LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w23 November masa. 26-30
  • Napeza Citetezo Ceniceni Podalila Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Napeza Citetezo Ceniceni Podalila Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIYAMBI CA UMOYO WODALILA YEHOVA
  • KUDALILA YEHOVA M’DELA LIMENE NKHONDO INASAKAZA
  • KUKUMANA NA CITSUTSO M’DZIKO LA NIGER
  • “SITIDZIŴA ZAMBILI ZOKHUDZA NCHITO YA UFUMU MU GUINEA”
  • KUDALILA YEHOVA MONGA BANJA
  • GWELO LA CITETEZO CENICENI
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Coloŵa Cauzimu Cimene N’nalandila Cinanithandiza Kupita Patsogolo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Nakhala Nikuona Cikhulupililo ca Anthu a Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
w23 November masa. 26-30
Israel Itajobi.

MBILI YANGA

Napeza Citetezo Ceniceni Podalila Yehova

WOSIMBA NI MWINIWAKE: ISRAEL ITAJOBI

ANTHU akanifunsa zokhudza moyo wanga, nimaŵauza kuti, “Ndine katundu m’dzanja la Yehova!” Nimatanthauza kuti monga mmene ningatengele katundu wanga n’kupita naye kulikonse kumene nifuna, nimafunanso kuti Yehova na gulu lake azinisankhila kumene ningapite, komanso nthawi imene ningafunike kupita. N’navomelepo kucita mautumiki ovuta komanso oopsa. Koma n’naphunzila kuti kudalila Yehova n’kumene kumabweletsa citetezo ceniceni.

CIYAMBI CA UMOYO WODALILA YEHOVA

N’nabadwa mu 1948 m’mudzi waung’ono kummwela cakumadzulo kwa Nigeria. Panthawi imeneyo, atate aang’ono a Moustapha, komanso mkulu wanga Wahabi anabatizika kukhala Mboni za Yehova. Atate anamwalila nili na zaka 9. Izi zinanipweteka mtima kwambili. Wahabi ananiuza kuti tingadzawaonenso Atate pa nthawi ya ciukitso. Mawu otonthoza amenewa, ananilimbikitsa kuyamba kuphunzila Baibo. Conco, n’nabatizika mu 1963. Kenako, abale anga atatu nawonso anabatizika.

Mu 1965, n’napita kukakhala na mkulu wanga Wilson ku Lagos, ndipo zinali zosangalatsa kugwilizana na apainiya ena mu mpingo wa Igbobi. N’nalimbikitsidwa kuona cimwemwe komanso khama lawo. Conco, mu January 1968, nanenso n’nayamba upainiya.

M’bale Albert Olugbebi, amene anali kutumikila pa Beteli, anakonza miting’i yapadela ya acinyamata kuti akambe nafe zokhudza kusoŵekela kwa apainiya apadela kumpoto kwa Nigeria. Nikali kukumbukila mawu ogwila mtima a m’bale Olugbebi akuti: “Mukali acinyamata, mungaseŵenzetse nthawi na mphamvu zanu kutumikila Yehova. Utumiki wakutsegukilani!” Pofuna kutsanzila mzimu wodzipeleka wa mmeneneli Yesaya, ninapeleka fomu yofunsila utumikiwo.—Yes. 6:8.

Mu May 1968, n’natumizidwa monga mpainiya wapadela ku mzinda wa Kano, kumpoto kwa Nigeria. Apo nkhondo ya Biafran ili mkati (1967-1970). Nkhondo imeneyi inabweletsa mavuto osiyana-siyana, ndipo ambili anaphedwa. Kenako nkhondoyo inakabukilanso kum’mawa kwa Nigeria. Cifukwa conidela nkhawa, m’bale wina anayesetsa kuniletsa kuti nisapiteko kumeneko. Koma n’namuuza kuti: “Zikomo ponidela nkhawa. Koma ndine wotsimikiza kuti ngati Yehova afuna kuti nicitedi utumiki umenewu ndiye kuti iye adzakhala nane.”

Mapu yoonetsa malo na maiko ya ku West Africa, kumene m’bale Israel Itajobi anatumikila na kukhalako: Conakry, Guinea; Sierra Leone; Niamey, Niger; Kano, Orisunbare, komanso Lagos, Nigeria.

KUDALILA YEHOVA M’DELA LIMENE NKHONDO INASAKAZA

Zinthu sizinali bwino mu mzinda wa Kano. Nkhondo inali itawononga mzinda umenewu. Nthawi zina mu utumiki, tinali kupeza mitembo ya anthu amene anaphedwa pa nkhondoyi. Ngakhale munali mipingo ingapo mu mzinda wa Kano, abale ambili anali atathaŵa mu mzindawu. Munatsala ofalitsa ocepekela pa 15, omwe analinso na mantha komanso anataya mtima. Abale na alongo anakondwela ngako ataona kagulu kathu ka apainiya apadela okwanila 6 katafika m’delalo. Ofalitsa analandila cilimbikitso cathu. Tinawathandiza kuyambilanso kucita zauzimu, kutumiza malipoti a utumiki wa kumunda, komanso kuitanitsa zofalitsa ku nthambi.

Ife tonse monga apainiya apadela, tinayamba kuphunzila cinenelo ca Hausa. Cifukwa tinayamba kulengeza uthenga wabwino m’cinenelo ca kumaloko, anthu ambili anayamba kumvetsela. Komabe, ma membala a cipembedzo codziŵika kwambili ku Kano sanakondwele na nchito yathu yolalikila. Conco tinayamba kucita zinthu mosamala kwambili. Mwacitsanzo, tsiku lina ine na m’bale wina tili mu utumiki, munthu wina anatithamangitsa na mpeni, koma tinakwanitsa kuthaŵa ndipo tinapulumuka! Ngakhale kuti tinakumana na zoopsa, Yehova anatithandiza “kukhala otetezeka,” ndipo ciŵelengelo ca ofalitsa cinayamba kukula. (Sal. 4:8) Lomba, ku Kano kuli ofalitsa opitilila 500 amene akutumikila m’mipingo 11.

KUKUMANA NA CITSUTSO M’DZIKO LA NIGER

Kutumikila monga mpainiya wapadela ku Niamey, Niger

N’tatumikila miyezi yocepa mu mzinda wa Kano, mu August 1968, n’natumizidwa ku Niamey, mzinda waukulu m’dziko la Republic of Niger, limodzi na abale aŵili omwe nawonso anali apainiya apadela. Coyamba, tinazindikila kuti dziko la Niger lomwe lili kumadzulo kwa Africa, ni limodzi mwa madela otentha kwambili. Kuwonjezela pa kuyesetsa kuzoloŵela nyengo yotentha, tinafunikanso kuphunzila ci French, comwe n’cinenelo cacikulu m’dzikoli. Mosasamala kanthu za zovutazi, tinaika cidalilo cathu mwa Yehova, ndipo tinayamba kulalikila limodzi na ofalitsa ocepa a mu mzindawo. Sipanapite nthawi yaitali anthu ambili mu mzinda wa Miamey anayamba kuŵelenga na kulandila buku lophunzilila Baibo lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Ndipo ena anali kucita kutifunafuna kuti tiŵapatse buku limeneli!

Posakhalitsa, tinazindikila kuti akulu-akulu a boma m’delali sanali kukondwela na Mboni za Yehova. Mu July 1969, tinakhala na msonkhano wa dela woyamba m’dzikoli, ndipo panapezeka anthu 20. Tinali kuyembekezela mwacidwi kuona ofalitsa aŵili akubatizika. Koma pa tsiku loyamba la msonkhanowu apolisi anabwela na kuimitsa pulogalamu. Anatenga abale omwe anali apainiya apadela komanso woyang’anila dela n’kupita nawo ku polisi. Pambuyo potifunsa mafunso, anatiuza kuti tikabwelenso tsiku lotsatila. Cifukwa coganizila mavuto amene angadzakhalepo, tinakonza zoti nkhani ya ubatizo ikakambidwile ku nyumba. Komanso kuti ubatizo ukacitikile ku mtsinje koma mwakabisila.

Patapita milungu yocepa, boma linalamula kuti ine pamodzi na apainiya ena apadela 5 ticoke m’dzikoli. Tinapatsidwa maola 48 kuti tituluke. Ndipo nkhani ya mayendedwe tinafunika kukoza tokha. Tinamvela cigamulo cawo na kucoka. Kenako tinapita ku ofesi ya nthambi ku Nigeria, kumene tinalandilanso utumiki wina watsopano.

N’natumizidwa ku mudzi wa Orisunbare ku Nigeria kumenenso n’nasangalala na nchito ya ulaliki limodzi na ofalitsa ocepa a kumeneko. Pambuyo pa miyezi 6, ofesi inanipempha kuti nibwelele ku Niger, koma ulendowu n’nafunika kupita nekha. N’nadabwa komanso kuda nkhawa, koma pambuyo pake n’nakhala wofunitsitsa kukaonananso na abale a ku Niger!

Conco n’nabwelela ku Niamey. Tsiku lotsatila n’tafika, wamalonda wina wa ku Nigeria anazindikila kuti ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anayamba kunifunsa mafunso a m’Baibo. Kenako n’nayamba kuphunzila naye Baibo. Ndipo atakwanitsa kuthetsa cizoloŵezi cokoka fodya komanso kumwa moŵa kwambili, anabatizika. Kuyambila pamenepo, n’nakhala wosangalala kuthandizako pa nchito yolalikila m’madela osiyana-siyana m’dziko la Niger, imene inali kupita patsogolo mwapang’ono-pang’ono. Pa nthawi imene n’nafika, munali ofalitsa 31, koma pamene n’nali kucoka anafika 69.

“SITIDZIŴA ZAMBILI ZOKHUDZA NCHITO YA UFUMU MU GUINEA”

Cakumapeto kwa caka ca 1977, n’nabwelela ku Nigeria kuti nikalandile maphunzilo. Pambuyo pa maphunzilo a milungu itatu, m’bale Malcolm Vigo, yemwe anali mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi, ananipempha kuŵelenga kalata yocokele ku nthambi ya ku Sierra Leone. Abalewa anali kufuna m’bale yemwe anali na thanzi labwino, wosakwatila, komanso wotha kulankhula Cingelezi na ci French kuti akatumikile monga woyang’anila dela ku dziko la Guinea. M’bale Vigo ananiuza kuti, n’nalandila maphunzilowo cifukwa ca utumiki umenewu. Iye ananitsimikizila kuti utumiki umenewu sunali wopepuka. Ananiuza kuti, “Uganizilepo mofatsa usanauvomele.” Koma nthawi imeneyo n’namuyankha kuti, “Popeza ni Yehova amene afuna kuti nipite, n’zapita.”

N’nayenda ulendo wa ndege kupita ku Sierra Leone, ndipo n’nakumana na abale ku ofesi ya nthambi. M’bale wina wa m’komiti ya nthambi ananiuza kuti, “Sitidziŵa zambili zokhudza nchito ya Ufumu ku Guinea.” Ngakhale kuti ofesi ya nthambi inali kuyang’anila nchito yolalikila m’dziko la Guinea, zinali zovuta kulankhulana na ofalitsa m’dzikolo cifukwa ca mikangano yandale imene inali kumeneko. Kwa maulendo angapo, nthambi inayesa kutumiza m’bale ku Guinea, koma sizinatheke. Conco ananipempha kuti nipite mu mzinda wa Conakry, m’dziko la Guinea kuti nikapemphe akulu-akulu a boma ngati anganilole kukhala m’dzikolo.

“Popeza ni Yehova amene afuna kuti nipite, nizapita”

N’tafika ku Conakry, n’napita ku nyumba ya kazembe wa ku Nigeria, ndipo n’nalankhulana naye. N’namuuza za cifuno canga colalikila mu Guinea. Koma ananiuza kuti nibwelele cifukwa ningamangidwe kapena kucitilidwa zinthu zina zoipa. Iye anati, “Bwelela ku Nigeria ndipo uzikalalikila kumeneko.” Koma n’namuyankha kuti, “Ndine wofunitsitsa kukhala kuno.” Conco analemba kalata yopempha nduna yoona zam’kati mwa dzikolo kuti inithandize, ndipo inatelodi.

Posapita nthawi, n’nabwelela ku ofesi ya nthambi ku Sierra Leone, ndipo n’nadziŵitsa abale za cigamulo cimene nduna ya boma ija inapeleka. Abalewo anafuula mwacimwemwe n’taŵauza mmene Yehova anadalitsila ulendo wanga. N’nali n’tapatsidwa cilolezo cokakhala m’dzilo la Guinea!

M’bale Israel atanyamula katundu wake mosangalala.

Mu nchito ya dela ku Sierra Leone

Kucokela 1978 mpaka mu 1989, n’natumikila monga woyang’anila dela m’dziko la Guinea, Sierra Leone, komanso monga woyang’anila dela wogwilizila m’dziko la Liberia. Poyamba n’nali kudwala-dwala. Nthawi zina n’nali kudwala nili kumadela akutali. Koma abale anali kucita zonse zotheka kuti anipeleke ku cipatala.

Pa nthawi ina, n’nadwala kwambili maleliya, ndipo n’napezekanso na njoka za m’mimba. N’tacila, n’nazamva kuti abale anali kukambitsilana zakuti adzaniika manda ati. Ngakhale kuti moyo wanga unakhala pa ciopsezo cifukwa ca matendawa, sin’naganizepo zosiya utumiki wanga. N’nali kudziŵa kuti citetezo ceniceni komanso cokhalitsa cimacokela kwa Mulungu yekhayo amene angathe kuniukitsa kwa akufa.

KUDALILA YEHOVA MONGA BANJA

M’bale Israel ali na mkazi wake pa tsiku la cikwati cawo.

Pa tsiku la cikwati cathu mu 1988

M’caka ca 1988, n’nakumana na Dorcas, mlongo wodzicepetsa, komanso mpainiya wokonda zauzimu. Tinamanga banja, ndipo anayamba kunithandiza pa utumiki wanga monga woyang’anila dela. Dorcas anaonetsa kuti anali mkazi wacikondi ndiponso wodzipeleka. Posamuka kucoka pa mpingo wina kupita pa wina, tinali kuyenda maulendo atali-atali ngati makilomita 25 titanyamula katundu wathu. Ku mipingo imene inali kutali kwambili, tinali kuseŵenzetsa mayendedwe aliwonse akanapezeka, kudutsa m’misewu yamatope yokumbika-kumbika.

Dorcas ni wolimba mtima. Mwacitsanzo, nthawi zina tinafunika kuwoloka mitsinje yokhala ni ng’ona. Pa ulendo wina wa masiku 5, tinapeza kuti biliji ya pamtsinje yawonongeka. Conco tinagwilitsa nchito mabwato. Dorcas ataimilila kuti atsike m’bwato, mwatsoka lanji anagwela m’madzi. Tonse aŵili sitinali kudziŵa kunyaya, ndipo mu mtsinjemo munali ng’ona. Mwamwayi, mnyamata wina anadumphila m’madzimo na kum’pulumutsa. Zinatitengela masiku kuti tiiŵaleko cocitika cimeneci, koma ngakhale n’telo sitinasiye kucita utumiki wathu.

Jahgift na Eric ataimilila patsogolo pa Nyumba ya Ufumu.

Ana athu, Jahgift na Eric, ni mphatso zauzimu kwa ise

Cakumayambililo kwa 1992, tinakondwela kwambili kudziŵa kuti Dorcas anali na pakati. Kodi awa ni amene adzakhala mapeto a utumiki wathu? Tinati, “Yehova watipatsa mphatso!” Conco tinacha mwana wathu wamkazi Jahgift. Pambuyo pa zaka 4 Jahgift atabadwa, tinakhalanso na mwana wina ndipo tinamucha Eric. Timaona kuti ana athuwa ni mphatsodi zocokela kwa Yehova. Jahgift anatumikilako pa ofesi yomasulila mabuku ku Conakry, pamene Eric ni mtumiki wothandiza.

M’bale Israel na mlongo Dorcas ali na ana awo, Jahgift komanso Eric ataimilila patsogolo pa Nyumba ya Ufumu.

Dorcas anali atasiya upainiya wapadela, koma anapitilizabe kucita upainiya wa nthawi zonse ngakhale pamene tinali kulela ana athu. Na thandizo la Yehova, n’napitiliza utumiki wa nthawi zonse wapadela. Ana athu atakula, Dorcas anayambilanso upainiya wapadela. Lomba, tikutumikila limodzi monga amishonale ku Conakry.

GWELO LA CITETEZO CENICENI

Nakhala nikupita kulikonse kumene Yehova wanituma. Kwa maulendo angapo, ine na mkazi wanga tadzionela tokha citetezo na dalitso lake. Kudalila Yehova kwatiteteza ku mavuto obwela cifukwa codalila cuma. Zimene takumana nazo pa umoyo wathu zationetsa kuti Gwelo la citetezo ceniceni ni “Mulungu wacipulumutso cathu,” Yehova. (1 Mbiri 16:35) Ndine wotsimikiza kuti munthu aliyense amene amam’dalila, ‘Yehova Mulungu adzakulunga ndi kuteteza moyo wake m’phukusi la moyo.’—1 Sam. 25:29.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani