LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 December tsa. 7
  • Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Funsilani Kuloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Amishonale Akutumizidwa “Mpaka Kumalekezelo a Dziko Lapansi”
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 December tsa. 7
Abale na alongo ali m’kilasi ya Sukulu ya Alengezi a Ufumu.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu

Kodi ndimwe mtumiki wanthawi zonse ndipo muli na zaka zapakati pa 23 na 65? Kodi muli na thanzi labwino ndipo ndimwe wodzipeleka kukatumikila kulikonse kumene kuli alengezi a Ufumu ocepa? Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso amenewa, kodi munaganizilapo zofunsila kuti mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu? Kucokela pamene sukuluyi inayamba, Akhristu a pabanja, abale osakwatila, komanso alongo osakwatiwa ofika m’masauzande afunsilako sukuluyi. Koma tifunabe abale ambili osakwatila kuti afunsile sukuluyi. Pemphani Yehova kuti akulitse cilakolako canu cofuna kum’kondweletsa na kutengela citsanzo ca Mwana wake. (Sal. 40:8; Mat. 20:28; Aheb. 10:7) Kenako ganizilani mmene mungasinthile zinthu pa umoyo wanu kuti mukwanitse kufunsilako sukuluyi.

Kodi Akhristu amene aloŵa sukuluyi amakhala na mwayi wocita mautumiki ati? Ena amawatumiza kuti akatumikile m’magawo a citundu cina kapena kuti akacite ulaliki wapoyela wa m’mizinda ikulu-ikulu. Ndipo ena pambuyo pake amatumikila monga oyang’anila madela ogwilizila, oyang’anila madela, kapena amishonale. Pamene muganizila za utumiki umene mungaciteko m’gulu la Yehova, khalani na maganizo amene Yesaya anali nawo pamene anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni!”—Yes. 6:8.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI AMISHONALE—ANCHITO OKOLOLA, NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Amishonale—Anchito Okolola.’ Mwamuna na mkazi wake amene ni amishonale akuyenda mumsewu pamene ali mu ulaliki.

    Kodi amishonale amasankhidwa bwanji?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Amishonale—Anchito Okolola.’ M’mishonale na mlongo wina akuphunzila Baibo na mzimayi.

    Kodi amishonale amagwila nchito yabwino iti?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Amishonale—Anchito Okolola.’ M’mishonale amene akutumikila m’gawo la cinenelo camanja akukambilana na m’bale wina za m’fomu yofunsila utumiki wapadela.

    Ni madalitso ena ati amene utumiki wa umishonale umabweletsa?

Kodi mufuna kudziŵa zambili zokhudza Sukulu ya Alengezi a Ufumu? Pitani ku “Mavidiyo,” pa mbali ya pa jw.org yakuti Laibulali, ndiyeno onani pa ZIMENE TIMACITA > MASUKULU AUMULUNGU NA MAPHUNZILO. Tambani mavidiyo aya: Masukulu a Zaumulungu mu Africa, Olemela Mwauzimu Cifukwa Cophunzitsidwa na Yehova, komanso yakuti Mwambo Wotsiliza Maphunzilo a Sukulu ya Alengezi a Ufumu Yoyamba.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani