NYIMBO 117
Ubwino
Yopulinta
	(2 Mbiri 6:41)
- 1. O Yehova M’lungu wathu, - Ise mwatidalitsa. - Ndinu wokhulupilika - Wabwino m’zinthu zonse. - Mwationetsa cifundo - Cifukwa mutikonda. - Tidzakutumikilani - Nakukulambilani. 
- 2. Tiona ubwino wanu - Mwa anthu munasankha. - Amalengeza uthenga - Na kucita zabwino. - Mwa akulu a mumpingo, - Tipita patsogolo. - Tipatseni mzimu wanu - Tionetse ubwino. 
- 3. Kwa abale athu onse, - Tionetse ubwino. - Tipempha mutithandize - Kukonda athu onse. - Ku mipingo na mabanja, - Ndi kwa anansi athu, - Tipempha thandizo lanu, - Tionetse ubwino. 
(Onaninso Sal. 103:10; Maliko 10:18; Agal. 5:22; Aef. 5:9.)