LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 February masa. 28-29
  • Ziwalo Ziŵili Zatsopano za Bungwe Lolamulila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ziwalo Ziŵili Zatsopano za Bungwe Lolamulila
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Nkhani Zofanana
  • Ciwalo Catsopano ca Bungwe Lolamulila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kodi Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova N’ciyani?
    Mafunso Ofunsidwa Kaŵili-kaŵili pa Mboni za Yehova
  • Ziwalo Ziwili Zatsopano za Bungwe Lolamulila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Nchito Zabwino Zimene Sizidzaiŵalidwa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 February masa. 28-29

Ziwalo Ziŵili Zatsopano za Bungwe Lolamulila

PA CITATU, January 18, 2023, cilengezo capadela cinaonekela pa jw.org. Cilengezoci cinali cakuti M’bale Gage Fleegle na M’bale Jeffrey Winder aikidwa kukhala ziwalo zatsopano za Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Abale onse aŵili ali na mbili yakuti atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili.

M’bale Gage Fleegle na mkazi wake Nadia

M’bale Fleegle anakulila kumadzulo kwa mzinda wa Pennsylvania, m’dziko la America, ndipo analeledwa na makolo ake m’coonadi. Ali wacinyamata, banja lawo linasamukila kudela laling’ono la kumudzi komwe kunali kufunikila olalikila ambili. Posakhalitsa, iye anabatizika pa November 20, 1988.

Makolo a M’bale Fleegle nthawi zonse anali kumulimbikitsa kuti aloŵe utumiki wa nthawi zonse. Banja lawo nthawi zambili linali kulandilako oyang’anila madela, komanso atumiki a pa Beteli ku nyumba kwawo. Ndipo M’bale Fleegle anali kuona cimwemwe cimene abale na alongo amenewa anali naco. Patapita kanthawi kocepa atabatizika, anayamba upainiya wa nthawi zonse—pa September 1, 1989. Patapita zaka ziŵili, iye anakwanilitsa colinga cake cimene anadziikila ali na zaka 12—colinga cokatumikila pa Beteli. Anayamba utumiki wake pa Beteli ya ku Brooklyn mu October 1991.

M’bale Jeffrey Winder na mkazi wake Angela

Pa Beteli, M’bale Fleegle anaseŵenzela ku dipatimenti yopanga mabuku kwa zaka 8, pambuyo pake anasamutsidwa kupita ku Dipatimenti ya Utumiki. Pa nthawi imeneyo anali kutumikila mu mpingo wa cinenelo ca manja ca ku Russia, ndipo anatumikilamo kwa zaka zingapo. Mu 2006 iye anakwatila Nadia, ndipo anayamba kutumikila pamodzi pa Beteli. Atumikila capamodzi m’gawo la Cipwitikizi, ndipo kwa zaka zoposa 10 atumikila m’gawo la Cisipanishi. M’bale Fleegle atatumikila zaka zambili m’Dipatimenti ya Utumiki, anayamba kutumikila mu Ofesi ya Komiti Yophunzitsa. Ndipo pambuyo pake anayamba kutumikila mu Ofesi ya Komiti ya Utumiki. Mu March 2022 iye anaikidwa kukhala wothandiza Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila.

M’bale Winder anakulila ku America mumzinda wa Murrieta, ku California. Iye analeledwa na makolo ake m’coonadi, ndipo anabatizika pa March 29, 1986. M’mwezi wotsatila, iye anacitako upainiya wothandiza. Anasangalala nawo kwambili cakuti sanafune kuleka. Pambuyo pa miyezi ingapo akucita upainiya wothandiza, anayamba upainiya wa nthawi zonse pa October 1, 1986.

Ali wacinyamata, M’bale Winder anapita kukaona abale ake aŵili omwe anali kutumikila pa Beteli pa nthawiyo. Ulendowo unamulimbikitsa kuti adziikile colinga cokatumikila pa Beteli akakula. Ndipo mu May 1990, iye anaitanidwa kukatumikila pa Beteli ya ku Wallkill.

M’bale Winder atumikilapo m‘madipatimenti osiyana-siyana pa Beteli, kuphatikizapo m’Dipatimenti ya Zaukhondo, Dipatimenti ya Zaulimi, komanso mu Ofesi ya Beteli. Anakwatila mkazi wake Angela mu 1997, ndipo onse aŵili akhala akutumikila pa Beteli kucokela nthawi imeneyo. Mu 2014 iwo anasamutsidwila ku Warwick, komwe M’bale Winder anathandiza pomanga likulu la pa dziko lonse. Mu 2016 anasamutsidwila ku Likulu la Maphunzilo la Watchtower ku Patterson. Kumeneko, iye anayamba kuseŵenzela m’Dipatimenti Yoona Zomvetsela na Mavidiyo. Pambuyo pa zaka 4, iwo anabwelelanso ku Warwick, ndipo M’bale Winder anayamba kuseŵenzela mu Ofesi ya Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli. Mu March 2022 iye anaikidwa kukhala wothandiza Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli ya Bungwe Lolamulila.

Pemphelo lathu n’lakuti Yehova adalitse “mphatso za amuna” zimenezi, pomwe akupitiliza kutumikila kaamba ka Ufumu.—Aef. 4:8.

Tsopano m’Bungwe Lolamulila muli abale 9 odzozedwa. Maina awo ni aya: Kenneth Cook, Jr.; Gage Fleegle; Samuel Herd; Geoffrey Jackson; Stephen Lett; Gerrit Lösch; Mark Sanderson; David Splane; na Jeffrey Winder.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani