Mawu Oyamba a Cigawo 12
Yesu anali kuphunzitsa anthu za Ufumu wa kumwamba. Anaŵaphunzitsanso kuti azipemphela kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe, Ufumu wake ubwele, komanso kuti cifunilo cake cicitike pa dziko lapansi. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa kuti pemphelo imeneyi ni yofunika kwambili kwa ise. Yesu sanalole kuti Satana amutaitse cikhulupililo cake mwa Mulungu. Yesu anasankha atumwi ake, oyamba kusankhidwa kuti akalamulile mu Ufumu wa Mulungu. M’cigawo cino, mudzaona kuti Yesu anali wodzipeleka pa kulambila koona. Cinanso, Yesu anali kukonda kuthandiza anthu. N’cifukwa cake anacilitsa odwala, kudyetsa anjala, ngakhalenso kuukitsa akufa. Mwa izi, Yesu anaonetsa zimene Ufumu wa Mulungu udzacitila anthu.