LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 masa. 12-13
  • Ziphunzitso Zimene Zimatipatsa Ciyembekezo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ziphunzitso Zimene Zimatipatsa Ciyembekezo
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mulungu Adzawononga Anthu Oipa
  • Mulungu Adzawononga Satana
  • Mulungu Adzathetsa Matenda na Imfa
  • Mlengi Wathu Adzapanga Dziko Lapansi Kukhala Paradaiso
  • Mulungu Adzaukitsa Akufa
  • Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Anzake A Mulungu Adzakhala mu Paladaiso
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Mavuto Adzatha Posacedwapa!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Kodi Cifunilo ca Mulungu Kwa Anthu N’ciani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 1 masa. 12-13
Anthu ali pa mtendele na nyama, ali na cakudya camwanaalilenji, komanso ali m’paradaiso wokongola.

Ziphunzitso Zimene Zimatipatsa Ciyembekezo

Mulungu analonjeza kuti posacedwa adzakonza zinthu padziko lapansi. Iye adzathetsa mavuto onse na kupangitsa kuti anthu adzakhale na umoyo wacimwemwe padzikoli. (Salimo 37:11) N’cifukwa ciani tingalikhulupilile lonjezo limeneli? Cifukwa “Mulungu si munthu woti anganene mabodza.” (Numeri 23:19) Onani zina mwa zinthu zabwino zimene Mlengi wathu adzacita.

Mulungu Adzawononga Anthu Oipa

“Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ocita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, amatelo kuti awonongeke kwamuyaya.”—SALIMO 92:7.

Monga taonela m’nkhani yapita, zinthu zoipa zikuwonjezeka. Izi sitiyenela kudabwa nazo. Baibo inakambilatu pa 2 Timoteyo 3:1-5 kuti mu “masiku otsiliza” anthu adzaipilatu. Kodi titanthauza ciani tikati masiku otsiliza? Titanthauza masiku otsiliza a anthu oipa amene samvela Mulungu. Posacedwa, Mulungu adzawononga anthu amene amakana kusintha makhalidwe awo oipa. Akadzatelo, anthu abwino okha, amene amamvela Mulungu ndiwo adzakhale padziko lapansi. Malemba amati: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

Mulungu Adzawononga Satana

“Mulungu amene amapatsa mtendele [adzaphwanya] Satana.”—AROMA 16:20.

Satana, ziŵanda, na anthu oipa akadzacotsedwa, padziko lapansi padzakhala mtendele. Mlengi wathu analonjeza kuti: “Sipadzakhala [wokuwopsani.]”—Mika 4:4.

Mulungu Adzathetsa Matenda na Imfa

“Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu. . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.

Kuvutika komanso matenda zidzatha cifukwa Mulungu adzakonza zonse zimene zinawonongeka cifukwa ca Satana, Adamu, Hava, na kupanda ungwilo kwathu. Zotulukapo zake, “imfa sidzakhalaponso.” Anthu amene amakonda Mlengi na kumumvela adzakhala na moyo kwamuyaya. Koma kodi adzakhala kuti?

Mlengi Wathu Adzapanga Dziko Lapansi Kukhala Paradaiso

“Cipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dela lacipululu lidzakondwa ndipo lidzacita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—YESAYA 35:1.

Mulungu akadzawononga anthu oipa, dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Mudzakhala malo ambili okongola, minda yabwino, na cakudya coculuka. (Salimo 72:16) M’nyanja zamcele, m’nyanja zing’ono-zing’ono komanso m’mitsinje mudzakhala madzi aukhondo na zamoyo zambili. Anthu sadzakumbukanso kuti dziko lapansi linali loipa. Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo, ndipo palibe munthu amene adzakhala wosauka, wanjala, kapena wosoŵa pokhala.—Yesaya 65:21, 22.

Mulungu Adzaukitsa Akufa

“Kudzakhala kuuka.”—MACHITIDWE 24:15.

Kodi mumalakalaka kuonananso na okondedwa anu amene anamwalila? Mulungu Wamphamvuzonse adzawaukitsa kuti akhalenso na moyo m’Paradaiso pano padziko lapansi. Akadzaukitsidwa mudzawadziŵa, ndipo nawonso adzakudziŵani. Tangoganizilani cimwemwe cimene imwe na iwo mudzakhala naco! N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti zimenezi zidzacitika? Cifukwa m’Baibo muli zitsanzo za anthu akulu-akulu komanso ana amene anaukitsidwa, ndipo anakhalanso pamodzi na mabanja awo. Cina, nthawi zambili Yesu anali kuukitsa akufa pamaso pa anthu ambili.—Luka 8:49-56; Yohane 11:11-14, 38-44.

Tsopano Nili na Cimwemwe Ceniceni

“Nikumbukila nthawi yoyamba pamene n’namvela za dziko la paradaiso kuti simudzakhala kuvutika, matenda, na imfa. Mumtima n’naseka cifukwa coona ngati zimenezo zinali zokokomeza. Koma kuphunzila Baibo kunanithandiza kudziŵa cifukwa cake ningakhulupilile buku lapadela limeneli na zimene limalonjeza. Sinikayikila kuti Baibo ni buku locokela kwa Mulungu. Kale, nthawi zambili n’nali kuoneka wacisoni pankhope yanga. Koma tsopano nili na cimwemwe ceniceni. Ngakhale banja langa na mabwenzi anga amaona kuti tsopano ndine wacimwemwe.”—Ravi.

Ravi.

Phunzilani zambili:

Kuti mudziŵe zambili za colinga ca Mlengi cakuti anthu adzakhale na moyo kwamuyaya m’paradaiso padziko lapansi, pitani pa jw.org ku Chichewa na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO > MOYO KOMANSO IMFA.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani