CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 17-19
Nkhondo ya Mulungu Idzathetsa Nkhondo Zonse
19:11, 14-16, 19-21
N’cifukwa ciani Yehova, “Mulungu wacikondi ndi wamtendele” anapatsa Mwana wake amene ni “Kalonga Wamtendele” nchito yomenya nkhondo?—2 Akor. 13:11; Yes. 9:6.
Yehova na Yesu amakonda cilungamo ndipo amadana na zoipa
Mtendele weni-weni na cilungamo zidzakhalapo kokha ngati anthu oipa acotsedwapo
Gulu lankhondo lakumwamba la Mulungu limene ‘likumenya nkhondo mwacilungamo,’ laimilidwa na mahosi oyela, litavala zovala zapamwamba, zoyela bwino, za mbee!
Tingacite ciani kuti tikapulumuke pa nkhondo yapadela imeneyi?—Zef. 2:3