NYIMBO 131
“Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”
Yopulinta
1. Anthu na Mulungu,
Acita umboni,
Za cikwati ca lelo,
Comangidwa bwino.
(KOLASI 1)
Mwamuna walonjeza
Kukonda mkaziyu.
“Ngati M’lungu wamanga,
Musalekanitse.”
2. Onse aphunzila,
Mau a Yehova.
Lomba ayembekeza,
Dalitso la M’lungu.
(KOLASI 2)
Mkazinso walonjeza
Kukonda mwamuna.
“Ngati M’lungu wamanga,
Musalekanitse.”
(Onaninso Gen. 2:24; Mlal. 4:12; Aef. 5:22-33.)