NYIMBO 53
Kukonzeka Kukalalikila
Yopulinta
(Yeremiya 1:17)
1. N’kuseni,
Tikonzeke
Kupita mu‘tumiki.
Mvula ikugwa,
Ndipo kwazizila.
Tingafune kupitiliza
kugona.
(KOLASI)
Pemphelo na kukonzekela,
Izi tikacita;
Tidzalalikila uthenga,
Mosaleka.
Angelo amatithandiza.
Yesu aŵatuma.
Na bwenzi lokhulupilika,
Sitifo’ka.
2. Cimwemwe
Tidzapeza
Ngati tipitiliza.
Ndipo tidziŵa
Kuti M’lungu wathu,
Amaona zonse zimene
ticita.
(KOLASI)
Pemphelo na kukonzekela,
Izi tikacita;
Tidzalalikila uthenga,
Mosaleka.
Angelo amatithandiza.
Yesu aŵatuma.
Na bwenzi lokhulupilika,
Sitifo’ka.
(Onaninso Mlal. 11:4; Mat. 10:5, 7; Luka 10:1; Tito 2:14.)