Yehova Amatisamalila ndi Kutiteteza
“Popeza wasonyeza kuti amandikonda, Inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza cifukwa wadziŵa dzina langa.”—SAL. 91:14.
1, 2. Kodi umoyo wa anthu a m’banja limodzi umasiyana bwanji? Nanga timaphunzila coonadi m’njila zosiyana-siyana ziti?
YEHOVA ndiye anayambitsa banja. (Aef. 3:14, 15) Anthu angakhale a m’banja limodzi, koma makhalidwe ao ndi zokumana nazo pa umoyo wao zingakhale zosiyana. Ena analeledwa ndi makolo. Ena makolo ao anamwalila cifukwa ca matenda, ngozi kapena tsoka linalake. Ndipo anthu ena makolo ao samawadziŵa n’komwe.
2 Atumiki a Yehova amaphunzila coonadi m’njila zosiyana-siyana. Ena analeledwa ndi makolo amene anawaphunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Deut. 6:6, 7) Mwina ena anaphunzila coonadi cifukwa cakuti mtumiki wina wa Yehova anawalalikila.—Aroma 10:13-15; 1 Tim. 2:3, 4.
3. Kodi tonsefe timafanana bwanji?
3 Ngakhale kuti tinakula m’njila zosiyana-siyana, ndife ofanana pa zinthu zina. Popeza kuti Adamu sanamvele Mulungu, tonse ndife opanda ungwilo, tili ndi ucimo ndipo timafa. (Aroma 5:12) Komabe, monga atumiki oona, timacha Yehova kuti “Atate wathu.” Anthu a Yehova akale anali kunena mau amene ali pa Yesaya 64:8 akuti: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu.” Nayenso Yesu anayamba pemphelo lake la citsanzo ndi mau akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.”—Mat. 6:9.
4, 5. Kodi tidzakambitsilana mfundo ziti zimene zingatithandize kukulitsa cikondi cathu pa Atate wathu wakumwamba, Yehova?
4 Cifukwa cakuti timakhulupilila Atate wathu wakumwamba ndi kuitanila pa dzina lake, iye amatisamalila ndi kutiteteza. Mogwilizana ndi zimene wamasalimo analemba, Yehova anati: “Popeza [wolambila woona] wasonyeza kuti amandikonda, Inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza cifukwa wadziwa dzina langa.” (Sal. 91:14) Zoonadi, Yehova Mulungu amatisamalila mwacikondi ndi kutiteteza kwa adani athu kuti asatifafanize.
5 Tiyeni tikambilane mfundo zitatu zofunika zimene zingatithandize kukulitsa cikondi cathu pa Yehova. (1) Atate wathu amatipatsa zinthu zabwino. (2) Yehova ndi mtetezi wathu, ndipo (3) Mulungu ndi bwenzi lathu lapamtima. Pamene tikambilana mfundo zimenezi, tingacite bwino kuganizila mmene zimakhudzila ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi zimene tingacite kuti tilemekeze Atate wathu. Tingacitenso bwino kuganizila madalitso amene Yehova wasungila anthu onse amene amayandikila kwa iye.—Yak. 4:8.
YEHOVA AMATIPATSA ZINTHU ZONSE ZABWINO
6. Ndi njila imodzi iti imene Yehova amasonyezela kuti ndi Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino”?
6 Wophunzila Yakobo analemba kuti: “Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo imacokela kumwamba, pakuti imatsika kucokela kwa Atate wa zounikila zonse zakuthambo.” (Yak. 1:17) Moyo wathu ndi mphatso ya mtengo wapatali yocokela kwa Yehova. (Sal. 36:9) Ngati tigwilitsila nchito moyo wathu kucita cifunilo ca Mulungu, tidzadalitsidwa panopa ndi kukhala ndi ciyembekezo ca moyo wamuyaya m’dziko latsopano. (Miy. 10:22; 2 Pet. 3:13) Koma kodi zimenezi zingatheke bwanji popeza tonsefe ndife opanda ungwilo, timacimwa ndi kufa cifukwa ca kusamvela kwa Adamu?
7. Kodi Mulungu wacita ciani kuti tikhale paubwenzi wabwino ndi iye?
7 Yehova ndi Mpatsi Wamkulu cifukwa cakuti amatipatsa zinthu zambili. Cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu, iye anatipulumutsa. Tonsefe ndife ocimwa ndipo tinatengela kupanda ungwilo kwa Adamu. (Aroma 3:23) Komabe, cifukwa cakuti Yehova amatikonda, iye anatsegula njila yotithandiza kuti tikhale naye paubwenzi wabwino. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye. Cikondi cimeneci cikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba macimo athu.”—1 Yoh. 4:9, 10.
8, 9. Kodi Yehova anakhala Mpatsi Wamkulu kwa Abulahamu ndi Isaki m’njila yotani? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
8 Zimene zinacitikila Abrahamu ca m’ma 1893 B.C.E, zinasonyeza mmene Yehova adzapelekela moyo wosatha kwa anthu omvela. Lemba la Aheberi 11:17-19 limafotokoza kuti: “Mwa cikhulupililo, pamene Abulahamu anayesedwa, zinali ngati wapeleka kale Isaki nsembe. Conco munthu ameneyu, amene analandila malonjezo mokondwela, anali wokonzeka kupeleka nsembe mwana wake wobadwa yekha. Anali wokonzeka kucita zimenezo ngakhale kuti anali atauzidwa kuti: ‘Amene adzachedwa “mbeu yako” adzacokela mwa Isaki.’ Koma anadziŵa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa. Ndipo iye anamulandiladi kucokela kwa akufa m’njila ya fanizo.” Monga mmene Abrahamu anali wofunitsitsa kupeleka mwana wake Isaki monga nsembe, nayenso Yehova mofunitsitsa anapeleka Mwana wake, Yesu Kristu monga nsembe kuti apulumutse anthu.—Welengani Yohane 3:16, 36.
9 Tangoganizilani cisangalalo cimene Isaki anali naco pamene anadziŵa kuti saphedwa. Mosakaikila, Isaki anayamikila Yehova cifukwa copeleka mwana wankhosa kuti apelekedwe nsembe m’malo mwa iye. (Gen. 22:10-13) Malo amene anapelekela nsembeyo anachedwa “Yehova-yire.” Dzina limeneli limathanthauza kuti “Yehova Adzapeleka Zinthu Zofunikila.”—Gen. 22:14; mau a munsi.
ZIMENE YEHOVA WACITA KUTI TIYANJANENSO NAYE
10, 11. Kodi ndani akutsogolela pa “utumiki wokhazikitsanso mtendele”? Nanga akucita bwanji utumiki umenewu?
10 Pamene tisinkha-sinkha pa zinthu zimene Yehova amatipatsa, timaona kuti Yesu akanapanda kupeleka moyo wake monga nsembe, sitikanakhala paubwenzi ndi Yehova. Paulo analemba kuti: “Tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafela anthu onse, cifukwatu onsewo anali atafa kale. Iye anafelanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafela n’kuukitsidwa.”—2 Akor. 5:14, 15.
11 Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kukonda kwambili Yehova ndi kuyamikila kwambili mwai waukulu umene anali nao wom’tumikila. Pa cifukwa cimeneci io anali osangalala kucita “utumiki wokhazikitsanso mtendele.” Nchito yao yolalikila ndi kupanga ophunzila inatsegula mwai wakuti anthu a mitima yabwino akhalenso pamtendele ndi Yehova, akhale naye paubwezi ndi kuti mtsogolo akakhale ana ake auzimu. Masiku ano, Akristu odzozedwa amacitanso utumiki umenewu. Zimene io amacita monga akazembe a Mulungu ndi Kristu zimapangitsa kuti anthu oona mtima akhale paubwenzi ndi Yehova ndi olambila anzao.—Ŵelengani 2 Akorinto 5:18-20; Yoh. 6:44; Mac. 13:48.
12, 13. Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso zonse zimene Yehova amatipatsa?
12 Akristu onse amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi amathandiza odzozedwa kugwila nchito yolalikila za Ufumu. Amacita zimenezi cifukwa coyamikila Yehova monga Mpatsi Wamkulu. Pocita nchito imeneyi, timagwilitsila nchito Baibulo limene ndi mphatso yocokela kwa Yehova. (2 Tim. 3:16, 17) Pamene tigwilitsila nchito mwaluso Mau a Mulungu ouzilidwa muutumiki, timapatsa ena mwai wodzalandila moyo wosatha. Koma kuti tikwanitse kucita nchito imeneyi, tonsefe timadalila mzimu woyela wa Yehova umene ndi mphatso inanso imene iye watipatsa. (Zek. 4:6; Luka 11:13) Nchito imeneyi yakhala ndi zotsatilapo zabwino monga mmene Buku Lapacaka la Mboni za Yehova limasonyezela. Ndi mwai wamtengo wapatali kugwila nao nchito yotamanda Atate wathu amene ndi Mpatsi Wamkulu.
13 Tikamanganizila zinthu zonse zimene Mulungu watipatsa, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikucita zonse zimene ndingathe muutumiki kuti ndionetse kuti ndimayamikila Yehova ndi mtima wonse pa zinthu zonse zimene iye wandipatsa? Kodi ndi zinthu ziti zimene ndiyenela kucita kuti ndikhale mlaliki wogwila mtima wa uthenga wabwino?’ Tingaonetse kuti timayamikila Mulungu pa zinthu zabwino zimene watipatsa mwa kuika zinthu za Ufumu patsogolo paumoyo wathu. Tikamatelo, Yehova adzasamalila zosoŵa zathu. (Mat. 6:25-33) Popeza kuti Mulungu amatikonda ndi kutisamalila, tiyenela kucita zonse zimene tingathe kuti tikondweletse mtima wake.—Miy. 27:11.
14. Kodi Yehova amapulumutsa bwanji anthu ake?
14 Wamasalimo Davide anaimba kuti: “Ine ndasautsika ndipo ndasauka. Yehova amandiwelengela. Inu ndinu thandizo langa ndi wopeleka cipulumutso kwa ine.” (Sal. 40:17) Nthawi zambili, Yehova monga Mpulumutsi, amapulumutsa anthu ake monga gulu maka-maka pamene akuzunzidwa mwakhanza ndi adani ao. Timayamikila kwambili thandizo limene Yehova amatipatsa panthawi zovutazo ndi cakudya ca kuuzimu cimene amatipatsa nthawi zonse.
YEHOVA AMATETEZA ANTHU AKE
15. Fotokozani citsanzo ca mmene tate wacikondi anatetezela mwana wake.
15 Tate wabwino amasamalila ndi kuteteza ana ake. Mwacibadwa, iye amayesetsa kupulumutsa anao akakhala pa ngozi. M’bale wina amakumbukila zimene zinacitika pamene anali mnyamata. Tsiku lina pamene iye ndi atate wake anali kucokela mu ulaliki wakumunda, anapitila njila yodutsa pa mtsinje wina wake. Cifukwa cakuti m’mawa tsiku limenelo kunagwa cimvula cacikulu, madzi a mtsinjewo anasefukila. Njila yokha imene io akanawolokela mtsinjewo ndi mwa kuponda pa miyala ikulu-ikulu imene inali pamtsinjewo. Mnyamatayo anali patsogolo ndipo anateleleka ndi kugwela pamadzi osefukilawo kaŵili konse. Iye anasangalala kwambili pamene atate wake anamugwila paphewa mwaphamvu ndi kumuthandiza kuti asamile. Nayenso Atate wathu wakumwamba amatithandiza tikakumana ndi mavuto m’dziko loipali. Iye amatitetezanso kwa Satana amene ndi wolamulila wa dzikoli. Yehova ndi mtetezi wabwino kwambili kuposa wina aliyense.—Mat. 6:13; 1 Yoh. 5:19.
16, 17. Kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli ndi kuwateteza pamene anali kumenyana ndi Aameleki?
16 Mwacikondi Yehova anateteza anthu ake m’caka ca 1513 B.C.E. Iye anapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo ndipo anawateteza pamene anali kuwoloka pa nyanja yofiila. Pambuyo podutsa m’cipululu, Aisiraeli anafika ku Refidimu kumene kunali kufupi ndi Phili la Sinai.
17 Mogwilizana ndi ulosi umene Mulungu ananena wa pa Genesis 3:15, Satana mosakaikila anali kufuna-funa mpata woukila Aisiraeli amene anali kuoneka kuti alibe thandizo. Iye anagwilitsila nchito Aamaleki kuti akwanilitse colinga cake cimeneci cifukwa cakuti io anali adani a anthu a Mulungu. (Num. 24:20) Kodi Yehova anateteza bwanji anthu ake kwa adani amenewa kudzela mwa Yoswa, Mose, Aroni ndi Hura? Pamene Yoswa anali kumenyana ndi Aameleki, Mose, Aroni ndi Hura anaima pa phili limene linali capafupi. Mose akangokweza manja ake m’mwamba, Aisraeli anali kupambana nkhondoyo. Manja a Mose akatopa, Aroni ndi Hura anali kuwacilikiza. Conco mwathandizo la Yehova ndi citetetezo cake, “Yoswa anagonjetsa Aamaleki ndi anthu amene anali kumbali yao.” (Eks. 17:8-13) Mose anamanga guwa lansembe pamalo amenewo ndipo anawacha kuti “Yehova-nisi.” Dzina limeneli limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Mlongoti Womwe Ndi Cizindikilo Canga.”—Ŵelengani Ekisodo 17:14, 15; mau a munsi.
MULUNGU AMATITETEZA KU MISAMPHA YA SATANA
18, 19. Kodi Yehova amateteza bwanji atumiki ake masiku ano?
18 Yehova amateteza anthu onse amene amam’konda ndi kumumvela. Monga mmene zinalili ndi Aisiraeli ku Refidimu, timadalila Mulungu kuti atiteteze tikayanganizana ndi adani. Yehova nthawi zonse amatiteteza monga gulu kuti mdyelekezi asativulaze. Mulungu nthawi zambili wakhala akuteteza abale athu amene akhala okhulupilika mwa kusatenga mbali m’zandale. Mwacitsanzo, Mulungu anateteza abale athu panthawi ya ulamulilo wa Nazi ku Germany ndi m’maiko ena m’zaka za m’ma 1930 mpaka kumayambililo kwa 1940. Tikamawelenga ndi kusinkha-sinkha zimene zinacitikila abale athu ndiponso nkhani za m’Buku Lapacaka, timalimbikitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova amene ndi pothawilapo pathu. Nkhani zimenezi zimaonetsa mmene Mulungu anatetezela anthu ake panthawi imene anali kuzunzidwa.—Sal. 91:2.
19 Kuti tikhale otetezeka, timapatsidwa zikumbutso kudzela m’gulu la Yehova ndi m’zofalitsa zathu. Onani mmene tapindulila ndi zikumbutso zimenezi m’zaka za posacedwapa. Masiku ano, anthu amakonda kwambili ciwelewele, kumwa mwaucidakwa ndi zinthu zamalisece. Komabe, Yehova amatipatsa zikumbutso za panthawi yake ndi thandizo loyenelela kuti titetezedwe ku zinthu zimene zingaononge ubwenzi wathu ndi iye. Mwacitsanzo, timalandila malangizo acikondi oticenjeza kuti tisamagwilizane ndi anthu oipa pa Intaneti.a—1 Akor. 15:33.
20. Kodi mumpingo wacikristu timapezamo citetezo ndi citsogozo cotani?
20 Kodi tingaonetse bwanji kuti ndifedi “ophunzitsidwa ndi Yehova”? Tingaonetse zimenezi mwa kutsatila malamulo ake. (Yes. 54:13) Mpingo ndi malo abwino amene timapezamo citetezo ndi citsogozo cifukwa ndi kumene akulu amapeleka thandizo ndi uphungu wa m’Malemba. (Agal. 6:1) Yehova amatisamalila mwacikondi kudzela mwa “mphatso za amuna.” (Aef. 4:7, 8) Kodi tiyenela kutani ndi malangizo amene amatipatsa? Ngati timagonjela ndi kumvela ndi mtima wonse malangizo amene akulu amatipatsa, Mulungu adzatidalitsa.—Aheb. 13:17.
21. (a) Kodi tiyenela kukhala otsimikiza mtima kucita ciani? Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambitsilana ciani?
21 Motelo, tiyeni tizidalila thandizo la mzimu woyela ndi citsogozo ca Atate wathu wakumwamba. Tiyenelanso kusinkha-sinkha za citsanzo cabwino ca Mwana wake, Yesu Kristu, ndi kuyesetsa kumutsanzila. Yesu anadalitsidwa kwambili cifukwa cakuti anakhala womvela mpaka imfa. (Afil. 2:5-11) Ifenso tikhoza kudalitsidwa ngati timakhulupilila Yehova ndi mtima wonse. (Miy. 3:5, 6) Conco, tiyeni nthawi zonse tizidalila Yehova amene amatipatsa zinthu zabwino ndi kutiteteza kuposa wina aliyense. Kutumikila Yehova ndi mwai wamtengo wapatali ndipo timasangala kumutumikila. Kodi Yehova ndi bwenzi lathu lapamtima m’njila yotani? Cikondi cathu pa iye cidzalimba kwambili pamene tidzakambitsilana yankho la funso limeneli m’nkhani yotsatila.
a Macenjezo ena othandiza mukhoza kuwapeza m’nkhani za m’magazini otsatilawa: Nsanja ya Olonda ya August 15, 2011, tsamba 3 mpaka 5 pa nkhani yakuti “Tiyenela Kugwilitsa Nchito Intaneti Mwanzelu.” Ndiponso mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2012, tsamba 20 mpaka 29 pa nkhani yakuti “Samalani ndi Misampha ya Mdyelekezi” ndi yakuti “Musasunthike Popewa Misampha ya Satana.”