Kunola Luso lathu mu Ulaliki—Kulankhula za Ufumu Molimba Mtima
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Tikatsatila malangizo opezeka pa 2 Timoteyo 1:7, 8, tidzaona kuti kulankhula za Ufumu molimba mtima ndi kofunika. Nanga tingakhale bwanji olimba mtima tikamalengeza za Ufumu?
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Mukaona munthu amene mufuna kulalikila, pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kulankhula molimba mtima.