LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 July tsa. 3
  • Onetsani Cifundo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onetsani Cifundo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Onetsani Cifundo
    Galamuka!—2020
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Afikeni Pamtima Anthu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 July tsa. 3

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Onetsani Cifundo

Cifundo cimatanthauza kumvetsetsa mmene ena amaganizila, mmene amamvelela, zimene amakonda, na zimene amafunikila. N’zosavuta anthu ena kudziŵa ngati timawamvela cifundo. Mtima wofunadi kuthandiza ena ndiwo umatisonkhezela kuwaonetsa cifundo. Tikamaonetsa cifundo mu ulaliki, timatengela khalidwe la Yehova la cikondi komanso lodela nkhawa ena, ndipo izi zimawasonkhezela kufuna kuphunzila za iye.—Afil. 2:4.

Tisamaonetse cifundo na colinga cofuna cabe kuphunzitsa munthu. Timaonetsa cifundo mwa kumumvetsela munthu mosamala komanso mokoma mtima. Timaonetsanso cifundo mwa zokamba zathu, khalidwe lathu, magesica amene timacita, komanso mmene nkhope yathu ionekela. Timasonyeza cifundo mwa kumuonetsa cidwi ceni-ceni munthu. Timaganizila zimene amakonda, zimene amakhulupilila komanso mmene zinthu zilili pa umoyo wake. Timaphunzitsa anthu mfundo zothandiza na kuwapatsa thandizo lofunikila, koma sitiwakakamiza kusintha umoyo wawo. Ngati ena alandila thandizo limene tawapatsa, cimwemwe cathu mu ulaliki cimawonjezeka.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUONETSA CIFUNDO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuonetsa Cifundo.’ Pamalo omwela khofi, Rose akufotokoza cifukwa cake sangaphunzile Baibo tsikulo.

    Kodi Neeta anaonetsa bwanji cifundo pamene Rose anacedwa?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuonetsa Cifundo.’ Mlongo Neeta akumvetsela mwacifundo.

    Kodi Neeta anaonetsa bwanji cifundo pamene Rose anakamba kuti sakanakwanitsa kuphunzila cifukwa colema?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe Pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuonetsa Cifundo.’ Neeta athandiza Rose kuika zinthu mwadongosolo m’cipinda cake.

    Anthu amafuna kuphunzila za Yehova ngati tiwaonetsa cifundo

    Kodi Neeta anaonetsa bwanji cifundo pamene Rose anakamba kuti alibe dongosolo kweni-kweni?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani