NYIMBO 19
Mgonelo wa Ambuye
Yopulinta
1. Atate ise tasonkhana
Pa tsiku lopatulika.
Imwe munasankha kuti muonetse
Cikondi canu kwa anthu.
Mwana wa nkhosa anadyewa,
Kumasula anthu anu.
Yesu modzipeleka anatifela,
Kukwanilitsa ulosiwo.
2. Yesu anapeleka moyo
Kuti atipulumutse.
Tikaona vinyo na mkate tidziŵa,
Ukulu wa mphatso iyi.
Timakumbukila tsikuli
Na mtima woyamikila.
Cifukwa tidziŵa kuti mphatso iyi
Inatimasula ku imfa.
3. Tasonkhana pamaso panu,
Kuti’se tiyamikile,
Cikondi cimene munationetsa
Potumiza mwana wanu.
Tidziŵa kuti tsiku iyi
Imakulemekezani.
Tikapitiliza kutsatila Yesu,
Tidzapeza moyo wosatha.
(Onaninso Luka 22:14-20; 1 Akor. 11:23-26.)