LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 114
  • Mapeto A Zoipa Zonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mapeto A Zoipa Zonse
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Paladaiso Yatsopano Padziko Lapansi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhondo ya Mulungu Idzathetsa Nkhondo Zonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Zimene Baibo Imakamba Zimacitika
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 114

Nkhani 114

Mapeto A Zoipa Zonse

KODI uonapo ciani pacithunzi-thunzi apa? Inde, gulu lankhondo lili pa mahachi oyela, kapena kuti mahosi. Koma ona kumene acokela. Mahosi ali pa liŵilo kwambili m’mitambo kucoka kumwamba! Kodi uganiza kumwamba kuli mahosi eni-eni?

Iyai, awa si mahosi eni-eni. Timadziŵa zimenezi cifukwa cakuti mahosi sangathamange m’mitambo, si conco? Koma Baibo imakamba za mahosi a kumwamba. Kodi udziŵa cifukwa cake imakambila conco?

N’cifukwa cakuti mahosi anali kuwaseŵenzetsa kwambili mu nkhondo. Conco Baibo imatiuza za anthu amene akwela pa mahosi kucoka kumwamba kuonetsa kuti Mulungu adzacita nkhondo ndi anthu a padziko lapansi. Kodi malo ankhondo amenewa amachedwa kuti ciani? Amachedwa Aramagedo. Nkhondo imeneyo idzacotsa zoipa zonse padziko lapansi.

Yesu ni amene adzatsogolela nkhondo imeneyi pa Aramagedo. Kumbukila kuti, Yesu ni amene anasankhidwa ndi Yehova kuti akhale mfumu ya Boma lake. Ndiye cifukwa cake Yesu wavala cisoti cacifumu. Ndipo lupanga lionetsa kuti adzapha adani onse a Mulungu. Kodi tiyenela kudabwa kuti Mulungu adzaononga anthu onse oipa?

Tiye tibwelele kumbuyo pankhani namba 10. Kodi uonapo ciani pacithunzi-thunzi cimeneco? Tionapo cigumula cacikulu cimene cinaononga anthu oipa. Ndani anabweletsa cigumula cimeneco? Ni Yehova Mulungu. Tsopano ona pankhani namba 15. Nanga n’ciani cicitika apa? Mizinda ya Sodomu ndi Gomora ionongedwa ndi moto umene Yehova watumiza.

Tsegula pankhani namba 33. Ona zimene zicitikila mahosi ndi magaleta ankhondo a Aiguputo. Ndani anacititsa kuti madzi awambize? Ni Yehova. Anacita zimenezi kuti achinjilize anthu ake. Ona pankhani namba 76. Pankhani imeneyi tiona kuti Yehova analola ngakhale anthu ake, Aisiraeli, kuonongedwa cifukwa ca khalidwe lao loipa.

Conco, tsopano sitiyenela kudabwa kuti Yehova adzatumiza gulu lake lankhondo lakumwamba kudzacotsa zoipa zonse padziko lapansi. Koma ganizila cabe mmene zinthu zidzakhalila padziko lapansi! Tiye tione peji yotsatila.

Chivumbulutso 16:16; 19:11-16.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani