NYIMBO 1
Makhalidwe a Yehova
Yopulinta
(Chivumbulutso 4:11)
1. Mulungu wathu wamphamvu zonse.
Tiyamikila potipatsa moyo.
Cilengedwe canu cimanena
za mphamvu zanu zodabwitsa.
2. Yehova ndimwe wokoma mtima.
Ufumu wanu ni wacilungamo.
Mau anu amapatsa nzelu.
Timalengeza njila zanu.
3. Mumatipatsa zonse zabwino.
Cikondi canu cimatidabwitsa.
Mwa cimwemwe tikuimbilani.
Tidzatamanda dzina lanu.
(Onaninso Sal. 36:9; 145:6-13; Mla. 3:14; Yak. 1:17)