LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 July tsa. 32
  • Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Ikani Patsogolo Zinthu Zofunika Kwambili
  • Khalani na Cizoloŵezi Cabwino Coŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Gwilitsilani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Ulaliki—“Khala Bwenzi la Yehova”
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Mfundo Yothandiza pa Kufufuza Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 July tsa. 32

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu

Ikani Patsogolo Zinthu Zofunika Kwambili

N’zoona kuti tonsefe timakhala na nthawi yocepa yocita phunzilo la munthu mwini. Koma kodi tingaiseŵenzetse motani kuti tizipindula kwambili? Coyamba, musamathamange. Mudzapindula kwambili mukamaŵelenga mfundo zocepa modekha, kuposa kuŵelenga mfundo zambili mothamanga.

Kenako, ikani patsogolo zinthu zofunika kwambili. (Aef. 5:15, 16) Onankoni malingalilo otsatilawa:

  • Muziŵelenga Baibo tsiku lililonse. (Sal. 1:2) Poyambila pabwino ni kuŵelenga macaputala a kuŵelenga Baibo kwa mlungu na mlungu pa msonkhano wa mkati mwa mlungu.

  • Muzikonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, na msonkhano wa mkati mwa mlungu, ndipo muzipelekapo ndemanga.—Sal. 22:22.

  • Malinga na nthawi imene muli nayo, muziyesetsa kudya cakudya cina zauzimu, monga kuonenela mavidiyo, kuŵelenga magazini ogaŵila, na zofalitsa zina za pa jw.org.

  • Muziŵelenga nkhani zimene muli nazo cidwi. Mungafufuze nkhani yokhudza vuto limene mukukumana nalo, funso limene muli nalo, kapena nkhani ya m’Baibo imene mufuna kumvetsetsa. Kuti mupeze malingalilo ena, pitani pa jw.org pa mbali yakuti “Bible Study Activities.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani