UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zimene Tingaphunzile kwa Samueli
Samueli anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova moyo wake wonse. Pamene anali wacicepele anakana kutengela makhalidwe oipa a ana a Eli, Hofeni na Pinihasi. (1 Sam. 2:22-26) Samueli anapitiliza kukula, ndipo Yehova anakhalabe naye. (1 Sam. 3:19) Ngakhale ku ukalamba wake, Samueli anapitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika ngakhale kuti ana ake anali osakhulupilika.—1 Sam. 8:1-5.
Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Samueli? Ngati ndinu wacicepele, dziŵani kuti Yehova amamvetsa mavuto amene mumakumana nawo komanso mmene mumamvelela. Iye angakuthandizeni kukhala wolimba mtima. (Yes. 41:10, 13) Ngati ndinu kholo ndipo mwana wanu analeka kutumikila Yehova, mungalimbikitsidwe kudziŵa kuti Samueli sanakakamize ana ake kutsatila miyezo ya Yehova. Iye anasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, ndipo anapitiliza kusunga umphumphu wake, moti Atate wake Wakumwamba Yehova anakondwela naye. Mukakhala wokhulupilika, mwina citsanzo canu cabwino cidzasonkhezela mwana wanu kubwelela kwa Yehova.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGAPHUNZILE KWA IWO—SAMUELI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Kodi Samueli anaonetsa bwanji kulimba mtima ali kamnyamata?
Kodi Danny anaonetsa bwanji kulimba mtima?
Kodi Samueli anapeleka bwanji citsanzo cabwino pamene anali wokalamba?
Yehova amawacilikiza anthu amene sasunthika pocita zabwino
Kodi makolo a Danny anapeleka bwanji citsanzo cabwino?