Kumanzele: Msonkhano wa pamtetete ku London mu 1945; kulamanja: Msonkhano wa pamtetete ku Malawi
CIGAWO 5
Maphunzilo a Ufumu—Kuphunzitsa Atumiki a Mfumu
TAYELEKEZELANI kuti m’bale wina akukamba nkhani pa pulatifomu. Pamene mukumuyang’ana mukumwetulila. M’baleyu ndi wacinyamata ndipo ndi wa mumpingo wanu. Iye akukamba nkhani yake yoyamba pa msonkhano waukulu. Pamene mukumvetsela nkhaniyo, mukusoŵa conena mukaganizila maphunzilo amene anthu a Mulungu amalandila. Mukakumbukila mmene m’baleyu anavutikila nthawi yoyamba pamene anakamba nkhani papulatifamu, mukucita cidwi ndi mmene wapitila patsogolo. Iye wapita patsogolo kwambili pambuyo poloŵa Sukulu ya Apainiya. Posacedwapa, m’baleyu ndi mkazi wake analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Pamene m’baleyu akumaliza nkhani yake yolimbikitsa, mukuomba m’manja. Ndiyeno mukuyang’ana anthu amene muli nao pafupi ndi kuyamikila maphunzilo amene anthu onse a Mulungu amalandila.
Baibulo linanenelatu za nthawi pamene anthu onse a Mulungu ‘adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yes. 54:13) Tikukhala m’nthawi imeneyo. Timaphunzitsidwa kupyolela m’zofalitsa zathu ndi pamisonkhano ya mpingo, kuphatikizapo misonkhano ikuluikulu. Timaphunzitsidwanso kudzela m’masukulu osiyanasiyana amene colinga cake ndi kutithandiza kusamalila mautumiki osiyanasiyana m’gulu la Yehova. M’cigawo cino, tidzaona mmene maphunzilo onsewa amapelekela umboni wamphamvu wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila masiku ano.