LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 37 tsa. 90-tsa. 91 pala. 1
  • Yehova Akamba na Samueli

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Akamba na Samueli
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Samueli Sanaleke Kucita Zabwino
    Phunzitsani Ana Anu
  • Kamnyamata Kotumikila Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Zimene Tingaphunzile kwa Samueli
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Wamphamvuzonse Koma Woganizila Ena
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 37 tsa. 90-tsa. 91 pala. 1
Samueli atsegula zitseko za ku cihema

PHUNZILO 37

Yehova Akamba na Samueli

Mkulu wa Ansembe wina, Eli, anali ndi ana aamuna aŵili amene anali kutumikila pa cihema. Maina awo anali Hofeni na Pinihasi. Iwo sanali kumvela malamulo a Yehova, ndipo anali kucitila anthu zinthu zoipa kwambili. Amati Aisiraeli akabweletsa nsembe kwa Yehova, Hofeni na Pinihasi anali kutengapo nyama yabwino kwambili kuti akadye. Eli anamvela zimene ana ake anali kucita, koma sanacitepo kanthu. Kodi Yehova analekelela zimenezi?

Olo kuti Samueli anali wamng’ono kwambili poyelekezela na Hofeni na Pinihasi, iye sanatengele khalidwe lawo. Yehova anali kum’konda Samueli. Tsiku lina atagona usiku, Samueli anamvela mawu oitana dzina lake. Anauka, n’kuthamangila kwa Eli, na kuyankha kuti: ‘Nili pano!’ Koma Eli anamuuza kuti: ‘Sin’nakuitane. Yenda ukagone.’ Samueli anapita kukagona. Koma anamvelanso kuitana. Pamene Samueli anamvela kuitana kacitatu, Eli anazindikila kuti Yehova ndiye anali kuitana Samueli. Conco, anauza Samueli kuti ngati adzamvelanso mawu omuitana, ayankhe kuti: ‘Lankhulani Yehova, ine mtumiki wanu nikumvetsela.’

Samueli afotokozela Eli zimene Yehova anamuuza

Samueli anayendanso kukagona. Koma anamvelanso kuitana kuti: ‘Samueli! Samueli!’ Pamenepo anayankha kuti: ‘Lankhulani, ine mtumiki wanu nikumvetsela.’ Yehova anamuuza kuti: ‘Umuuze Eli kuti nidzamulanga pamodzi na banja lake. Iye adziŵa kuti ana ake akucita zinthu zoipa kwambili pa cihema canga. Koma sacitapo kanthu.’ M’mawa mwake, Samueli anatsegula zitseko za cihema, monga anali kucitila nthawi zonse. Iye anacita mantha kuti auze mkulu wa ansembe zimene Yehova anamuuza. Koma Eli anamuitana na kumufunsa kuti: ‘Mwana wanga, kodi Yehova anakuuza ciani? Niuze zonse.’ Conco Samueli anafotokozela Eli zonse.

Pamene Samueli anali kukula, Yehova anapitiliza kukhala naye. Aisiraeli onse anali kudziŵa kuti Yehova anasankha Samueli kukhala mneneli ndi woweluza.

“Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”—Mlaliki 12:1

Mafunso: Kodi Samueli anali wosiyana bwanji na Hofeni komanso Pinihasi? Nanga ni uthenga uti umene Yehova anauza Samueli?

1 Samueli 2:12-17, 22-26; 3:1-21; 7:6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani