Mawu Oyamba a Cigawo 5
Patapita miyezi iŵili, Aisiraeli atawoloka Nyanja Yofiila, anafika pa Phili la Sinai. Pamalo amenewo, Yehova anacita pangano na mtundu wa Isiraeli kuti adzakhala mtundu wake wapadela. Iye anawateteza na kuwapatsa zonse zofunikila monga cakudya ca mana, zovala zimene sizinali kutha, komanso malo okhala otetezeka. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa cifukwa cake Yehova anapatsa Aisiraeli Cilamulo, cihema colambililako, komanso ansembe. Gogomezani kufunika kocita zimene talonjeza, kukhala odzicepetsa, na kukhala okhulupilika kwa Yehova nthawi zonse.