LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • kr nkhani 17 nkhani 182-191
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “Ndimalankhula Zinthu Izi Ndendende Mmene Atate Anandiphunzitsila”
  • Kuphunzitsa Atumiki a Mulungu Kukhala Alengezi a Ufumu
  • Kuphunzitsa Abale Kukwanilitsa Maudindo Apadela
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaphunzitsidwa Bwanji Mmene Angacitile Utumiki Wawo?
    Mafunso Ofunsidwa Kaŵili-kaŵili pa Mboni za Yehova
  • Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Pitilizani Kulandila Maphunzilo Aumulungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Onaninso Zina
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
kr nkhani 17 nkhani 182-191

NKHANI 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu amathandizila atumiki a Ufumu kukwanilitsa utumiki wao

1-3. Kodi Yesu anacita ciani kuti apititse patsogolo nchito yolalikila? Nanga zimenezo zikudzutsa mafunso otani?

KWA zaka ziŵili, Yesu analalikila m’madela onse a ku Galileya. (Ŵelengani Mateyu 9:35-38.) Iye anayenda m’mizinda ndi m’midzi yambili. Anali kuphunzitsa m’masunagoge ndi kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Makamu a anthu anali kumutsatila kulikonse kumene anali kulalikila. Yesu anati: “Zokolola n’zoculuka,” ndipo anazindikila kuti panali kufunika anchito ambili.

2 Yesu anapanga makonzedwe othandiza kuti nchito yolalikila ipite patsogolo. Kodi anacita bwanji zimenezo? Iye anatumiza atumwi ake 12 “kukalalikila Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:1, 2) N’kutheka kuti atumwiwo sanali kudziŵa kuti adzagwila bwanji nchitoyo. Koma asanawatumize, Yesu anawapatsa malangizo a mmene angagwilile nchitoyo mofanana ndi mmene Atate wake anamuphunzitsila.

3 Zimenezi zikudzutsa mafunso awa: Kodi Yesu analandila maphunzilo otani kwa Atate wake? N’ciani cimene Yesu anaphunzitsa atumwi ake? Kodi Mfumu Mesiya ikuphunzitsa otsatila ake kucita utumiki wao masiku ano? Ngati ikutelo, ikucita bwanji zimenezo?

“Ndimalankhula Zinthu Izi Ndendende Mmene Atate Anandiphunzitsila”

4. Ndi liti pamene Yesu anaphunzitsidwa? Nanga anaphunzilila kuti?

4 Yesu anakamba momveka bwino kuti anaphunzitsidwa ndi Atate wake. Pa nthawi ina mkati mwa utumiki wake, Yesu anati: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsila.” (Yoh. 8:28) Ndi liti pamene Yesu anaphunzitsidwa? Nanga anaphunzilila kuti? Mwacionekele, iye monga mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, anayamba kuphunzitsidwa atangolengedwa. (Akol. 1:15) Kwa zaka zambili, Mwanayu anakhala ndi Atate wake, amene ndi ‘Mlangizi Wamkulu,’ ndipo panthawi yonseyo anali kumvetsela zimene io anali kunena ndiponso anali kuona zimene anali kucita. (Yes. 30:20) Motelo, Mwana ameneyu anaphunzila zambili zokhudza makhalidwe a Atate ake, nchito, ndi zolinga zao.

5. Kodi Atate anapeleka malangizo otani kwa Mwana wake okhudza utumiki umene anali kudzacita padziko lapansi?

5 Yehova anaphunzitsa Mwana wake pasadakhale mocitila utumiki wake padziko lapansi. Taganizilani ulosi umene umafotokoza za ubale wa pakati pa Mlangizi Wamkulu ameneyu ndi Mwana wake woyamba kubadwa. (Ŵelengani Yesaya 50:4, 5.) Ulosiwu umanena kuti Yehova anali kudzutsa Mwana wakeyo “m’mawa uliwonse.” Mau ophiphilitsa amenewa amatikumbutsa zimene mphunzitsi amacita pothandiza mwana wa sukulu m’mawa n’colinga cakuti amuphunzitse. Buku lina lofotokoza Baibulo limati: “Monga . . . mwana wa sukulu, Yehova anali kumulowetsa m’kalasi ndi kumuphunzitsa zimene afunika kulalikila ndi mmene ayenela kulalikilila.” Panthawi imene Yesu analandila maphunzilo amenewo, Yehova anamuphunzitsa ‘zoyenela kunena ndi kulankhula.” (Yoh. 12:49) Atateyo anaphunzitsanso Mwana wake mmene angaphunzitsile ena.a Ali padziko lapansi, Yesu anagwilitsila nchito bwino zimene anaphunzila mwa kukwanilitsa utumiki wake komanso mwa kuphunzitsa otsatila ake mmene angacitile utumiki wao.

6, 7. (a) Ndi malangizo otani amene Yesu anapeleka kwa atumwi ake? Nanga malangizowo anawathandiza kucita ciani? (b) Ndi maphunzilo otani amene Yesu wapatsa otsatila ake masiku ano?

6 Kodi Yesu anawaphunzitsa ciani atumwi ake? Pa Mateyu caputala 10, Yesu anawapatsa malangizo acindunji okhudza utumiki wao. Iye anawauza kumene anafunika kukalalikila (vesi 5 ndi 6), uthenga woyenela kulalikila (vesi 7), kufunika kodalila Yehova (vesi 9 ndi 10), zoyenela kucita akafika panyumba (vesi 11 mpaka 13), zofunika kucita ngati anthu akana uthenga wao (vesi 14 ndi 15), ndiponso zoyenela kucita akamazunzidwa (vesi 16 mpaka 23).b Malangizo osapita m’mbali amene Yesu anapeleka kwa atumwi ake anawathandiza kutsogolela bwino pa nchito yolalikila uthenga wabwino m’nthawi yao.

7 Nanga bwanji masiku ano? Yesu, amene ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anapatsa otsatila ake udindo waukulu kwambili wolalikila “uthenga wabwino uwu wa ufumu . . . padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Kodi Mfumuyi imatiphunzitsa mmene tingagwilile nchito yofunika kwambili imeneyi? Inde imatiphunzitsa. Mfumu yokhala kumwamba imeneyi imaonetsetsa kuti otsatila ake akuphunzila mmene angalalikilile kwa ena ndiponso mmene angasamalile maudindo mumpingo.

Kuphunzitsa Atumiki a Mulungu Kukhala Alengezi a Ufumu

8, 9. (a) Kodi colinga cacikulu ca Sukulu ya Ulaliki cinali ciani? (b) Kodi msonkhano wa mkati mwa wiki wakuthandizani bwanji kukhala mlaliki wogwila mtima?

8 Kupyolela m’misonkhano ikuluikulu ndi misonkhano ya mpingo monga Msonkhano wa Nchito, gulu la Yehova lakhala likuphunzitsa anthu a Mulungu mmene angacitile utumiki wao. Koma kuyambila m’zaka za m’ma 1940, abale amene anali kutsogolela gulu ku likulu anapanga makonzedwe akuti pakhale masukulu osiyanasiyana ophunzitsa atumiki a Mulungu.

9 Sukulu ya Ulaliki. Monga tinaonela m’nkhani yapita, sukulu imeneyi inayamba mu 1943. Kodi colinga ca sukuluyi cinali kungothandiza ophunzila kuti azikamba bwino nkhani pamisonkhano yampingo? Iyai. Colinga cacikulu ca sukuluyi cinali kuphunzitsa anthu a Mulungu kugwilitsila nchito mphatso yao yolankhula polemekeza Yehova mu utumiki. (Sal. 150:6) Sukuluyi inali kuthandiza abale ndi alongo amene alembetsa kuti akhale atumiki ogwila mtima a Ufumu wa Mulungu.

10, 11. Ndani oyenelela kuloŵa Sukulu ya Gileadi masiku ano? Nanga colinga ca maphunzilo a sukuluyi n’ciani?

10 Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Sukulu imene tsopano imachedwa Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo, inayamba pa Mande pa February 1, mu 1943. Poyamba, colinga ca sukuluyi cinali kuphunzitsa apainiya ndi atumiki ena a nthawi zonse kuti akatumikile monga amishonale m’maiko osiyanasiyana padziko lapansi. Koma kuyambila mu October 2011, abale ndi alongo amene ali kale mu utumiki wa nthawi zonse wapadela ndi okhawo amene amaloŵa sukuluyi. Atumiki amenewa ndi apainiya apadela, oyang’anila oyendela ndi akazi ao, atumiki a pa Beteli, ndiponso amishonale ena amene sanaloŵepo sukuluyi.

11 Kodi colinga ca maphunzilo a Sukulu ya Giliyadi n’ciani? M’bale wina amene wakhala mlangizi pa sukuluyi kwa zaka zambili anati: “Colinga ca sukuluyi ndi kulimbitsa cikhulupililo ca ophunzila mwa kuwathandiza kuphunzila Mau a Mulungu mwakuya ndiponso kuwathandiza kukulitsa makhalidwe ofunika polimbana ndi mavuto pa utumiki wao. Koma colinga cacikulu ca maphunzilowa ndi kuthandiza ophunzilawo kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwila nchito yolalikila.”—Aef. 4:11.

12, 13. Kodi Sukulu ya Gileadi yathandiza bwanji pa nchito yolalikila padziko lonse? Pelekani citsanzo.

12 Kodi Sukulu ya Gileadi yathandiza bwanji pa nchito yolalikila padziko lonse? Kuyambila mu 1943, abale ndi alongo oposa 8,500 aloŵa kale sukuluyi,c ndipo amishonale amene anamaliza maphunzilo a Giliyadi akhala akutumikila m’maiko oposa 170 padziko lonse. Amishonalewa amagwilitsila nchito bwino zimene amaphunzila. Iwo ndi citsanzo cabwino pa kugwila nchito mu utumiki mwakhama ndiponso kuphunzitsa ena kucita cimodzimodzi. Nthawi zambili, amishonale akhala akutsogolela panchito yolalikila m’madela amene kuli ofalitsa Ufumu ocepa.

13 Ganizilani zimene zinacitika ku Japan. M’dzikolo, nchito yolalikila inatsala pang’ono kuimilatu panthawi ya Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Pofika mu August 1949, ku Japan kunali ofalitsa osakwana 10. Koma podzafika kumapeto kwa cakaco, m’dzikolo munafika amishonale 13 ndipo anali kulalikila mwakhama. M’kupita kwa nthawi m’dzikolo munafikanso amishonale ena ambili. Poyamba, amishonalewo anali kulalikila kwambili m’mizinda ikuluikulu, koma pambuyo pake anasamukilanso m’mizinda ina. Iwo anali kulimbikitsa kwambili anthu amene anali kuphunzila nao Baibulo ndi ofalitsa ena kuti naonso ayambe upainiya. Khama la amishonalewo linali ndi zotsatilapo zabwino kwambili. Tsopano ku Japan kuli ofalitsa Ufumu oposa 216,000, ndipo pafupifupi ofalitsa 40 pa 100 alionse ndi apainiya.d

14. Kodi masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu amapeleka umboni wotani? (Onani kamutu kakuti “Masukulu Ophunzitsa Atumiki a Ufumu,” patsamba 188.)

14 Masukulu ena ophunzitsa atumiki a Mulungu. Masukulu ochedwa Sukulu ya Apainiya, Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akristu Ali Pabanja, ndi Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatila, athandiza amene analoŵa masukuluwa kukhala okhwima mwakuuzimu ndiponso kutsogolela pa nchito yolalikila.e Masukulu amenewa ndi umboni wamphamvu wakuti Mfumu yathu yakhala ikuthandiza otsatila ake kukhala okonzeka mokwanila kukwanilitsa utumiki wao.—2 Tim. 4:5.

Kuphunzitsa Abale Kukwanilitsa Maudindo Apadela

15. Kodi abale amaudindo ayenela kutsatila citsanzo ca Yesu m’njila ziti?

15 Ganizilaninso za ulosi wa Yesaya umene umakamba zakuti Yesu anaphunzitsidwa ndi Mulungu. Pamene anali kuphunzitsidwa kumwamba, Mwana wa Mulungu anaphunzila ‘mmene angayankhile munthu wotopa.’ (Yes. 50:4) Yesu anali kugwilitsila nchito malangizo amene anapatsidwa, ndipo pamene anali padziko lapansi, iye anali kutsitsimula anthu “ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa.” (Mat. 11:28-30) Potengela citsanzo ca Yesu, abale amene ali ndi maudindo osiyanasiyana afunika kutsitsimula abale ndi alongo ao. Conco, masukulu osiyanasiyana akhazikitsidwa pofuna kuthandiza abale oyenelela kuti azitumikila bwino Akristu anzao.

16, 17. Kodi colinga ca Sukulu ya Utumiki wa Ufumu n’ciani? (Onaninso mau amunsi.)

16 Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Kalasi yoyamba ya sukulu imeneyi inayamba pa March 9, 1959, ku South Lansing, mumzinda wa New York. Oyang’anila oyendela ndiponso atumiki a mipingo anali kuitanidwa ku sukuluyi imene inali kucitika kwa mwezi wathunthu. Pambuyo pake, nkhani zacingelezi zophunzila pa sukulu imeneyi zinamasulidwa m’zinenelo zina, ndipo abale m’maiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi anayambanso kuloŵa sukuluyi.f

M’bale Lloyd Barry akuphunzitsa abale pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Japan, mu 1970

M’bale Lloyd Barry akuphunzitsa abale pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Japan, mu 1970

17 Buku Lapacaka la Mboni za Yehova lacingelezi la mu 1962 linafotokoza colinga ca Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Bukulo linati: “M’dziko lino muli zotangwanitsa zambili. Conco, woyang’anila mumpingo wa Mboni za Yehova afunika kukhala mwamuna wadongosolo n’colinga cakuti azisamalila bwino onse mumpingo ndi kuwathandiza m’njila zina. Komabe, iye safunikila kunyalanyaza banja lake cifukwa cosamalila mpingo, koma afunika kukhala woganiza bwino. Ndi mwai waukulu kwa atumiki a mipingo padziko lonse lapansi kukumana pamodzi pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kuti alandile maphunzilo amene angawathandize kucita zimene Baibulo limawalangiza kucita monga oyang’anila.”—1 Tim. 3:1-7; Tito 1:5-9.

18. Kodi anthu onse a Mulungu amapindula bwanji ndi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu?

18 Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yakhala yopindulitsa kwa anthu onse a Mulungu. Kodi io amapindula motani? Ngati akulu ndi atumiki othandiza agwilitsila nchito zimene anaphunzila ku sukuluyi, io amatsitsimula Akristu anzao monga mmene Yesu anali kucitila. Kodi mumamva bwanji mkulu kapena mtumiki wothandiza akakuuzani mau olimbikitsa, akakumvetselani mokoma mtima, kapena akakuyendelani ndi kukulimbikitsani? (1 Ates. 5:11) Amuna otelo amathandiza kwambili mipingo yao kupita patsogolo.

19. Ndi masukulu ena ati amene Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa imayang’anila? Ndipo colinga ca masukulu amenewo n’ciani?

19 Masukulu ena ophunzitsa atumiki a Mulungu. Komiti ya Bungwe Lolamulila Yoona za Ntchito Yophunzitsa, imayang’anila masukulu ena ophunzitsa abale amene ali ndi maudindo m’gulu la Mulungu. Colinga ca masukulu amenewa ndi kuthandiza abale amaudindo monga akulu, oyang’anila oyendela, ndi abale a m’Makomiti a Nthambi kukwanilitsa bwino maudindo ao. Maphunzilo ozikidwa pa Baibulo amenewa amathandiza abalewa kulimbitsa ubwenzi wao ndi Mulungu. Amawathandizanso kudziŵa mmene angagwilitsile nchito mfundo za m’Malemba posamalila nkhosa zamtengo wapatali zimene Yehova anazisiya m’manja mwao.—1 Pet. 5:1-3.

Kalasi yoyamba ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Malawi

Kalasi yoyamba ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Malawi, mu 2007

20. N’cifukwa ciani Yesu ananena kuti tonsefe ‘tikuphunzitsidwa ndi Yehova’? Nanga inuyo mukufunitsitsa kucita ciani?

20 N’zoonekelatu kuti Mfumu Mesiya yakhala ikuonetsetsa kuti otsatila ake akuphunzitsidwa bwino. Maphunzilo onsewa amacokela kwa Yehova. Iye anaphunzitsa Mwana wake, ndipo Mwana wakeyo akuphunzitsanso otsatila ake. Mpake kuti Yesu anakamba kuti onse “adzaphunzitsidwa ndi Yehova.” (Yoh. 6:45; Yes. 54:13) Tiyeni ticite zilizonse zimene tingathe kuti tipindule mokwanila ndi maphunzilo amene Mfumu yathu ikupeleka. Ndipo tisaiwale kuti colinga cacikulu ca maphunzilo amenewa ndi kutithandiza kukhalabe olimba kuuzimu ndi kuti tikwanilitse mbali zonse za utumiki wathu.

a Kodi timadziŵa bwanji kuti Atate anaphunzitsa Mwana wake mmene angaphunzitsile ena? Ganizilani izi: Yesu anali kukonda kugwilitsila nchito mafanizo polalikila, ndipo zimenezi zinakwanilitsa ulosi umene unalembedwa zaka zambilimbili iye asanabadwe. (Sal. 78:2; Mat. 13:34, 35) Mwacionekele, Mlembi wamkulu wa ulosiwo, Yehova, anadziŵilatu kuti Mwana wake adzagwilitsila nchito mafanizo pophunzitsa.—2 Tim. 3:16, 17.

b Pambuyo pa miyezi ingapo, Yesu “anasankha anthu ena 70 ndi kuwatumiza aŵiliaŵili” kuti akalalikile. Iye anawaphunzitsa zoyenela kucita.—Luka 10:1-16.

c Ena aloŵa Sukulu ya Gileadi maulendo angapo.

d Kuti mumve mmene amishonale amene analoŵa Sukulu ya Gileadi athandizila pa nchito yolalikila padziko lonse, onani mutu 23 m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom.

e Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akristu Ali Pabanja, ndiponso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatila, onse aŵili analoŵedwa m’malo ndi Sukulu ya Alengezi a Ufumu.

f Masiku ano, akulu onse amapindula ndi maphunzilo a Sukulu ya Utumiki wa Ufumu imene imacitika pambuyo pa zaka zingapo, ndipo imacitika kwa nthawi ya utali wosiyanasiyana. Kuyambila m’caka ca 1984, atumiki othandiza naonso akhala akulandila maphunzilo m’sukuluyi.

Kodi Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu ndi Weniweni?

  • Ndi maphunzilo otani amene Yesu analandila kwa Atate wake?

  • Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu yaphunzitsa bwanji otsatila ake kukhala alaliki?

  • Kodi abale a maudindo aphunzitsidwa bwanji kukwanilitsa maudindo ao?

  • Mungasonyeze bwanji kuti mumayamikila maphunzilo amene Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ikupeleka?

MASUKULU OPHUNZITSA ATUMIKI A UFUMU

UMOYO NA UTUMIKI WATHU WACIKHRISTU

Colinga: Kuphunzitsa ofalitsa kuti azilalikila ndi kuphunzitsa mogwila mtima uthenga wabwino.

Nthawi: Siikutha.

Malo: Pa Nyumba ya Ufumu.

Oyenela Kuloŵa: Onse amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse, ndipo amavomeleza zimene Baibulo limaphunzitsa komanso amayesetsa kutsatila mfundo za m’Malemba. Mungalembetse kwa woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki.

Mapindu: Msonkhano wa mkati mwa wiki umatiphunzitsa kufufuza zinthu na kuzifotokoza motsatilika. Umatithandizanso kumvetsela pamene ena akulankhula ndi kuona mmene tingawathandizile mwauzimu m’malo moganizila zathu zokha.

M’bale Arnie amene wakhala woyang’anila woyendela kwa nthawi yaitali anati: “Ndili mnyamata ndinali wacibwibwi ndipo sindinali kuyang’ana anthu polankhula nao. Koma msonkhano umenewu wandithandiza kuti ndisamadzikaikile. Kudzela mu msonkhanowu, Yehova wandithandiza kudziŵa kupuma bwino polankhula ndi kuika maganizo pa zimene ndikucita. Ndimasangalala kwambili kuti panopa ndimatha kutamanda Mulungu mu mpingo ndiponso mu utumiki.”

Wofalitsa wacicepele akuŵelenga Baibulo mu Sukulu ya Ulaliki

SUKULU YA AKULUg

Colinga: Kuthandiza akulu kuti azigwila bwino nchito yao mu mpingo ndi kuti azikonda kwambili Mulungu.

Nthawi: Masiku asanu.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha. Koma nthawi zambili imacitikila pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Nyumba ya Msonkhano.

Oyenela Kuloŵa: Akulu, ndipo ofesi ya nthambi ndi imene imawadziŵitsa.

Mapindu: Tamvani zimene ananena akulu ena amene analoŵa kalasi ya nambala 92 ku Patterson, New York, m’dziko la United States:

“Sukuluyi yandithandiza kwambili cifukwa yandilimbikitsa kudzifufuza ndi kuona mmene ndingasamalile nkhosa za Yehova.”

“Mfundo zimene ndaphunzila zindithandiza moyo wanga wonse.”

SUKULU YA APAINIYA

Colinga: Kuthandiza apainiya kuti ‘akwanilitse mbali zonse’ za utumiki wao.—2 Tim. 4:5.

Nthawi: Masiku 6.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha koma nthawi zambili imacitikila pa Nyumba ya Ufumu.

Oyenela Kuloŵa: Amene acita upainiya wokhazikika kwa caka cimodzi kapena kuposelapo. Apainiya oyenelela amadziŵitsidwa ndi woyang’anila dela. Apainiya ena amene atumikila kwa nthawi yaitali, ndipo papita zaka zisanu kucokela pamene analoŵa sukuluyi angaitanidwe kuti aloŵenso.

Mapindu: Mlongo Lily anati: “Sukuluyi yandithandiza kuti ndizithana ndi mavuto mu utumiki komanso pa moyo wanga. Tsopano ndadziŵa mmene ndingaphunzilile bwino Baibulo ndi mmene ndingaphunzitsile ena mowafika pamtima. Ndine wokonzeka kuthandiza ena, kucita zinthu mogwilizana ndi akulu ndi kuthandiza mpingo wonse kuti ukule.”

Brenda amene analoŵa sukuluyi kaŵili anati: “Sukuluyi yandithandiza kukonda kwambili coonadi, kulimbitsa cikumbumtima canga ndiponso kuti ndizikonda kuthandiza ena. Kunena zoona, Yehova ndi wabwino.”

SUKULU YA ATUMIKI A PA BETELI ATSOPANO

Colinga: Kuthandiza amene angofika kumene pa Beteli kuti azicita bwino utumiki wao.

Nthawi: Masiku 4, maola 4 pa tsiku.

Malo: Ku Beteli.

Oyenela Kuloŵa: Munthu amene akutumikila pa Beteli nthawi zonse kapena amene wavomelezedwa kutumikila pa Beteli kwa caka cimodzi kapena zingapo.

Mapindu: M’bale Demetrius amene analoŵa sukuluyi m’ma 1980 anati: “Sukuluyi inandithandiza kuti ndiziphunzila bwino Baibulo ndi kuti ndikhale wokonzeka kutumikila nthawi yaitali pa Beteli. Alangizi ake, maphunzilo ake ndi malangizo amene tinali kupatsidwa zinandithandiza kuona kuti Yehova amandikonda ndi kuti amafuna kuti ndizicita bwino utumiki wa pa Beteli.”

SUKULU YA ALENGEZI A UFUMUh

Colinga: Kupeleka maphunzilo apadela kwa amene ali mu utumiki wa nthawi zonse (amene ali pabanja, abale osakwatila, ndi alongo osakwatiwa) kuti Yehova ndi gulu lake awagwilitsile nchito mokwanila. Ambili a omaliza maphunzilowa amatumizidwa kumene kuli ofalitsa ocepa kapena kumene kulibiletu. Ena a omaliza maphunzilowa amene sanakwanitse zaka 50 amaikidwa kukhala apainiya apadela akanthawi, ndi kutumizidwa ku madela akutali kuti akapititse patsogolo nchito yolalikila ku madelawo.

Nthawi: Miyezi iŵili.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha koma nthawi zambili imacitikila pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Nyumba ya Msonkhano.

Mlongo ali mu ulaliki

Abale ndi alongo amapindula ndi masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu

Oyenela kuloŵa: Abale ndi alongo a zaka za pakati pa 23 ndi 65 amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, a thanzi labwino, ndiponso amene angathe kukatumikila kumene kukufunika thandizo ndipo ali ndi mtima wa, “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Onse oloŵa sukuluyi, amene ali pa banja kapena amene sali pabanja, akhale oti akhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zosacepela ziŵili mosalekeza. Abale ndi alongo amene ali pabanja akhale akuti akwanitsa zaka ziŵili ali pabanja. Abale akhale kuti atumikila pa udindo monga mtumiki wothandiza kapena mkulu kwa nthawi yosacepela zaka ziŵili mosalekeza. Pa msonkhano wacigawo padzakhala kukumana kwa abale ndi alongo amene afuna kuloŵa sukuluyi ngati sukuluyi idzacitika m’dziko lanu.

Mapindu: Amene analoŵa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatila, ndi Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akristu Ali Pabanja akhala akupeleka ndemanga zambili zolimbikitsa zokhudza masukuluwa. Mu 2013, Bungwe Lolamulila linavomeleza kuti masukulu aŵiliwa aphatikizidwe ndi kupanga sukulu imodzi yochedwa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Apainiya ambili okhulupilika, kuphatikizapo alongo osakwatiwa, adzapindula kwambili ndi sukuluyi.

SUKULU YA GILIYADI YOPHUNZITSA BAIBULO

Colinga Cake: Omaliza maphunzilowa angaikidwe kukhala oyang’anila oyendela, amishonale, kapena atumiki a pa Beteli. Mwa kugwilitsila nchito zimene anaphunzila, io amathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino mu utumiki komanso panthambi.

Nthawi: Miyezi isanu.

Malo: Ku Likulu la Maphunzilo la Watchtower ku Patterson, ku New York.

Abale ndi alongo a m’kalasi ya Giliyadi akumvetsela kwa mphunzitsi wa Giliyadi

Kalasi ya Giliyadi ku Patterson, New York

Oyenela Kuloŵa: Akristu a pabanja ndiponso abale ndi alongo amene sali pabanja ndipo ali kale mu utumiki wa nthawi zonse wapadela. Komiti ya Nthambi ingapemphe amishonale amene sanalowepo sukuluyi, apainiya apadela, oyang’anila oyendela kapena atumiki a pa Beteli kuti afunsile kuloŵa sukuluyi. Akhale oti amakwanitsa kukamba, kuŵelenga ndi kulemba Cingelezi bwinobwino.

Mapindu: Lade ndi mkazi wake, Monique, a ku United States, akhala mu utumiki wao kwa zaka zingapo.

Lade anati: “Sukuluyi inatikonzekeletsa kupita kulikonse kukagwila nchito mwakhama limodzi ndi abale athu okondedwa.”

Nayenso Monique anati: “Ndikamatsatila zimene ndaphunzila m’Mau a Mulungu ndimasangalala kwambili ndi utumiki wanga. Zimenezi zimandisonyeza kuti Yehova amandikonda kwambili.”

SUKULU YA UTUMIKI WA UFUMU

Colinga: Kuphunzitsa oyang’anila oyendela, akulu ndi atumiki othandiza kuti azicita bwino utumiki wao. (Mac. 20:28) Amathandizidwa kudziŵa zinthu zatsopano ndiponso mmene angathandizile abale ndi alongo malinga ndi mmene zinthu zikusinthila m’dzikoli. Imacitika pakapita zaka zingapo, ndipo Bungwe Lolamulila ndi limene limakonza kuti icitike.

Nthawi: M’zaka zaposacedwapa, sukuluyi yakhala ikucitika kwa nthawi ya utali wosiyanasiyana.

Malo: Pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Nyumba ya Msonkhano.

Oyenela Kuloŵa: Woyang’anila dela amauza akulu ndi atumiki othandiza za sukuluyi, ndipo ofesi ya nthambi ndi imene imauza oyang’anila oyendela.

Mapindu: M’bale Quinn anati: “Ngakhale kuti amaphunzila zinthu zambili nthawi yocepa, sukuluyi imalimbikitsa akulu ndi kuwathandiza kukhalabe acimwemwe ndi ‘kupitiliza kucita camuna’ potumikila Yehova. Akulu atsopano ndiponso amene atumikila nthawi yaitali amaphunzila mmene angawetele nkhosa ndi kukhala ndi maganizo amodzi.”

M’bale Michael anati: “Sukuluyi inatithandiza kukhala ndi mtima woyamikila zinthu zauzimu, inaticenjeza za zinthu zoopsa ndi kutidziŵitsa mmene tingasamalile nkhosa.

SUKULU YA OYANG’ANILA MADELA NDI AKAZI AOi

Colinga: Kuthandiza oyang’anila madela kuti azigwila bwino nchito zao akamatumikila mipingo, kuti ‘azicita khama polankhula ndi kuphunzitsa,’ ndi kuti aziweta nkhosa zimene zili m’manja mwao.—1 Tim. 5:17; 1 Pet. 5:2, 3.

Nthawi: Mwezi umodzi.

Malo: Imasankha ndi ofesi ya nthambi.

Oyenela Kuloŵa: Ofesi ya nthawi ndi imene imaitana oyang’anila madela ndi akazi ao.

Mapindu:“Tinathandizidwa kumvetsa zimene Yesu akucita potsogolela gulu. Tinaona kuti m’pofunika kulimbikitsa abale amene timawatumikila ndi kulimbikitsa mgwilizano mu mpingo. Sukuluyi inatithandiza kudziŵa kuti ngakhale kuti oyang’anila oyendela amafunika kupeleka malangizo ndi kuongolela zinthu zina, colinga cao cacikulu ndi kuthandiza abale kuona kuti Yehova amawakonda.”—Joel ndi Connie, kalasi yoyamba, mu 1999.

SUKULU YA ABALE A M’KOMITI YA NTHAMBI NDI AKAZI AO

Colinga: Kuphunzitsa abale a m’Komiti ya Nthambi kuti azigwila bwino nchito yao yotsogolela mabanja a Beteli, kusamalila nchito ya utumiki yokhudza mipingo, ndiponso kuyang’anila madela.—Luka 12:48b.

Nthawi: Miyezi iŵili.

Malo: Ku Likulu la Maphunzilo la Watchtower ku Patterson, ku New York.

Oyenela Kuloŵa: Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila ndi imene imaitana abale a m’Komiti ya Nthambi kapena a m’Komiti ya Dziko ndi akazi awo.

Mapindu: M’bale Lowell ndi mkazi wake, Cara, analoŵa kalasi ya nambala 25 ndipo akutumikila ku Nigeria.

M’bale Lowell anati: “Ndinakumbutsidwa kuti kaya ndili wotanganidwa bwanji, kaya ndapatsidwa nchito yotani, cinthu cofunika kwambili ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.”

Mlongo Cara anafotokoza mfundo imene anaphunzilapo pa sukuluyo. Iye anati: “Ngati sindingathe kufotokoza mfundo m’njila yosavuta ndiye kuti ndifunika kuiphunzila bwino ndisanakaphunzitse ena.”

g M’maiko ambili, sukuluyi sinayambe kucitika.

h M’maiko ambili, sukuluyi sinayambe kucitika.

i M’maiko ambili, sukuluyi sinayambe kucitika.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani