LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 April tsa. 8
  • Pitilizani Kulandila Maphunzilo Aumulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pitilizani Kulandila Maphunzilo Aumulungu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaphunzitsidwa Bwanji Mmene Angacitile Utumiki Wawo?
    Mafunso Ofunsidwa Kaŵili-kaŵili pa Mboni za Yehova
  • Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Funsilani Kuloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 April tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pitilizani Kulandila Maphunzilo Aumulungu

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Mlangizi Wamkulu Yehova, amatipatsa maphunzilo abwino koposa. Kwaulele, iye amatiphunzitsa mmene tingakhalile na umoyo wabwino, ndiponso amatikonzekeletsa mmene tingakhalile na tsogolo labwino. (Yes. 11:6-9; 30:20, 21; Chiv. 22:17) Kupitila m’maphunzilo aumulungu, Yehova amatiphunzitsa mmene tingauzileko ena uthenga wopatsa moyo.—2 Akor. 3:5.

MMENE TINGACITILE:

  • Kulitsani khalidwe la kudzicepetsa na kufatsa.—Sal. 25:8, 9

  • Landilani maphunzilo amene Yehova akukupatsani pali pano. Mwacitsanzo mbali za m’sukulu pa msonkhano wa mkati mwa wiki

  • Dziikileni zolinga zauzimu.—Afil. 3:13

  • Yesetsani kudzipeleka kuti muyenelele kucita maphunzilo owonjezeleka.—Afil. 3:8

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI OLEMELA MWAUZIMU CIFUKWA COPHUNZITSIDWA NA YEHOVA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni zopinga zotani zimene ofalitsa ena anakumana nazo kuti angene Sukulu ya Alengezi a Ufumu?

  • Kodi Sukulu ya Alengezi a Ufumu imaphunzitsa zotani?

  • Kodi abale na alongo amene anatsiliza maphunzilo a Sukulu ya Alengezi a Ufumu anathandizidwa bwanji na abale a m’mipingo imene anatumizidwako?

  • Kodi cofunika n’ciani kuti munthu ayenelele kungena Sukulu ya Alengezi a Ufumu? (kr 189)

  • Ni maphunzilo ena ati amene mungaciteko m’gulu la Yehova?

Otsiliza maphunzilo a Sukulu ya Alengezi a Ufumu akutumikila ku Namibia, Norway, United States, na ku Japan

Ni madalitso otani amene mudzapeza mukacita maphunzilo aumulungu?

MAPHUNZILO AUMULUNGU AMENE NACITAKO:

  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu

  • Sukulu ya Apainiya

  • Sukulu ya Utumiki wa Ufumu

  • Sukulu ya Akulu a Mpingo

  • Sukulu ya Alengezi a Ufumu

MAPHUNZILO AUMULUNGU AMENE NIFUNA KUCITA:

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani