, tiyenela kuyesetsa kugonjetsa mantha athu.

20. N’ciyani cingatithandize kugonjetsa mantha athu?

20 Tiyeni tikulitsebe cidalilo cakuti Yehova amakonda atumiki ake komanso amawateteza. Tingatelo, posinkhasinkha na kuuzako ena za mmene Yehova anatetezela atumiki ake kumbuyoku. Cina, tiziganizila mmene Mulungu watithandizila patokha pa nthawi zovuta. Mwa thandizo la Yehova, tingakwanitse kugonjetsa mantha athu!—Sal. 34:4.

KODI CIKONDI CA YEHOVA CINGATITHANDIZE BWANJI . . .

  • kuthetsa nkhawa yakuti sitidzakwanitsa kupeza zosoŵa za banja lathu?

  • kugonjetsa mantha oopa anthu?

  • kugonjetsa mantha oopa imfa?

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

a Kucita mantha n’cibadwa, ndipo kungatiteteze ku zinthu zoopsa. Koma kukhala na mantha osayenela si kwabwino cifukwa kungatigwetsele m’mavuto. Motani? Satana angagwilitsile nchito mantha amenewo kuti atipangitse kupanga cisankho colakwika. Conco, tiyenela kuyesetsa kugonjetsa mantha otelowo. Kodi n’ciyani cingatithandize? Monga tionele m’nkhani ino, tikakhulupilila kuti Yehova ali ku mbali yathu komanso kuti amatikonda, tidzakwanitsa kugonjetsa mantha alionse.

b Maina ena asinthidwa.

c Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2012, mas. 7-11.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Banja likupita kukapeleka cakudya kwa mlongo pamodzi na banja lake. Mlongoyo amagwila nchito molimbika.

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Makolo a m’bale wacinyamata akumuletsa kutumikila Yehova, koma iye ali na cidalilo cakuti Mulungu adzam’thandiza.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani