LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ypq funso 10 masa. 30-31
  • Kodi Baibo Ingan’thandize Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Ingan’thandize Bwanji?
  • Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa
  • Nkhani Zofanana
  • Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
    Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
  • 12 Zolinga
    Galamuka!—2018
  • Malangizo Owonjezela kwa Makolo
    Galamuka!—2019
Onaninso Zina
Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa
ypq funso 10 masa. 30-31
Mnyamata wakhala pansi panja aŵelenga Baibo

10

Kodi Baibo Ingan’thandize Bwanji?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Baibo imakamba kuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Ngati zimenezi n’zoona, ndiye kuti Baibo ni imene ingakutsogolele bwino.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Ganizila cocitika ici: David ali paulendo ayendetsa motoka. Kenako, aona kuti ciliconse cioneka cacilendo. Poyang’ana zikwangwani za m’mbali mwa mseu, David wadziŵa kuti wasoŵa. Azindikila kuti penapake watenga mseu wolakwika.

Kukhala David, ungacite bwanji?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

Sankha zimene ungacite pa izi:

  1. Kufunsa anthu kuti akuonetse njila.

  2. Kuyang’ana pa mapu, olo pa pulogilamu ya GPS.

  3. Kungopitiliza kuyendetsa motoka kuti mwamwayi ungatulukile m’njila imene ufuna.

Mwacionekele, C si yothandiza kweni-kweni.

Koma B ni yabwino kuposa A. Zili conco cifukwa mapu kapena GPS imakutsogolela paliponse pamene wafika.

Baibo ingakuthandize m’njila yofanana.

Buku yofunika kwambili imeneyi

  • ingakuthandize pa mavuto mu umoyo wako

  • ingakuthandize kudzidziŵa bwino kuti ukhale munthu wanzelu

  • ingakupatse nzelu zopezela umoyo wabwino lelo mpaka muyaya

KUYANKHA MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI MU UMOYO

Mwana akangoyamba kukamba, amafunsa mafunso.

  • Dzuŵa imayenda kuti?

  • Nyenyezi ni zingati?

Tikakula timayamba kufunsa pa zocitika za m’dziko.

  • N’cifukwa ciani zinthu zoipa zimacitika?

  • N’cifukwa ciani anthu amafa?

Kodi udziŵa kuti mayankho pa mafunso aya alimo m’Baibo?

Anthu ambili amakamba kuti nkhani zonse za m’Baibo ni nthano cabe, inasila nchito, kapena ni yovuta kuimvetsetsa. Kodi uganiza vuto ni Baibo, kapena ni zimene anthu amakamba? Kodi si zoona kuti amauzidwa zolakwika?

Mwacitsanzo, anthu amaganiza kuti Baibo imakamba kuti Mulungu ndiye amalamulila dziko lonse. Koma zimenezo n’zosatheka! M’dziko muli cipwilikiti cokha-cokha. Muli mavuto, matenda, imfa, umphawi, na ngozi zosiyana-siyana. Kodi n’zoona kuti Mulungu wacikondi ndiye amacititsa mavuto onse aya?

Koma kodi ufuna kudziŵa yankho ya zoona? Mwina ungadabwe kumvela amene Baibo imamutomola kuti ndiye wolamulila dziko lonse lapansi.

Tikhulupilila waona kuti malangizo ali m’kabuku kano ni ocokela m’Baibo. A Mboni za Yehova amadziŵa bwino kuti malangizo anzelu amapezeka m’Baibo. Zili conco cifukwa mau ake “anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Ufunika kuisanthula na kuimvetsetsa bwino buku imeneyi—yamakedzana, komanso yamakono!

KUTI UDZIŴE ZAMBILI!

N’cifukwa Ninji Kuŵelenga Baibo N’kofunika?

Ukatambe vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? pa www.jw.org.

[DO NOT SET] This page will not contain any WEB tags or SEO information.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani