LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ol gao 8 masa. 25-28
  • Cokani m’Cipembedzo Conama; Loŵani m’Cipembedzo Coona?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cokani m’Cipembedzo Conama; Loŵani m’Cipembedzo Coona?
  • Njila ya Kumoyo Wamuyaya—Kodi Mwaipeza?
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Masukani ku Cipembedzo Conama
  • Onongani Zinthu Zonse za Kulambila Konama
  • Gwilizanani ndi Anthu a Yehova
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kanani Cipembedzo Conama!
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Ndani Amene Ali ku Malo a Mizimu?
    Njila ya Kumoyo Wamuyaya—Kodi Mwaipeza?
Onaninso Zina
Njila ya Kumoyo Wamuyaya—Kodi Mwaipeza?
ol gao 8 masa. 25-28

MBALI 8

Cokani m’Cipembedzo Conama; Loŵani m’Cipembedzo Coona

1. Kodi anthu masiku ano afunika kusankha ciani pankhani ya kulambila?

YESU anakamba kuti: “Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine.” (Mateyu 12:30) Ngati sitili kumbali ya Yehova ndiye kuti tili kumbali ya Satana. Anthu ambili amaganiza kuti amalambila Mulungu m’njila imene iye amavomeleza, koma Baibo imakamba kuti Satana “akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Anthu mamiliyoni amakhulupilila kuti amalambila Mulungu, koma io maka-maka amatumikila Satana Mdyelekezi. Anthu masiku ano afunika kusankhapo cimodzi: Kaya kutumikila Yehova, “Mulungu wa coonadi,” kapena Satana, “tate wake wa bodza.”—Salimo 31:5; Yohane 8:44.

Masukani ku Cipembedzo Conama

2. Kodi njila ina imene Satana amaseŵenzetsa kuti aletse anthu kulambila Yehova ni iti?

2 Kusankha kutumikila Yehova ni cinthu canzelu, ndipo Mulungu amakondwela nako. Koma Satana sakondwela ndi anthu amene amatumikila Mulungu; ndipo amawabweletsela mavuto. Njila ina imene amavutitsila atumiki a Mulungu ni yakuti amasonkhezela anthu ena, ngakhale anzao ndi apabanja, kuti aziwaseka kapena kuwatsutsa. Yesu anacenjeza kuti: “Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake leni-leni.”—Mateyu 10:36.

3. Ngati apabanja panu kapena anzanu amatsutsa kulambila kwanu Mulungu, kodi mudzacita bwanji?

3 Ngati zimenezi zakucitikilani, kodi mudzacita bwanji? Anthu ambili amadziŵa kuti kulambila kwao ni kwabodza, koma safuna kuleka. Amaganiza kuti akaleka ndiye kuti samalemekeza makolo. Kodi muganiza kuti ni canzelu kucita zimenezi? Ngati mwadziŵa kuti ena pabanja panu amagwilitsila nchito mankhwala osokoneza ubongo, kodi simudzawauzako kuti mankhwala ameneo ni oipa? Kodi inu mungayambe kugwilitsila nchito mankhwala ameneo?

4. Kodi Yoswa anawauza ciani Aisiraeli pankhani ya kulambila?

4 Yoswa analimbikitsa Aisiraeli kuleka zizoloŵezi ndi miyambo ya makolo ao ya cipembedzo conama. Iye anakamba kuti: “Tsopano opani Yehova ndi kumutumikila mosalakwitsa ndiponso mokhulupilika. Cotsani milungu imene makolo anu [anali kutumikila] kutsidya lina la Mtsinje ndi ku Iguputo, ndipo tumikilani Yehova.” (Yoswa 24:14) Yoswa anali wokhulupilika kwa Mulungu, ndipo Yehova anamudalitsa. Ngati tili okhulupilika kwa Yehova, ifenso adzatidalitsa.—2 Samueli 22:26.

Ziphunzitso za Zipembedzo—Zoona ndi Zabodza

  • Wa Mboni za Yehova akuphunzila Baibulo ndi mzimayi pamodzi ndi mwana wake

    Utatu: Zipembedzo zambili zimaphunzitsa kuti Mulungu ndi Utatu. Iwo amakamba kuti: “Atate ni Mulungu, Mwana [Yesu] ni Mulungu, ndipo Mzimu Woyela ni Mulungu, koma Mulungu ni mmodzi si atatu iyai.”

    M’Baibo mulibe mau akuti “Utatu” ngakhale pang’ono, ndipo siphunzitsa kuti Yehova ndi anthu atatu mwa munthu mmodzi. Yehova yekha ndiye Mulungu. Lemba la 1 Akorinto 8:6 limakamba kuti: “Mulungu alipo mmodzi yekha basi amene ndi Atate.” Yehova ni Wam’mwamba-mwamba. Yesu si Mulungu iyai, koma ni “Mwana wa Mulungu.” (1 Yohane 4:15) Mzimu woyela nao si Mulungu. Ndipo mzimu woyela si munthu, koma ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito.—Machitidwe 1:8; Aefeso 5:18.

  • Mzimu: Zipembedzo zambili zimaphunzitsa kuti mzimu ni cinthu cina cimene cili mwa munthu ndipo sicimafa. Baibo imaphunzitsa kuti mzimu ni mphamvu ya moyo imene imacititsa thupi kukhala lamoyo koma sungacite ciliconse palibe thupi. Ndiponso, Baibo imaphunzitsa kuti akufa sangacite ciliconse.—Yakobo 2:26; Mlaliki 9:10.

  • Moto wa kuhelo: Zipembedzo zonama zimaphunzitsa kuti mizimu ya anthu oipa imazunzika kosatha kuhelo. Baibo imakamba kuti anthu akufa “sadziŵa ciliconse.” (Mlaliki 9:5) Baibo imaphunzitsanso kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Conco, Yehova, Mulungu wacikondi, sangazunze ena m’moto.

Bokosi: Kodi Baibo imaphunzitsa kuti ciani pankhani ya Utatu, mzimu, ndi moto wa kuhelo?

Onongani Zinthu Zonse za Kulambila Konama

Mzimayi akuwocha zamatsenga zake

5. N’cifukwa ciani tiyenela kuononga zinthu zonse zamatsenga?

5 Ngati tifuna kumasuka ku cipembedzo conama, tiyenelanso kuononga zinthu zonse zamatsenga zimene tingakhale nazo, monga zithumwa, mphete (maling’i) ndi zibangili zamatsenga, ndi zina zaconco. Tifunika kucita zimenezi kuti tionetse kuti tikudalila Yehova ndi mtima wathu wonse.

6. Kodi Akristu oyambilila anacita bwanji ndi mabuku ao amatsenga?

6 Ganizilani zimene Akristu ena oyambilila anacita pamene anasankha kukhala m’cipembedzo coona. Baibo imakamba kuti: “Ambili ndithu amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.”—Machitidwe 19:19.

7. Kodi tiyenela kucita ciani ngati viŵanda vitivuta?

7 Ena amene amayamba kutumikila Yehova ndipo kale anali kucita ufiti kapena zamatsenga, nthawi zina viŵanda vingawavute. Ngati zimenezi zakucitikilani, pemphelani kwa Yehova mokweza mau ndi kuchula dzina lake. Iye adzakuthandizani.—Miyambo 18:10; Yakobo 4:7.

8. Kodi Akristu amaona bwanji mafano, zifanizilo kapena zithunzi-thunzi zimene zimagwilitsidwa nchito pakulambila konama?

8 Anthu amene afuna kutumikila Yehova ayenela kuleka kugwilitsila nchito mafano, zifanizilo, kapena zithunzi-thunzi za cipembedzo conama. Akristu oona amayenda “mwa cikhulupililo, osati mwa zooneka ndi maso.” (2 Akorinto 5:7) Amamvela lamulo la Mulungu limene limaletsa kugwilitsila nchito mafano pa kulambila.—Ekisodo 20:4, 5.

Gwilizanani ndi Anthu a Yehova

Mayi ndi mwana wake akonza cakudya

9. Kodi Baibo imakamba kuti tiyenela kucita ciani kuti tikhale anzelu?

9 Baibo imakamba kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” (Miyambo 13:20) Ngati tifuna kukhala anzelu, tiyenela kuyenda, kapena kuti kugwilizana, ndi Mboni za Yehova. Anthu amenewa ndi amene akuyenda panjila yopita kumoyo.—Mateyu 7:14.

10. Kodi Mboni za Yehova zingakuthandizeni bwanji kutumikila Mulungu?

10 Mboni zimaganizila anthu anzao. Nchito yao ndi kuthandiza anthu oona mtima kuti amvetsetse coonadi ca m’Baibo cimene cidzawatsogolela kumoyo wamuyaya. Zingakuthandizeni kumvetsetsa Baibo mwa kuphunzila ndi inu mahala. Zidzayankha mafunso anu ndipo zidzakuonetsani mmene mungagwilitsile nchito cidziŵitso ca m’Baibo pa umoyo wanu.—Yohane 17:3.

11. Kodi misonkhano ya Cikristu ingakuthandizeni bwanji?

11 Pamisonkhano yao, imene imacitikila ku Nyumba ya Ufumu, mungaphunzile zambili za Yehova ndi njila zake. Mwa kupezeka pamisonkhano, cikhumbo canu cofuna kukhala m’cipembedzo coona cidzalimba. Ndiponso mudzaphunzitsidwa mmene mungathandizile anthu ena kudziŵa coonadi ca m’Baibo.—Aheberi 10:24, 25.

Mpingo uli pa msonkhano mu Nyumba ya Ufumu

12. Kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji kutumikila Mulungu?

12 Pamene mupitiliza kuphunzila zambili za cifunilo ca Yehova ndi colinga cake, mosalephela mudzamvetsetsa njila zake zacikondi ndipo mudzayamba kuzikonda. Mudzakulitsanso mtima wofuna kucita zinthu zimene iye amakondwela nazo ndi kupewa zimene samakondwela nazo. Kumbukilani kuti mungapemphele kwa Yehova kuti akuthandizeni kucita cabwino ndi kupewa coipa.—1 Akorinto 6:9, 10; Afilipi 4:6.

Banja liŵelenga Baibulo pamodzi

Kodi mungalambile bwanji m’njila ya coonadi?

13. Kodi muyenela kucita ciani kuti mukondweletse mtima wa Yehova?

13 Pamene mupitiliza kukula kuuzimu, mosakaikila inu mudzazindikila kuti mufunika kudzipeleka ndi kubatizika kuti mukhale wa Mboni za Yehova. Mukagwilizana ndi anthu a Yehova, mudzakondweletsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Mudzakhala pakati pa anthu acimwemwe amene Mulungu amakamba za io kuti: “Ndidzakhala pakati pao ndi kuyenda pakati pao. Ndidzakhala Mulungu wao, ndipo io adzakhala anthu anga.”—2 Akorinto 6:16.

Ndinamasuka ku Viŵanda

Josephine Ikezu pamodzi ndi ana ake ena

Tsiku lina usiku ndinali gone pabedi ndi mwamuna wanga. Ndinamvela mau akuitana dzina langa katatu. Ndiyeno ndinaona kuti mtenje wang’ambika, ndipo cinthu coyaka moto cimene cinali kuoneka ngati bola cinandigwela pamimba. Izi zonse amuna anga sanazione. Ngakhale ndi conco, ndinali kumvela kupsa kwambili kwa miyezi ingapo.

Patapita miyezi 6, mau aja anandiitananso. Pamenepo, nyumba yonse inaoneka ngati yamila m’madzi. Cinsato cinatuluka m’madzi ndi kukulunga dzanja langa. Ndinayesa kucicotsa koma ndinalephela. Ndinacita mantha. Ndiyeno madzi ndi njoka ija zinaleka kuoneka ndipo ndinaponyedwa pansi mwamphamvu. Ndinakomoka kwa maola ambili. Mau aja anandiuza kuti ndipitenso kukacisi wamizimu wocilitsila anthu pamudzi. Pamene ndinafunsa mzimu umeneo dzina lake, unandiuza dzina limene limatanthauza kuti “wacuma koma alibe mwana.” Unandilonjeza kuti udzandithandiza kukhala wolemela mwa kundipatsa mphamvu zocilitsila anthu.

Anthu odwala ocokela pafupi ndi kutali anali kubwela kwa ine. Anthu ameneo akalibe kufika panyumba panga, anali kuonekela pagalasi langa lapadela. Munthu akafika, ndinali kutenga dzanja langa ndi kumenya m’manja mwake, ndipo nthawi imeneyo ndinali kudziŵa matenda kapena vuto lake ndi mankhwala ake. Mzimu unali kundiuza ndalama zimene anthu anayenela kulipila.

Ndalama ndi mphatso zinali mbwee, cifukwa cakuti mankhwala anga anali amphamvu. Ndinakhaladi “wacuma,” koma ndinadziŵanso tanthauzo lakuti “alibe mwana.” Ndikabala cabe mwana, mkulu wake anali kufa. Zimenezi zinali zoŵaŵitsa mtima. Pazaka zonse 12 zimene ndinagwilila nchito mzimu umeneu, ana anga 6 anafa.

Ndinayamba kupemphela kwa Mulungu kuti andithandize. Ndinapemphela ndi mtima wonse. Tsiku lina a Mboni za Yehova anagogoda pakhomo panga. Ngakhale kuti kambili ndinali kuwathamangitsa, patsiku limeneli ndinaganiza kuti ndimvetsele. Pokambitsilana nao, ndinaphunzila kuti ndinali kuseŵenzela ciŵanda! Ndinasankha kuleka kukhulupilila zamizimu.

Pamene ndinauza mzimu uja zimenezi, unandicenjeza kuti ndisaleke. Koma ine ndinauuza kuti: “Cokani apa, sindikukufunani ngakhale pang’ono.”

Ndinaocha zinthu zonse zimene ndinali kuseŵenzetsa poombedza. Ndinaphunzila Baibo ndi Mboni, ndinakhala mtumiki wa Yehova, ndipo ndinabatizika mu 1973. Pano ndili ndi ana asanu athanzi. Mwamuna wanga naye anakhala Mboni yobatizika.—Wosimba ndi Josephine Ikezu.

Bokosi: Kodi mzimai wina anamasuka bwanji ku viŵanda?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani