Mawu Oyamba a Cigawo 11
Cigawo cino cifotokoza nkhani za m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Yesu anabadwila m’banja yosaukila, imene inali kukhala m’tauni yaing’ono. Anali kuthandiza atate ake pa nchito yawo ya ukalipentala. Yesu ndiye anali kudzapulumutsa mtundu wa anthu. Yehova anam’sankha kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa kuti Yehova anasankha mosamala banja limene Yesu adzabadwilamo, komanso kumene adzakulila. Fotokozani mmene Yehova anatetezela Yesu kuti asaphedwe na Herode, komanso kuti palibe cingalepheletse colinga ca Yehova. Kambilanani za mmene Yehova anapatsila Yohane nchito yokonzela njila Yesu. Unikani mmene Yesu anaonetsela kuti kuyambila ali mwana, anali kukonda nzelu zocokela kwa Yehova.