NKHANI YOPHUNZILA 18
NYIMBO 1 Makhalidwe a Yehova
Khulupililani Woweluza Wacifundo “wa Dziko Lonse Lapansi”!
“Kodi Woweluza wa dziko lonse lapansi sadzacita colungama?”—GEN. 18:25.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Kumvetsa zowonjezeleka pa cifundo na cilungamo ca Yehova pa nkhani ya kuukitsa anthu osalungama.
1. Ni phunzilo lokhazika mtima pansi liti limene Yehova anaphunzitsa Abulahamu?
ANALI makambilano amene Abulahamu sanawaiŵale. Mulungu anauza Abulahamu kupitila mwa mngelo kuti adzafafaniza mizinda ya Sodomu na Gomora. Munthu wokhulupilika ameneyu anada nkhawa. Conco anafunsa kuti: “Kodi zoona mungawononge olungama pamodzi ndi oipa? . . . Kodi Woweluza wa dziko lonse lapansi sadzacita colungama?” Yehova anaphunzitsa bwenzi lake moleza mtima phunzilo limene limatipindulila tonsefe na kutikhazika mtima pansi lakuti: Mulungu sangawononge anthu olungama.—Gen. 18:23, 25-33.
2. N’ciyani cimatitsimikizila kuti Yehova amaweluza molungama komanso mwacifundo?
2 N’ciyani cimatitsimikizila kuti Yehova amaŵeluza molungama komanso mwacifundo? Cifukwa tidziŵa kuti “Yehova amaona mumtima” wa munthu. (1 Sam. 16:7) Ndipo amadziŵa bwino “mtima wa munthu aliyense.” (1 Maf. 8:39; 1 Mbiri 28:9) Iyi ni mfundo yoonadi yocititsa cidwi. Ziweluzo za Yehova n’zakuya kwambili moti sitingazimvetsetse. M’pake kuti mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba izi ponena za Yehova: “Ziweluzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukile njila zake?”—Aroma 11:33.
3-4. Kodi nthawi zina tingadzifunse mafunso ati? Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino? (Yohane 5:28, 29)
3 Ngakhale n’telo, tingakhalebe na mafunso monga amene Abulahamu anafunsa. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi anthu amene Yehova anawawononga, monga a ku Sodomu na Gomora angadzakhalenso na ciyembekezo? Kodi ena a iwo ‘angadzaukitsidwe pa kuuka kwa osalungama’?’—Mac. 24:15.
4 Tiyeni tiunikenso zimene tidziŵa pa nkhani ya ciukitso. Caposacedwa tinalandila kamvedwe katsopano ponena za amene ‘adzauka kuti adzalandile moyo,’ komanso amene ‘adzauka kuti adzaweluzidwe.’a (Ŵelengani Yohane 5:28, 29.) Kamvedwe katsopano kameneka kacititsa kuti pakhale masinthidwe ena amene afotokozedwe m’nkhani ino komanso yotsatila. M’nkhani ino, coyamba tikambilane zimene sitidziŵa ponena za ziweluzo za Yehova zolungama, kenako tikambilane zimene tidziŵa zokhudza ziweluzo zake.
ZIMENE SITIDZIŴA
5. Kodi zofalitsa zathu zakale zinali kunena ciyani ponena za anthu amene anawonongedwa mu Sodomu na Gomora?
5 Zofalitsa zathu za kumbuyoku zinafotokozapo zimene zimacitikila anthu omwe Yehova waaweluza kuti ni osalungama. Tinali kufotokoza kuti anthu ngati a ku Sodomu na Gomora, alibe ciyembekezo codzakhalanso na moyo. Koma titasanthula nkhaniyi mwapemphelo, panabuka funso lakuti, Kodi tinganenedi zimenezi mwatsimitsimi?
6. Chulan’koni zitsanzo za ziweluzo za Yehova pa anthu osalungama. Nanga n’ciyani cimene sitidziŵa pa ziweluzo zimenezi?
6 Ganizilani zocitika za ngati cocitika ca mu Sodomu na Gomora. Nkhani zosiyana-siyana za m’Baibo zimafotokoza ziweluzo za Yehova pa anthu osalungama. Mwa citsanzo, imachulapo za kuwonongedwa kwa anthu osadziŵika ciŵelengelo pa Cigumula, komanso mitundu 7 imene Yehova analamula anthu ake kuti aiwononge yomwe inali kukhala m’Dziko Lolonjezedwa. Imachulanso za asilikali a Asuri 185,000 omwe anaphedwa na mngelo mmodzi wa Yehova usiku umodzi cabe. (Gen. 7:23; Deut. 7:1-3; Yes. 37:36, 37) Pa zocitika izi, kodi Baibo imatipatsa mfundo zokwanila zotithandiza kudziŵa ngati Yehova anapatsa anthu amenewa ciweluzo cothelatu, moti alibenso ciyembekezo codzakhalanso na moyo? Iyayi. Tikutelo cifukwa ciyani?
7. N’ciyani cimene sitidziŵa ponena za anthu omwe anawonongedwa pa Cigumula, komanso pamene dziko la Kanani linagonjetsedwa? (Onani cithunzi ca pacikuto.)
7 Sitidziŵa mmene Yehova anaweluzila munthu aliyense payekha-payekha; kapena ngati anthu amene anaphedwa anali na mwayi wophunzila za Yehova kuti alape. Ponena za nthawi ya Cigumula, Baibo imanena kuti Nowa anali “mlaliki wa cilungamo.” (2 Pet. 2:5) Koma siikamba kuti pamene anali kukhoma cingalawa analinso na colinga cofikila munthu aliyense pa dziko lapansi kuti amulalikile. Mofananamo, ponena za anthu oipa a ku Kanani sitidziŵa ngati onsewo anakhala na mwayi wophunzila za Yehova kuti asinthe njila zawo.
Nowa na banja lake akukhoma cingalawa. Sizidziŵika ngati Nowa anapanga makonzedwe a ulaliki akuti afikile anthu onse padziko lapansi pomwe anali kukhoma cingalawa Cigumula cisanafike (Onani ndime 7)
8. Sitidziŵa ciyani ponena za anthu a ku Sodomu na Gomora?
8 Bwanji za anthu a ku Sodomu na Gomora? Munthu wokhulupilika dzina lake Loti anali kukhala pakati pawo. Koma kodi tinganene motsimikiza kuti Loti anawalalikila onsewo? Ayi. N’zoona kuti iwo anali oipa, koma kodi anali kutha kusiyanitsa cabwino na coipa? Kumbukilani kuti cigulu ca amuna a mumzindawo cinafuna kugwilila alendo omwe anabwela kwa Loti. Baibo imanena kuti “pacigulupo panali anyamata komanso acikulile.” (Gen. 19:4; 2 Pet. 2:7) Kodi tinganenedi mwatsimitsimi kuti Mulungu wacifundo, Yehova, anawaweluza onsewo popanda ciyembekezo cakuti angadzaukitsidwe? Yehova anatsimikizila Abulahamu kuti anthu olungama mu mzindawo sanali kufika ngakhale 10. (Gen. 18:32) Iwo anali osalungama, m’pake kuti Yehova anawaweluza kuti awonongedwe cifukwa ca zocita zawo. Koma kodi tinganene motsimikiza kuti palibe aliyense wa iwo amene adzaukitsidwa pamene “Mulungu adzaukitsa . . . osalungama”? Ayi, sitingatelo mwatsimitsimi!
9. Kodi sitidziŵa ciyani ponena za Solomo?
9 Kumbali ina, timaŵelenganso m’Baibo za anthu amene anali olungama, amene kenako anadzakhala osalungama. Citsanzo ni Mfumu Solomo. Iye anaphunzitsidwa bwino njila za Mulungu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambili. Koma pambuyo pake anayamba kulambila milungu yonyenga. Macimo ake anamukhumudwitsa ngako Yehova, ndipo anabweletsa mavuto ambili pa mtundu wa Isiraeli kwa zaka mahandiledi. N’zoona kuti Malemba amanena kuti Solomo atamwalila “anagona pamodzi ndi makolo ake,” kuphatikizapo amuna okhulupilika monga Mfumu Davide. (1 Maf. 11:5-9, 43; 2 Maf. 23:13) Koma kodi izi zitipatsa citsimikizo cakuti adzaukitsidwa? Baibo siifotokoza. Koma ena anganene kuti “munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu wa macimo ake.” (Aroma 6:7) Zimenezi n’zoona, koma sizitanthauza kuti aliyense amene anamwalila adzaukitsidwa. Kuteloko kungatanthauze kuti kumwalila ni njila inanso yokapezela moyo m’dziko latsopano. Koma ciukitso ni mphatso yocokela kwa Mlengi wacikondi. Ndipo amangoipeleka kwa anthu omwe iye akufuna kuti am’tumikile kwamuyaya. (Yobu 14:13, 14; Yoh. 6:44) Kodi Solomo adzalandilako mphatso imeneyi? Yehova ndiye adziŵa, ife sitidziŵa. Cimene tidziŵa n’cakuti, Yehova adzacita cilungamo.
ZIMENE TIDZIŴA
10. Kodi Yehova amamva bwanji akaganizila zowononga anthu? (Ezekieli 33:11) (Onaninso cithunzi)
10 Ŵelengani Ezekieli 33:11. Mokoma mtima, Yehova amatiuza mmene amamvela poweluza anthu. Mtumwi Petulo mouzilidwa anagwila mawu amene mneneli Ezekieli analemba akuti, “Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.” (2 Pet. 3:9) Mfundo yazoona imeneyi imatitonthoza. Tidziŵa kuti Yehova safulumila kuwonongeletu anthu kwamuyaya pokhapo ngati pali cifukwa cocitila zimenezo. Iye ni wacifundo cacikulu, ndipo amacionetsa pakakhala pofunikila.
Pa kuuka kwa anthu osalungama, anthu osiyana-siyana adzakhala na mwayi wophunzila za Yehova (Onani ndime 10)
11. Kodi ndani amene sadzaukitsidwa? Nanga tidziŵa bwanji zimenezi?
11 Tidziŵa zotani ponena za anthu amene sadzaukitsidwa? Baibo imachula zitsanzo za anthu ocepa cabe amene sadzaukitsidwa.b Yesu anaonetsa kuti Yudasi Isikariyoti sadzaukitsidwa. (Maliko 14:21; Onaninso Yoh. 17:12.) Yudasi anali kudziŵa kuti zimene anali kucita zinali zosemphana na Yehova komanso Mwana Wake. Koma mwadala anasankha kuzicita. Mofananamo, Yesu ananena kuti atsogoleli azipembedzo amene anali kumutsutsa adzafa opanda ciyembekezo. (Mat. 23:33; onani Yoh. 19:11.) Nayenso mtumwi Paulo anacenjeza ampatuko osalapa kuti sadzaukitsidwa.—Aheb. 6:4-8; 10:29.
12. Tidziŵa ciyani za mmene Yehova amaonetsela cifundo cake? Fotokozani zitsanzo.
12 Nanga tidziŵa ciyani ponena za cifundo ca Yehova? Kodi iye waonetsa bwanji kuti “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe”? Ganizilani mmene anaonetsela cifundo cake kwa anthu amene anacitapo macimo akulu-akulu. Mfumu Davide anacitapo macimo akulu-akulu, kuphatikizapo cigololo komanso kupha munthu. Komabe Davide analapa, ndipo Yehova anam’khululukila. (2 Sam. 12:1-13) Mfumu Manase nayenso anacita zinthu zoipa kwambili kwa nthawi yaikulu ya moyo wake. Ngakhale kuti Manase anacita zoipa zambili, iye analapa ndipo Yehova anamucitila cifundo na kum’khululukila. (2 Mbiri 33:9-16) Zitsanzo zimenezi zitikumbutsa kuti Yehova amacita cifundo pakakhala cifukwa cocitila zimenezi. Iye adzaukitsa anthu ngati amenewa cifukwa iwo anazindikila kuti anacita macimo aakulu ndipo analapa.
13. (a) N’cifukwa ciyani Yehova anawacitila cifundo Anineve? (b) Kodi Yesu anati ciyani pambuyo pake za Anineve?
13 Tidziŵanso kuti Yehova anacitila cifundo anthu a ku Nineve. Iye anauza Yona kuti: “Ndaona zoipa zimene akucita.” Koma pamene analapa macimo awo, Yehova anawakhululukila mokoma mtima. Iye anaonetsa cifundo cacikulu kuposa Yona. Mulungu anakumbutsa mneneli wake wokhumudwa ameneyo kuti anthu a ku Nineve “sadziŵa kusiyanitsa zoyenela ndi zolakwika.” (Yona 1:1, 2; 3:10; 4:9-11) Pambuyo pake, Yesu anaseŵenzetsa citsanzo ca Anineve pofotokoza cilungamo ca Yehova na cifundo cake. Yesu ananena kuti cifukwa cakuti Anineve analapa “adzauka pa Tsiku la Ciweluzo.”—Mat. 12:41.
14. Kodi Anineve “adzauka kuti aweluzidwe” m’lingalilo lotani?
14 Kodi Anineve “adzauka” kuti ‘akaweluzidwe’ m’lingalilo lotani? Yesu anaphunzitsa kuti anthu m’tsogolo ‘adzauka kuti adzaweluzidwe.’ (Yoh. 5:29) Anali kunena za ulamulilo wake wa Zaka 1,000, pomwe “olungama ndi osalungama omwe” adzaukitsidwa. (Mac. 24:15) Osalungama, ‘adzauka kuti adzaweluzidwe.’ Izi zitanthauza kuti Yehova na Yesu azidzayang’anila zocita zawo, na kuona ngati iwo akulabadila zimene akuphunzitsidwa na kuzigwilitsa nchito. Ngati Mnineve wakana kulambila koona adzaweluzidwa kuti awonongedwe kothelatu. (Yes. 65:20) Koma awo amene adzasankha kulambila Yehova mokhulupilika, adzaweluzidwa kuti adzakhale na moyo wosatha!—Dan. 12:2.
15. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa kunena kuti anthu amene anawonongedwa mu mizinda ya Sodomu na Gomora palibe amene adzaukitsidwe? (b) Kodi tiyenela kuwamvetsa motani mawu a pa Yuda 7? (Onani danga lakuti “Kodi Yuda Anatanthauza Ciyani?”)
15 Yesu ananena kuti anthu a ku Sodomu na Gomora, zinthu zidzawayendelako bwino “pa Tsiku la Ciweluzo” kuposa anthu a m’nthawi yake amene anamukana na kukana ziphunzitso zake. (Mat. 10:14, 15; 11:23, 24; Luka 10:12) Kodi anatanthauzanji? Tingaganize kuti apa Yesu anayelekezela mokokomeza, koma sitelo ayi. N’cimodzimodzinso pamene anakamba za Anineve, sanali kungophiphilitsa ayi. Yesu anatanthauzadi zimene ananenazo. “Tsiku la Ciweluzo” limene Yesu ananena pa zocitika zonse ziŵilizi ni limodzimodzi. Monga zinalili kwa Anineve, anthu a ku Sodomu na Gomora nawonso anali kucita zoipa. Koma anthu a ku Nineve anapatsidwa mpata wolapa. Kuwonjezela apo, kumbukilani zimene Yesu anakamba za anthu amene “adzauka kuti aweluzidwe.” Anthuwo akuphatikizapo “amene ankacita zoipa.” (Yoh. 5:29) Conco zikuoneka kuti ciyembekezo cingakhalepo cakuti anthu a ku Sodomu na Gomora nawonso angadzaukitsidwe. Pali kuthekela kwakuti ena mwa anthu amenewo angadzaukitsidwe, ndipo tingadzakhale na mwayi wodzawaphunzitsa za Yehova na Yesu Khristu.
16. Kodi Yehova adzasankha motani anthu oyenela kuwaukitsa? (Yeremiya 17:10)
16 Ŵelengani Yeremiya 17:10. Vesi iyi imatithandiza kumvetsa zimene tikudziŵa kale zokhudza Yehova: Iye nthawi zonse amafufuza “maganizo a mkati mwa mtima wa munthu.” Podzaukitsa anthu m’tsogolo, monga mwa nthawi zonse, ‘munthu aliyense adzamucitila zinthu mogwilizana ndi zipatso za nchito zake.’ Yehova adzaweluza mosayang’ana nkhope, koma adzaweluzanso mwacifundo kwa oyenelela cifundo cake. Conco, tisamanene kuti uje sadzaukitsidwa, ngati Baibo sinakambe zimenezo!
“WOWELUZA WA DZIKO LONSE LAPANSI” ADZACITA COLUNGAMA
17. Kodi tsogolo la anthu omwe anamwalila n’lotani?
17 Kungoyambila pamene Adamu na Hava anagwilizana na Satana popandukila ulamulilo wa Yehova Mulungu, anthu mabiliyoni amwalila. Mdani wathuyo, “imfa,” wakokolola miyoyo yambilimbili! (1 Akor. 15:26) Kodi tsogolo la anthu onsewo n’lotani? Kagulu kocepa ka otsatila a Khristu okhulupilika okwanila 144,000 kadzaukitsidwila ku moyo wosafa kumwamba. (Chiv. 14:1) Koma anthu oculuka amene anali kukonda Yehova, adzaukitsidwa pamene Yehova “adzaukitsa olungama.” Ndipo iwo adzalandila moyo wosatha padziko lapansi akadzakhalabe okhulupilika mu ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000 komanso pa mayeso othela. (Dan. 12:13; Ahe. 12:1) Ndipo mu ulamulilo wa Zaka Cikwi, “osalungama”—kuphatikizapo omwe sanatumikilepo Yehova, ngakhale “amene ankacita zoipa”—adzapatsidwa mwayi wosintha njila zawo na kukhala okhulupilika. (Luka 23:42, 43) Komabe, anthu ena amakhala oipa zedi moti amam’pandukila mwadala Yehova na cifunilo cake. Anthu otelowo akamwalila, Yehova anaweluzilatu kuti sadzaukitsidwa.—Luka 12:4, 5.
18-19. (a) N’cifukwa ciyani sitikaika kuti Yehova adzaweluza moyenela anthu amene anamwalila? (Yesaya 55:8, 9) (b) Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?
18 Kodi ndife otsimikiza kuti Yehova nthawi zonse amaweluza anthu mwacilungamo? Inde! Abulahamu anamvetsa bwino kuti Yehova ni “Woweluza wa dziko lonse lapansi,” amene ni wangwilo, wanzelu zakuya, komanso wacifundo. Mulungu anaphunzitsa Mwana wake kuweluza, ndipo anam’patsa mphamvu zoweluza munthu aliyense. (Yoh. 5:22) Onse aŵili, Atate na Mwana, amatha kudziŵa za mumtima wa munthu aliyense. (Mat. 9:4) Conco, poweluza munthu aliyense, iwo ‘adzacita colungama’!
19 Tiyeni tonse tikhulupilile na mtima wonse kuti kaweluzidwe ka Yehova n’kolungama. Tikuvomeleza kuti kuweluza si kwathu—n’kwa Yehova! (Ŵelengani Yesaya 55:8, 9.) Conco na cidalilo conse, timasiya kuweluza konse m’manja mwake na Mwana wake, amene ni Mfumu yotengela cilungamo na cifundo ca Atate wake. (Yes. 11:3, 4) Nanga bwanji za mmene Yehova na Yesu adzaweluzile anthu pa cisautso cacikulu? N’ciyani cimene Sitidziŵa pa nkhaniyi? Nanga n’ciyani cimene tidziŵa? Tidzakambilana mafunso amenewa m’nkhani yotsatila.
NYIMBO 57 Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse
b Za ciyembekezo ca Adamu, Hava, komanso Kaini, onani mawu a m’munsi mu Nsanja ya Mlonda ya January 1, 2013, tsamba 12.