NYIMBO 119
Tikhale na Cikhulupililo
Yopulinta
(Aheberi 10:38, 39)
1. Mwa aneneli Mulungu kale
Anakamba na ‘nthu onse.
Mwa mwana wake lelo akuti,
‘Anthu onse alape.’
(KOLASI)
Kuti tikapulumuke
Na kukhala kwamuyaya,
Tifunika kuyesetsa
Kulimbitsa cikhulupililo.
2. Ise mokondwa timvela Yesu
Mwa kulengeza Ufumu.
Tilalikile molimba mtima
Uthenga wabwinowu.
(KOLASI)
Kuti tikapulumuke
Na kukhala kwamuyaya,
Tifunika kuyesetsa
Kulimbitsa cikhulupililo.
3. Ise sitidzabwelela m’mbuyo.
Tidzakhalabe olimba.
Timadalila Mulungu wathu;
Adzatipulumutsa.
(KOLASI)
Kuti tikapulumuke
Na kukhala kwamuyaya,
Tifunika kuyesetsa
Kulimbitsa cikhulupililo.
(Onaninso Aroma 10:10; Aef. 3:12; Aheb. 11:6; 1 Yoh. 5:4.)