LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 3 masa. 6-7
  • Onetsani Cifundo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onetsani Cifundo
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta
  • Mfundo ya m’Baibo
  • Kodi Cifundo Cimathandiza Bwanji?
  • Zimene Mungacite
  • Onetsani Cifundo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Umoyo wa Banja Komanso Mabwenzi
    Galamuka!—2019
  • Kunola Luso lathu mu Ulaliki—Kulankhula za Ufumu Molimba Mtima
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 3 masa. 6-7
Munthu wa ci Caucasian na wa ci Sikh akhala moyandikana m’ndeke. Iwo akukambilana mwacimwemwe.

Onetsani Cifundo

Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta

Ngati timakonda kuganizila mmene ena alili osiyana na ife, tingayambe kuwaona ngati ali na vuto. Ndiponso tingayambe kuona kuti anthu amene ni osiyana na ise ni otsalila. Tikakhala na maganizo aconco, cimakhala covuta kuwaonetsa cifundo anthu otelo. Kusoŵa cifundo kumeneko kungakhale cizindikilo cakuti tili na vuto lalikulu—tsankho.

Mfundo ya m’Baibo

“Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lilani ndi anthu amene akulila.” —AROMA 12:15.

Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? Mfundo imeneyi itiphunzitsa kuti tifunika kuonetsa cifundo kwa ena. Cifundo ni khalidwe lotha kuganizila mmene munthu wina amvelela, komanso mmene ife tikanamvelela sembe tinali munthu ameneyo.

Kodi Cifundo Cimathandiza Bwanji?

Tikamaonetsa cifundo kwa munthu, timayamba kuzindikila kuti ndife ofanana naye m’njila zambili. Tingazindikile kuti iye amamvela na kucita zinthu monga mmene ifenso timacitila. Cifundo cimatithandiza kuona kuti anthu onse, kaya ni a mtundu wotani, ni banja limodzi. Ngati tiganizila kwambili kufanana kumene kulipo pakati pa anthu ena na ife, timayamba kuwaona moyenela anthuwo.

Cifundo cimatithandizanso kuti tizilemekeza ena. Mwacitsanzo, ganizilani za Anne-Marie wa ku Senegal. M’dziko lawo muli mtundu wina wa anthu amene ambili amawaona kuti ni otsika. Nayenso Anne-Marie anali kuwaona kuti ni otsika anthu amenewo. Koma anafotokoza mmene cifundo cinam’thandizila kuthetsa vutoli. Anati: “Pamene n’naona mavuto amene anthu a mtundu umenewo anali kukumana nawo, n’nayamba kuganizila mmene ine nikanamvelela sembe n’nali wa mtundu umenewo. Izi zinanithandiza kuzindikila kuti sindine wapamwamba kuposa iwo, komanso kuti palibe ciliconse cimene n’nacita conipangitsa kukhala wapamwamba kuposa iwo.” Zoonadi, ngati tiyesetsa kumvetsetsa mavuto amene ena amakumana nawo, tidzawamvelela cifundo ndiponso tidzapewa kuwakambila zoipa.

Zimene Mungacite

Ngati anthu a mtundu winawake mumawaona molakwika, yesetsani kuganizila zinthu zimene imwe na iwo mumafanana. Mwacitsanzo, ganizilani mmene iwo amamvelela:

Cifundo cimatithandiza kuona kuti anthu onse ni banja limodzi

  • pamene akudya cakudya pamodzi na banja lawo

  • akakomboka kunchito pambuyo pogwila nchito yolemetsa

  • pamene aceza na anzawo

  • pamene amvetsela nyimbo zimene amakonda

Ndiyeno, yesetsani kuganizila mmene mukanamvelela sembe munali iwo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi ningamvele bwanji ngati wina wakamba mawu kapena kucita zinthu zonipangitsa kudziona wosafunika?’

  • ‘Ningamvele bwanji ngati ena aninena kuti ndine woipa pamene akalibe kunidziŵa bwino?’

  • ‘Kodi nikanakhala mmodzi wa iwo, sembe nifuna kuti anthu ena azicita nane zinthu motani?’

Anthu amodzi-modziwo akuonetsana mapikica a zinthu zimene onse amakonda monga mabanja awo, maseŵela amene amakonda, na nchito imene amagwila.

Citsanzo ca Zocitika Zeni-Zeni: Robert wa ku (Singapore)

“Kale n’nali kuona kuti anthu ogontha amacita zinthu mwacilendo, ni opanda nzelu, komanso ni a mtima wapacala. Conco n’nali kuwapewa. Komabe, n’nali kudziona kuti nilibe tsankho.

“Kumvelela cifundo anthu ogontha kunanithandiza kuthetsa tsankho limenelo. Mwacitsanzo, n’nali kuganiza kuti anthu ogontha si anzelu kweni-kweni cifukwa nikakamba nawo, anali kungoniyang’ana monga saikilako nzelu. Conco n’nayamba kuganizila mmene nikanamvelela kuti na ine n’nali wogontha. N’nazindikila kuti na ine nkhope yanga sembe ioneka monga siniikilako nzelu zokamba za ena. Olo nikanakhala na cipangizo cothandizila kumva, nkhope yanga sembe ioneka monga nikamba kuti, ‘Sinikumvetsetsa,’ pamene m’ceni-ceni nikulephela kumvela zokambazo.

“Pamene n’nayesetsa kuganizila mmene nikanamvelela nikanakhala wogontha, maganizo anga a tsankho anathelatu.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani