PHUNZILO 5
Samueli Sanaleke Kucita Zabwino
Kuyambila ali wamng’ono kwambili, Samueli anali kukhala ndi kutumikila pa cihema. Cihema ndi malo kumene anthu anali kulambilila Yehova. Kodi udziŵa zimene zinacitika kuti Samueli azikhala pa cihema? Coyamba tiye tiphunzile za amai ake a Samueli, a Hana.
Kwa nthawi yaitali Hana anali kufunitsitsa kukhala ndi mwana, koma sizinatheke. Conco, anapemphela kwa Yehova kuti amuthandize. Hana analonjeza kuti akadzabeleka mwana wamwamuna adzamupeleka kuti azikakhala ndi kutumikila pa cihema. Yehova anayankha pemphelo lake, ndipo anakhala ndi mwana wamwamuna. Anamupatsa dzina lakuti Samueli. Conco, monga mmene Hana analonjezela, Samueli atakwanitsa zaka zitatu kapena zinai, anamupeleka pacihema kuti azikatumikila Mulungu.
Eli anali mkulu wa ansembe pa cihema. Ana ake aŵili naonso anali kugwila nchito kumeneko. Kumbukila kuti cihema cinali nyumba ya Mulungu yolambililamo, ndipo anthu anali kufunika kucita zinthu zabwino kumeneko. Koma ana a Eli anali kucita zinthu zoipa. Samueli anaona zimene io anali kucita. Koma, kodi Samueli anacita zinthu zoipa monga ana a Eli?— Ayai, iye sanaleke kucita zabwino, monga mmene makolo ake anamulangizila.
Kodi uganiza kuti Eli akanacita nao ciani ana ake aŵili?— Iye anafunika kuwalanga ndi kuwaletselatu kugwila nchito panyumba ya Mulungu. Koma Eli sanacite zimenezo, conco Yehova anakwiila Eli ndi ana ake aŵili. Yehova anaganiza zowalanga.
Samueli anapeleka uthenga wa Yehova kwa Eli
Tsiku lina usiku, Samueli ali mtulo anamva munthu akumuitana kuti: ‘Samueli!’ iye anathamangila kwa Eli, koma iye anamuuza kuti: “Sindinakuitane.” Izi zinacitikanso kaciŵili. Koma zitacitika kacitatu, Eli anauza Samueli kuti ukamvanso mau unene kuti, ‘Conde, Yehova, lankhulani; ndikumvetsela.’ Izi ndi zimene Samueli anacita. Ndiyeno Yehova anauza Samueli kuti: ‘Uza Eli kuti ndidzaweluza nyumba yake cifukwa ca zolakwa zimene io acita.’ Kodi uganiza kuti zinali zopepuka kuti Samueli auze Eli uthenga umenewu?—Iyai, zinali zovuta. Koma ngakhale kuti Samueli anacita mantha, iye anacita zimene Yehova anamuuza. Yehova anakwanilitsadi mau ake. Ana aŵili a Eli anaphedwa ndipo Eli nayenso anafa.
Samueli ndi citsanzo cabwino kwa ife. Iye sanaleke kucita zabwino ngakhale kuti anaona anthu ena akucita zoipa. Nanga bwanji za iwe? Kodi udzayesetsa kukhala ngati Samueli ndi kupitiliza kucita zabwino? Ukacita zimenezo, Yehova ndi makolo ako adzakondwela kwambili.
ŴELENGA M’BAIBULO LAKO
1 Samueli 2:22-26; 3:1-21