LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 14
  • Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Sukulu ya Giliyadi—Ophunzila Ake Amacokela Padziko Lonse
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 14

PHUNZILO 14

Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?

Atumiki a nthawi zonse ali mu ulaliki

Ku United States

Ophunzila akulandila maphunzilo mu Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibo
A m’kilasi yaumishonali akonzekela maphunzilo awo

Sukulu ya Gileadi, ku Patterson, New York

mishonali ali pabanja alalikila ku Panama

Ku Panama

Kwa zaka zambili, maphunzilo aumulungu akhala mbali yofunika kwambili kwa Mboni za Yehova. Anthu amene amadzipeleka kuti azilalikila za Ufumu nthawi zonse, amalandila maphunzilo apadela kuti ‘akwanilitse mbali zonse za utumiki wawo.’—2 Timoteyo 4:5.

Sukulu ya Apainiya. Mpainiya wa nthawi zonse akakwanitsa caka cimodzi mu utumiki wake, amaloŵa sukulu ya masiku 6 imene ingacitikile pa Nyumba ya Ufumu ya kufupi ndi kwawo. Colinga ca sukulu imeneyi ni kuthandiza apainiya kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova, kunola maluso awo m’mbali zonse za utumiki, komanso kuti apitilize kutumikila mokhulupilika.

Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Sukulu imeneyi ya miyezi iŵili, anakonzela apainiya aciyambakale amene ni okonzeka kucoka kwawo ndi kukatumikila kumene alaliki ni ocepa. Amakhala ngati akukamba kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” Amacita izi potengela citsanzo ca Mlaliki wopambana onse amene anakhalapo padziko lapansi, Yesu Khristu. (Yesaya 6:8; Yohane 7:29) Kusamukila kumalo akutali kungafune kuti munthu ajaile kukhala na umoyo wosalila zambili. Cikhalidwe, nyengo, ndi cakudya zikhoza kukhala zosiyana kwambili na zimene anazoloŵela kwawo. Angafunikenso kuphunzila citundu catsopano. Sukulu imeneyi imathandiza abale ndi alongo amene sali pabanja, ndi amene ali pabanja, a zaka zoyambila 23 mpaka 65, kukulitsa makhalidwe auzimu ofunikila pa utumiki wawo. Imawathandizanso kuphunzila maluso amene adzacititsa kuti Yehova na gulu lake liwagwilitsile nchito kwambili.

Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibo. M’ciheberi, liu lakuti “Giliyadi” limatanthauza “Mulu wa Umboni.” Kucokela pamene sukulu ya Giliyadi inayamba mu 1943, anthu otsiliza maphunzilo opitilila 8,000 atumizidwa monga amishonali kuti akacitile umboni “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi,” ndipo pakhala zotulukapo zabwino. (Machitidwe 13:47) Mwacitsanzo, pamene otsiliza maphunzilo a Giliyadi anafika m’dziko la Peru koyamba, m’dzikomo munalibe mpingo olo umodzi. Koma lomba muli mipingo yopitilila 1,000. Amishonali athu atayamba kutumukila m’dziko la Japan, munali Mboni zosakwana 10. Koma lomba kuli Mboni zopitilila 200,000. Ku Sukulu ya Giliyadi imeneyi ya miyezi isanu, amaphunzila Mau a Mulungu mozamilapo. Aja amene akumikila monga apainiya apadela, amishonali, m’maofesi a nthambi, kapena oyang’anila madela, amaitanidwa kuti akaloŵe sukuluyi. Amalandila maphunzilo akuya kuti alimbikitse na kupititsa patsogolo nchito ya padziko lonse.

  • Kodi colinga ca Sukulu ya Apainiya n’ciani?

  • Kodi Sukulu ya Alengezi a Ufumu anakonzela ndani?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani