LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 2 masa. 8-9
  • 2. Kodi Ife Eni Ndiye Timapangitsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 2. Kodi Ife Eni Ndiye Timapangitsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho
  • Zofunika Kuganizila
  • Zimene Baibo Imakamba
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Zamkati
    Galamuka!—2020
  • 4. Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?
    Galamuka!—2020
  • 1. Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?
    Galamuka!—2020
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 2 masa. 8-9
Munthu ali m’cipinda cake cocezela ndipo ali na ndudu kumanja, pamene kudzanja lina wanyamula botolo la moŵa.

2. Kodi Ife Eni Ndiye Timapangitsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Ngati yankho ni inde, ndiye kuti ungakhale udindo wathu kucepetsako mavuto.

Zofunika Kuganizila

Kodi anthu apangitsa mavuto otsatilawa kufika pa mlingo uti?

  • Kacithunzi koonetsa munthu waunga khofi, kuimila nkhanza.

    Nkhanza.

    Bungwe la World Health Organization (WHO) limakamba kuti pa anthu 4, mmodzi anacitilidwapo nkhanza ali mwana. Ndipo pa azimai atatu, mmodzi anamenyedwapo kapena kugonedwa mwacikakamizo, mwinanso zonse ziŵili pa nthawi ina mu umoyo wawo.

  • Kacithunzi koonetsa zipilala, kuimila kumanda.

    Cisoni Cobwela Cifukwa ca Imfa.

    Lipoti la mu 2018 lochedwa World Health Statistics lofalitsidwa na bungwe la World Health Organization linati “anthu pafupi-fupi 477,000 anaphedwa padziko lonse mu 2016.” Kuwonjezela apo, anthu pafupi-fupi 180,000 zioneka anaphedwa pa nkhondo zimene zinacitika mu caka cimeneco.

  • Kacithunzi koonetsa mzele wa mmene mtima ukugundila, kuimila matenda.

    Matenda.

    M’nkhani yofalitsidwa m’magazini yakuti National Geographic, wolemba wina dzina lake Fran Smith anati: “Anthu oposa 1 biliyoni amakoka fodya, ndipo kaŵili-kaŵili fodya ndiye amabweletsa matenda akulu-akulu 5 akupha, monga matenda a mtima, sitroko, matenda otengela mu mphepo, matenda ovutika kupuma, komanso khansa ya kumapapo.”

  • Kacithunzi koonetsa sikelo yolemelela mbali imodzi, kuimila kusiyana cifukwa ca tsankho.

    Tsankho

    Jay Watts amene ni katswili wa zamaganizo anati: “Umphawi, kusiyana pa kapezedwe, kusankhana cifukwa cosiyana mitundu, cifukwa cokhala mkazi kapena mwamuna, kukakamizika kucoka kumalo kumene munthu amakhala, komanso mzimu wa mpikisano, zonsezi zimapangitsa anthu kuvutika maganizo kwambili.”

    DZIŴANI ZAMBILI

    Tambani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? pa jw.org

Zimene Baibo Imakamba

Munthu amene waonetsedwa poyamba, ali pabedi m’cipatala. Mkazi wake ayang’ana kumbali pamene dokotala aŵauza uthenga woipa wokhudza thanzi la amuna ake.

Mavuto ambili m’dzikoli amabwela cifukwa ca zocita za anthu.

Ambili mwa mavutowa amabwela cifukwa ca maboma opondeleza, ndipo izi zimapangitsa kuti umoyo ukhale wovuta kwa anthu amene maboma amenewo amati amaŵatumikila.

“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”—MLALIKI 8:9.

Mavuto angacepetsedwe.

Mfundo za m’Baibo zimalimbikitsa anthu kukhala na thanzi labwino komanso kukhala pa mtendele na ena.

“Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu, koma nsanje imawoletsa mafupa.”—MIYAMBO 14:30.

“Kuwawidwa mtima konse kwa njilu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu acipongwe zicotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” —AEFESO 4:31.

Kodi ife eni ndiye timapangitsa mavuto amene timakumana nawo?

Baibo imati: “Cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.” (Agalatiya 6:7) Mavuto ena amabwela cifukwa ca zosankha zathu. Ndiye cifukwa cake madokotala amalimbikitsa anthu kuti azidya zakudya zopatsa thanzi, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kupewa makhalidwe owononga monga kukoka fodya. Ngakhale n’telo, kungakhale kulakwitsa kukamba kuti anthu ndiye amapangitsa mavuto onse. Anthu ambili osalakwa amapezeka m’ngozi, kukumana na matsoka, komanso mavuto ena aakulu.

N’cifukwa ciani anthu abwino nawonso amavutika?

Onani funso 3.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani