NYIMBO 122
Cilimikani, Musasunthike!
Yopulinta
1. Anthu avutika maganizo.
Aopa zinthu zakutsogolo.
Ise tisaleke, tisafo’ke,
Titumikile M’lungu.
(KOLASI)
Ticilimike tonse;
Tisakonde za m’dziko.
Tikacilimika,
Tidzapeza moyo.
2. Tikakumana na mayeselo,
Tidziŵa kuti tidzapambana.
Ngati tikonda zinthu zabwino,
Tidzakhala olimba.
(KOLASI)
Ticilimike tonse;
Tisakonde za m’dziko.
Tikacilimika,
Tidzapeza moyo.
3. Tilambile Yehova Mulungu.
Tim’tumikile modzipeleka.
Tilalikile onse mwakhama.
Mapeto adzafika.
(KOLASI)
Ticilimike tonse;
Tisakonde za m’dziko.
Tikacilimika,
Tidzapeza moyo.
(Onaninso Luka 21:9; 1 Pet. 4:7.)