NYIMBO 67
“Lalikila Mau”
Yopulinta
(2 Timoteyo 4:2)
1. Mulungu watilamula
Kuti tilalikile uthenga.
Tilengeze kwa anthu onse,
Adziŵe ciyembekezo cathu.
(KOLASI)
Lalikila,
Kuti onse amvele!
Lalika,
Mapeto ayandika.
Lalika,
Ofatsa adzamvela.
Lalika,
Konse konse!
2. Anthu ena angaseke,
Olo angafune kutitsutsa.
Yehova adzatithandiza,
Kuti tilalikile kwa onse.
(KOLASI)
Lalikila,
Kuti onse amvele!
Lalika,
Mapeto ayandika.
Lalika,
Ofatsa adzamvela.
Lalika,
Konse konse!
3. Nthawi zina tidzapeza
Ofuna kumvetsela uthenga.
Iwo adzapulumukadi
Tikaŵaphunzitsa coonadi.
(KOLASI)
Lalikila,
Kuti onse amvele!
Lalika,
Mapeto ayandika.
Lalika,
Ofatsa adzamvela.
Lalika,
Konse konse!
(Onaninso Mat. 10:7; 24:14; Mac. 10:42; 1 Pet. 3:15.)