NYIMBO 145
Mulungu Analonjeza Paradaiso
Yopulinta
1. M’lungu wathu analonjeza
Tidzakhala m’paradaiso.
Adzacotsa ucimo wonse,
Na mavuto adzasila.
(KOLASI)
Tidzakhala m’paradaiso,
M’lungu wathu walonjeza.
Khristu Mfumu
Adzacita cifunilo ca Yehova.
2. Posacedwa ’pa Khristu Yesu
Adzaukitsa akufa.
Ndipo dziko lonse lapansi,
Lidzakhala Paradaiso.
(KOLASI)
Tidzakhala m’paradaiso,
M’lungu wathu walonjeza.
Khristu Mfumu
Adzacita cifunilo ca Yehova.
3. Titamande Mulungu wathu,
Cifukwa ca paradaiso.
Mwacimwemwe timuimbile,
Capamodzi tim’lambile.
(KOLASI)
Tidzakhala m’paradaiso,
M’lungu wathu walonjeza.
Khristu Mfumu
Adzacita cifunilo ca Yehova.
(Onaninso Mat. 5:5; 6:10; Yoh. 5:28, 29.)