Mawu Oyamba a Cigawo 4
Cigawo cino cifotokoza za Yosefe, Yobu, Mose, komanso Aisiraeli. Onsewa anavutika kwambili cifukwa ca Mdyelekezi. Ena anacitilidwa zopanda cilungamo, kuponyewa m’ndende, kuikidwa ukapolo, ngakhale kufedwa okondedwa awo mwadzidzidzi. Ngakhale n’telo, Yehova anawateteza m’njila zolekana-lekana. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa mmene atumiki a Yehova anavutikila, koma osataya cikhulupililo cawo.
Yehova anaseŵenzetsa Milili 10 kuonetsa kuti iye ni wamphamvu ngako kupambana milungu yonse ya Aiguputo. Fotokozani mmene Yehova anatetezela anthu ake kumbuyoko, na mmene amawatetezela masiku ano.