Malangizo a m’Baibo Amathandizadi
Baibo yathandiza anthu mamiliyoni ambili pa mbali zinayi izi za umoyo:
1. Ukwati
Anthu ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani ya ukwati, komanso zimene zingapangitse kuti ukwatiwo ukhale wacimwemwe.
BAIBO IMATI: “Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.
TANTHAUZO LAKE: Mulungu ndiye anayambitsa ukwati. Conco, adziŵa zimene okwatilana ayenela kucita kuti akhale acimwemwe. (Maliko 10:6-9) Banja limakhala la cimwemwe ngati mwamuna na mkazi wake amaika patsogolo zofuna za wina na mnzake. Mwamuna amaonetsa kuti amakonda mkazi wake mwa kumusamalila na kucita zinthu mwacikondi. Komanso mkazi amene amalemekeza mwamuna wake, amaonetsa ulemu mwa zokamba na zocita zake.
MALANGIZO A M’BAIBO NI OTHANDIZA: Quang na mkazi wake Thi, a ku Vietnam, anali kuona kuti n’zosatheka kukhala acimwemwe mu ukwati wawo. Nthawi zambili, Quang sanali kucita zinthu mokoma mtima na mkazi wake. Iye anati: “N’nalibe nazo kanthu za mmene anali kumvela, ndipo nthawi zambili n’nali kumucititsa manyazi.” Thi anaganiza zongothetsa cikwati. Iye anati: “N’nayamba kuona kuti siningamudalile kapena kumulemekeza mwamuna wanga.”
M’kupita kwanthawi, Quang na Thi anaphunzila zimene Baibo imanena, komanso mmene angaseŵenzetsele Aefeso 5:33 mu ukwati wawo. Quang anati: “Lembali linanithandiza kuona kufunika kokhala wokoma mtima. N’naonanso kuti niyenela kuthandiza Thi kumva kuti nimamukonda na kumusamalila kuthupi. Nikamacita izi, amanikonda na kunilemekeza.” Nayenso Thi anati: “Nikamalemekeza kwambili mwamuna wanga potsatila malangizo a pa Aefeso 5:33, m’pamene amanipangitsa kumva kuti ndine wokondedwa komanso wotetezeka, ndipo nimakhala na mtendele wa mumtima.”
Kuti mudziŵe zambili pa nkhani ya banja, ŵelengani Galamuka! ya Na. 2 2018, ya mutu wakuti “Zinsinsi 12 za Banja Lacimwemwe” pa jw.org.
2. Mocitila Zinthu na Anthu Ena
Kambili anthu amacitilana zopanda cilungamo cifukwa cosiyana mtundu, dziko, maonekedwe, cipembedzo, kapena mmene amaonela nkhani ya kugonana.
BAIBO IMATI: “Muzilemekeza anthu amitundu yonse.”—1 Petulo 2:17.
TANTHAUZO LAKE: Baibo sitilimbikitsa kuzonda anthu a mtundu wina kapena a dziko lina, kapenanso amene amacita mathanyula. Koma imatilimbikitsa kulemekeza anthu onse mosasamala kanthu za mtundu wawo na dziko lawo, kaya ni olemela kapena osauka. (Machitidwe 10:34) Ngakhale kuti sitigwilizana na zimene ena amakhulupilila kapena kucita, tiyenelabe kucita nawo zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu.—Mateyu 7:12.
MALANGIZO A M’BAIBO NI OTHANDIZA: Daniel anaphunzitsidwa kuti aziona anthu a ku Asia ngati adani a dziko lawo. Iye anayamba kudana na aliyense wocokela ku Asia, ndipo nthawi zambili anali kuŵatukwana akakumana nawo. Daniel anati, “N’nali kuona kuti kucita zimenezo ndiye ‘kulikonda dziko lathu’. Sin’naganizilepo kuti maganizo anga na zocita zanga zinali zolakwika.”
M’kupita kwa nthawi, Daniel anaphunzila zimene Baibo imanena. Iye anati: “N’nafunika kusintha kaganizidwe kanga. N’nafunika kuona anthu mmene Mulungu amaŵaonela. Kuona kuti tonse ndife amodzi mosasamala kanthu kuti kwathu n’kuti.” Daniel anafotokoza mmene amamvela tsopano akakumana na anthu. Iye anati: “Nthawi zambili siniganizilanso zakuti acokela kuti. Nimakonda anthu a mitundu yonse ndipo nili na mabwenzi a pamtima ocokela m’maiko osiyanasiyana.”
Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani Galamuka! ya Na. 3 2020, ya mutu wakuti “Kodi Pali Mankhwala Othetsela Tsankho?” pa jw.org.
3. Ndalama
Anthu ambili amafuna-funa cuma kuti akhale na cimwemwe komanso tsogolo labwino.
BAIBO IMATI: “Nzelu zimateteza mofanana ndi mmene ndalama zimatetezela. Koma ubwino wa kudziŵa zinthu ndi uwu: Nzelu zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeluzo.”—Mlaliki 7:12.
TANTHAUZO LAKE: Timafunika ndalama, koma sizingatigulile cimwemwe kapena tsogolo labwino. (Miyambo 18:11; 23:4, 5) Cimene cingatipatse cimwemwe ceniceni komanso tsogolo labwino ni kutsatila mfundo za Mulungu zopezeka m’Baibo.—1 Timoteyo 6:17-19.
MALANGIZO A M’BAIBO NI OTHANDIZA: Cardo, wa ku Indonesia, anayesetsa kudziunjikila cuma. Iye anati: “N’nali na zinthu zimene anthu ambili amalakalaka. N’nali kugula zinthu zodula, mamotoka, manyumba, komanso kupita kulikonse kumene nafuna. Koma cuma cimeneci sicinakhalitse.” Cardo anawonjezela kuti: “Cuma canga conse cinabedwa, ndipo m’kanthawi kocepa zinthu zonse zimene n’nakhetsela thukuta kwa zaka zambili zinapita. N’nagwila nchito molimbika kwa moyo wanga wonse kuti nilemele. Koma pamapeto pake n’nagwilitsidwa mwala cifukwa n’nalibe ciliconse ndipo n’nali kudziona wacabe-cabe.”
Cardo anayamba kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo pa nkhani ya ndalama. Iye analeka kuika maganizo ake pa kudziunjikila cuma, ndipo ali na umoyo wosalila zambili.” Ananenanso kuti: “Cuma ceniceni komanso cokhalitsa n’cauzimu. Nimagona tulo twabwino usiku ulionse ndipo nili na cimwemwe ceniceni.”
Kuti mudziŵe zambili zimene Baibo imakamba pa nkhani ya ndalama, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni kukhala na Tsogolo Labwino?” mu Nsanja ya Mlonda ya Na. 3 2021, pa jw.org.
4. Kugonana
Anthu ali na maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya kugonana.
BAIBO IMATI: “Muzipewa ciwelewele. Aliyense wa inu azidziŵa kulamulila thupi lake kuti likhale loyela komanso lolemekezeka pamaso pa Mulungu. Musakhale ngati anthu a mitundu ina omwe sadziŵa Mulungu komanso ali ndi cilakolako cosalamulilika ca kugonana ndipo sakhutilitsidwa.”—1 Atesalonika 4:3-5.
TANTHAUZO LAKE: Baibo inaika malile pa nkhani ya kugonana. Mawu akuti “ciwelewele” amaphatikizapo cigololo, uhule, kugonana kwa anthu osakwatilana, mathanyula, komanso kugona nyama. (1 Akorinto 6:9, 10) Kugonana ni mphatso yocokela kwa Mulungu, imene anaipeleka cabe kwa mwamuna na mkazi okwatilana.—Miyambo 5:18, 19.
MALANGIZO A M’BAIBO NI OTHANDIZA: Mzimayi wina wa ku Australia dzina lake Kylie anati: “Pamene n’nali mbeta, n’nali kuganiza kuti nikagonana na munthu wina m’pamene nidzaona kuti nimakondedwa ndipo ndine wotetezeka. Koma n’tacita zimenezo, m’pamene n’nadzimva wosatetezeka ndipo zinanipweteka mumtima.”
Pambuyo pake, Kylie anaphunzila malangizo a m’Baibo pa nkhani ya kugonana n’kuyamba kuwagwilitsa nchito. Iye anati: “Nadziŵa kuti malamulo a Mulungu amatiteteza ku zinthu zimene zingatibweletsele mavuto. Lomba ndine wotetezeka komanso wokondedwa cifukwa nimacita zinthu m’njila imene Yehova amafuna. Kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo kwaniteteza ku zinthu zambili!”
Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limavomeleza Kuti Mwamuna Ndi Mkazi Azikhalila Limodzi Asanakwatilane?” pa jw.org.
Mlengi wathu amatithandiza kudziŵa coyenela na cosayenela. Ngakhale kuti nthawi zina zimativuta kutsatila malangizo ake, timapindula tikamayesetsa kuwatsatila. Timakhala na cimwemwe cokhalitsa.