Mawu Oyamba a Cigawo 1
Baibo imayamba nkhani zake mwa kufotokoza zinthu zokongola zimene Yehova analenga kumwamba na pa dziko lapansi. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kudziŵa zinthu zodabwitsa za cilengedwe. M’fotokozeleni za mmene Mulungu analengela ise anthu mwapadela kwambili, kupambana nyama. Ife anthu timakamba, kuganiza, kupanga zinthu, kuimba, na kupemphela. M’thandizeni kuyamikila mphamvu za Yehova na nzelu zake, maka-maka cikondi cake pa zinthu zonse zimene analenga—kuphatikizapo aliyense wa ise.