Mawu Oyamba a Cigawo 13
Yesu anabwela pa dziko lapansi kudzapeleka moyo wake kaamba ka anthu opanda ungwilo. Ngakhale anafa, iye anagonjetsa dziko. Yehova anakhulupilika kwa Mwana wake, ndipo anamuukitsa atamwalila. Mpaka imfa yake, Yesu modzicepetsa anali kutumikila ena, ndipo anali kuwakhululukila akalakwitsa. Yesu ataukitsidwa, anaonekelanso kwa ophunzila ake. Anawaphunzitsa mmene angagwilile nchito yofunika kwambili imene anawapatsa. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kudziŵa kuti, ngakhale masiku ano, tili na mwayi wotengako mbali m’nchito imeneyo.