PHUNZILO 16
Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula
Yobu 16:5
ZOFUNIKILA: Muzikamba zinthu zothandiza komanso zolimbikitsa.
MOCITILA:
Khalani na cidalilo mwa omvela anu. Dalilani kuti iwo ali na mtima wofuna kukondweletsa Yehova. Ngakhale pofuna kupeleka uphungu, coyamba pezani cowayamikila moona mtima.
Cepetsani kukamba pa zinthu zoipa. Chulani zoipa m’nkhani yanu mongofuna kumveketsa mfundo inayake. Koma mzimu wonse wa nkhani yanu uzikhala pa zinthu zabwino.
Seŵenzetsani kwambili Mawu a Mulungu. Unikani zimene Yehova anacita, zimene akucita, na zimene adzacitila anthu. Apatseni ciyembekezo omvela anu na kuwalimbikitsa.